bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 12
1 Chronicles 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 13 →
1
Naŵa anthu amene adadza kwa Davide ku Zikilagi, kumene Davideyo adaathaŵira chifukwa choopa Saulo mwana wa Kisi. Anthu ameneŵa ankathandiza Davide kumenya nkhondo, pamodzi ndi anzao amphamvu.
2
Iwoŵa anali anthu odziŵa kugwiritsa ntchito uta. Mivi ndi miyala ankatha kuponyera dzanja lamanja kapena lamanzere. Iwoŵa anali Abenjamini, abale ake a Saulo.
3
Mtsogoleri wao anali Ahiyezere, wotsatana naye anali Yowasi. Aŵiri onsewo anali ana a Semaa wa ku Gibea. Panalinso Yeziyele ndi Peleti, ana a Azimaveti, Beraka, Yahu wa ku Anatoti,
4
ndi Isimaya wa ku Gibiyoni, amene anali wamphamvu mwa anthu makumi atatu aja ndiponso mmodzi mwa atsogoleri ao. Panalinso Yeremiya, Yahaziele, Yohanani, Yozabadi wa ku Gedera,
5
Eluzai, Yeremoti, Bealiya, Semariya, Sefatiya wa ku Harufi,
6
Elikana, Isiya, Azarele, Yowezere, ndiponso Yasobeamu. Onsewo anali Akora.
7
Panalinso Yowela ndi Zebadiya, ana a Yerohamu wa ku Gedori.
8
Asilikali ena amphamvu, ochokera ku dziko la Gadi, adafika kwa Davide ku linga lake lam'chipululu. Iwoŵa anali ngwazi zodziŵa kumenya nkhondo, makamaka pogwiritsa ntchito chishango ndi mkondo, ndipo anali oopsa ngati mikango. Akamathamanga, ngati ngoma zam'mapiri liŵiro lake.
9
Ezere anali mtsogoleri, wachiŵiri anali Obadiya, wachitatu Eliyabu,
10
wachinai Misimana, wachisanu Yeremiya,
11
wachisanu ndi chimodzi Atai, wachisanu ndi chiŵiri Eliyele,
12
wachisanu ndi chitatu Yohanani, wachisanu ndi chinai Elizabadi,
13
wa 10 Yeremiya, wa 11 Makibanai.
14
Agadi ameneŵa ndiwo amene anali m'gulu la atsogoleri ankhondo. Ang'onoang'ono ankalamulira anthu 100, pamene akuluakulu ankalamulira anthu 1,000.
15
Ameneŵa ndiwo anthu amene adaoloka Yordani mwezi woyamba, nthaŵi imene mtsinjewo unali wodzaza nkumasefukira pa zibumi zake zonse. Motero adapirikitsa anthu onse amene anali m'zigwa. Ena kuthaŵira kuvuma ena kuzambwe.
16
Tsiku lina anthu ena a ku Benjamini ndi a ku Yuda adadza ku linga la Davide.
17
Davide adatuluka kukakumana nawo, ndipo adaŵauza kuti, “Ngati mwadza kwa ine kuno mwaubwenzi kuti mudzandithandize, ndiye kuti mtima wanga udzagwirizana nanu. Koma ngati nkundipereka kwa adani anga, ngakhale sindidalakwe, pamenepo Mulungu wa makolo athu apenye ndipo akulangeni.”
18
Pomwepo Mzimu wa Mulungu udamtsikira Amasai, mtsogoleri wa anthu makumi atatu aja, ndipo adati, “Inu Davide, ifetu ndife anu. Tili limodzi nanu, inu mwana wa Yese. Inu ndi anthu amene amakuthandizani, mudzakhala opambana. Zoonadi Mulungu wanu ali nanu.” Tsono Davide adaŵalandira ndipo adaŵasandutsa atsogoleri a magulu ake ankhondo.
19
Anthu ena a fuko la Manase adabwera kwa Davide nthaŵi imene Davide adadza ndi Afilisti kudzamenyana nkhondo ndi Saulo. Komabe nthaŵiyo Davide sadaŵathandize Afilisti, poti akazembe ao adambweza namanena kuti, “Uyu akhoza kubwerera kwa mbuye wake Saulo, ndiye ife tidzaonongeka pamenepo.”
20
Motero pamene Davide ankabwerera ku Zikilagi, anthu a fuko la Manase aja adapita naye limodzi. Amanasewo anali aŵa: Adina, Yozabadi, Yediyaele, Mikaele, Yozabadi, Elihu ndi Ziletai, atsogoleri a magulu a ankhondo zikwi zambiri a ku Manase.
21
Iwoŵa adathandiza Davide kulimbana ndi magulu a achifwamba, pakuti onseŵa anali anthu amphamvu, olimba mtima, ndipo anali atsogoleri pa nkhondo.
22
Anthu ankabwera kwa Davide tsiku ndi tsiku kudzamthandiza, mpaka gulu lake lankhondo lidakula kwambiri, ngati gulu lankhondo la Mulungu.
23
Nachi chiwerengero cha magulu a anthu ankhondo amene adadza ku Hebroni kwa Davide, kudzamlonga ufumu m'malo mwa Saulo, potsata mau a Chauta.
24
Ankhondo a ku Yuda ogwira zishango ndi mikondo analipo 6,800.
25
A fuko la Simeoni, anthu amphamvu olimba mtima pomenya nkhondo, 7,100.
26
A fuko la Levi, 4,600.
27
Mtsogoleri Yehoyada wa banja la Aroni adabwera ndi anthu 3,700.
28
Zadoki mnyamata wolimba mtima adabwera ndi achibale ake 22.
29
A fuko la Benjamini, abale ake a Saulo, analipo 3,000. Koma mpaka pa nthaŵi imeneyo, ambiri mwa iwowo ankaumirirabe kumatsata banja la Saulo.
30
A banja la Efuremu, 20,800 anthu amphamvu ndi olimba mtima, anthu omveka ku mabanja a makolo ao.
31
A fuko lahafu la Manase analipo 18,000, amene adaachita kuŵaitana kuti adzalonge nao ufumu Davide.
32
A fuko la Isakara analipo atsogoleri 200 pamodzi ndi anthu ao. Atsogoleriwo ankamvetsa zinthu pa nthaŵi imeneyo, namadziŵa zimene Israele ankayenera kuchita pa nthaŵi yake.
33
A fuko la Zebuloni analipo 50,000 asilikali okonzekera nkhondo, okhala ndi zida zankhondo zamitundumitundu, othandiza Davide ndi mtima umodzi.
34
A fuko la Nafutali, atsogoleri 1,000 amene anali ndi asilikali 37,000 a zishango ndi mikondo.
35
A fuko la Dani, anthu 28,600 okonzekera kumenya nkhondo.
36
A fuko la Asere anali 40,000, ankhondo enieni, okonzekera kumenya nkhondo.
37
A fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi fuko lahafu la Manase, kuchokera pa tsidya ilo la mtsinje wa Yordani, analipo 120,000 odziŵa kumenya nkhondo ndi zida zosiyanasiyana.
38
Ankhondo onseŵa amene ankadziŵa kamenyedwe ka nkhondo, adadza ku Hebroni ndi mtima umodzi, kuti akamlonge ufumu Davide. Aisraele onse nawonso anali ndi mtima womwewo wofuna kumlonga ufumu Davide.
39
Ndipo adakhala komweko masiku atatu pamodzi ndi Davide namadya zimene abale ao anali ataŵakonzekera.
40
Nawonso anansi ao, ochokera ngakhale ku Isakara ndi Zebuloni ndi Nafutali, adadza atasenzetsa chakudya abulu ao, ngamira zao, nyulu zao ndi ng'ombe zao. Adazisenzetsa chakudya chambiri, makeke ankhuyu, ntchichi zamphesa, vinyo ndiponso mafuta. Adabweranso ndi ng'ombe ndi nkhosa zambiri, poti ku dziko la Israele kunali chisangalalo.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29