bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 24
1 Chronicles 24
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 25 →
1
Zidzukulu za Aroni ndi izi. Ana a Aroni naŵa: Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.
2
Koma Nadabu ndi Abihu adafa bambo wao akali moyo, ndipo analibe ana. Motero Eleazara ndi Itamara adaloŵa unsembe.
3
Zidzukulu za Aroni mfumu Davide adazigaŵira ntchito molongosoka bwino, pothandizidwa ndi Zadoki, mmodzi mwa zidzukulu za Eleazara, ndiponso Ahimeleki, mmodzi mwa zidzukulu za Itamara.
4
Popeza kuti pakati pa zidzukulu za Eleazara padapezeka atsogoleri ambiri kupambana pakati pa zidzukulu za Itamara, Davide adasankhula atsogoleri 16 pakati pa zidzukulu za Eleazara, ndiponso asanu ndi atatu pakati pa zidzukulu za Itamara.
5
Adaŵasankhula pochita maere mosakondera, poti panali atumiki a ku Nyumba ya Chauta ndi atsogoleri achipembedzo pakati pa zidzukulu za Eleazara ndiponso pakati pa zidzukulu za Itamara.
6
Magulu aŵiri a zidzukuluzi adachita maerewo motsatana, ndipo mlembi Semaya, mwana wa Netanele, amene anali Mlevi, adalemba maina ao. Mboni zake zinali izi: mfumu, nduna, wansembe Zadoki, Abimeleki mwana wa Abiyatara, ndiponso atsogoleri a mabanja a ansembe ndi a Alevi.
7
Maere oyamba adagwera Yehoyaribu, achiŵiri adagwera Yedaya,
8
achitatu adagwera Harimu, achinai adagwera Seorimu,
9
achisanu adagwera Malikiya, achisanu ndi chimodzi adagwera Miyamini,
10
achisanu ndi chiŵiri adagwera Hakozi, achisanu ndi chitatu adagwera Abiya,
11
achisanu ndi chinai adagwera Yesuwa, achikhumi adagwera Sekaniya,
12
a 11 adagwera Eliyasibu, a 12 adagwera Yakimu,
13
a 13 adagwera Hupa, a 14 adagwera Yesebeabu,
14
a 15 adagwera Biliga, a 16 adagwera Imeri,
15
a 17 adagwera Heziri, a 18 adagwera Hapizeze,
16
a 19 adagwera Petahiya, a 20 adagwera Yehezikele,
17
a 21 adagwera Yakini, a 22 adagwera Gamuli,
18
a 23 adagwera Delaya, a 24 adagwera Maaziya.
19
Ntchito yao ya anthu ameneŵa inali yotumikira m'Nyumba ya Mulungu potsata mwambo umene adaukhazikitsa Aroni kholo lao, monga momwe Chauta Mulungu wa Aisraele adaamlamulira.
20
Atsogoleri ena a mabanja a Levi naŵa: Yedeiya, mdzukulu wa Subaele, amene anali mdzukulu wa Amuramu.
21
Isiya, mdzukulu wa Rehabiya,
22
Yahati, mdzukulu wa Selomoti, amene anali mdzukulu wa Izihara.
23
Ana a Hebroni naŵa: Yeriya mtsogoleri, wachiŵiri Amariya, wachitatu Yahaziele, wachinai Yekameani.
24
Samiri anali mdzukulu wa Mika, kholo lao linali Uziyele.
25
Mbale wake wa Mika anali Isiya. Zekariya anali mdzukulu wa Uziyele, kholo lao linali Isiya.
26
Zidzukulu za Merari nazi: Mali, Musi ndi Yaziya.
27
Adzukulu a Merari, kuchokera mwa Yaziya mwana wake, naŵa: Sohamu, Zakuri ndi Ibiri.
28
Ana a Mali anali aŵa: Eleazara, amene analibe ana, ndiponso Kisi,
29
amene mwana wake anali Yerameele.
30
Ana a Musi anali Mali, Edere ndi Yerimoti. Ameneŵa ndiwo amene anali zidzukulu za Levi potsata mabanja a makolo ao.
31
Mabanja ameneŵanso kuti adziŵe ntchito zao, adachita maere monga abale ao, zidzukulu za Aaroni, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe. Ochita umboni anali mfumu Davide, Zadoki, Ahimeleki, ndiponso atsogoleri a mabanja a ansembe ndi a Alevi.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29