bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 1
Luke 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 2 →
1
Ateofilo olemekezeka, Anthu ambiri adayesa kulongosola mbiri ya zinthu zimene zidachitika pakati pathu.
2
Iwo adalemba zimene adaatisimbira anthu oziwona chamaso kuyambira pachiyambi pake, nakhala akuzilalika.
3
Tsono popeza kuti inenso ndalondola mosamala kwambiri m'mene zonsezo zidachitikira kuyambira pa chiyambi, ndaganiza kuti nkwabwino kuti ndikulembereni zimenezo mwatsatanetsatane.
4
Ndatero kuti mudziŵe ndithu kuti zimene adakuphunzitsanizo nzoonadi.
5
Pa nthaŵi imene Herode anali mfumu ya dziko la Yudeya, kunali wansembe wina, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya. Mkazi wake Elizabeti anali wa fuko la Aroni.
6
Aŵiri onsewo anali olungama pamaso pa Mulungu, ndipo ankatsata mokhulupirika malamulo ndi malangizo onse a Ambuye.
7
Adaalibe mwana, chifukwa Elizabeti anali wosabala, ndipo aŵiri onsewo anali okalamba.
8
Tsiku lina Zakariya ankagwira ntchito yake yaunsembe pamaso pa Mulungu. Inali nthaŵi ya gulu lake la ansembe kutumikira.
9
Potsata dongosolo lao la ansembe, iye adaasankhidwa mwamaere kuti akaloŵe m'Nyumba ya Mulungu kukafukiza lubani.
10
Khamu lonse la anthu linkapemphera kunja pa nthaŵi yofukiza lubaniyo.
11
Tsono mngelo wa Ambuye adaonekera Zakariya. Mngeloyo adaaimirira ku dzanja lamanja la guwa lofukizirapo lubani.
12
Zakariya adadzidzimuka pomuwona, nachita mantha.
13
Koma mngeloyo adamuuza kuti, “Usaope, Zakariya, Mulungu wamva pemphero lako. Mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.
14
“Udzakondwa ndi kusangalala, anthu ambirinso adzakondwa chifukwa cha kubadwa kwake,
15
popeza kuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye. Sazidzamwa konse vinyo kapena choledzeretsa china chilichonse. Adzakhala wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ngakhale asanabadwe nkomwe.
16
Adzatembenuza Aisraele ambiri kuti abwerere kwa Ambuye, Mulungu wao.
17
Molimba mtima ndiponso mwamphamvu monga mneneri Eliya, adzatsogolako Ambuye akubwera. Adzayanjanitsanso makolo ndi ana ao, adzatembenuza anthu osamvera kuti akhale ndi nzeru zonga za anthu olungama. Adzakonzera Ambuye anthu okonzekeratu kuŵatumikira.”
18
Zakariya adafunsa mngeloyo kuti, “Kodi ndingadziŵe bwanji kuti zimenezi nzoona? Ineyo ndine nkhalamba, mkazi wanga nayenso wakalamba.”
19
Mngeloyo adati, “Ine ndine Gabriele, amene ndimakhala kufupi ndi Mulungu. Iyeyo wachita kundituma kuti ndilankhule nawe ndi kukuuza uthenga wabwinowu.
20
Iweyo sudakhulupirire zimene ndanenazi, koma zidzachitika ndithu pa nthaŵi yake. Nchifukwa chake udzakhala duu, osatha kulankhula, kufikira tsiku lodzachitika zimenezi.”
21
Nthaŵi yonseyo anthu aja ankadikira Zakariya, nkumadabwa kuti akuchedwa m'Nyumba ya Mulungumo.
22
Pamene iye adatuluka, sadathe kulankhula nawo. Apo iwo adazindikira kuti m'Nyumbamo waona china chake m'masomphenya. Iye adalankhula nawo ndi manja okha, osathanso kunena mau.
23
Atatha masiku ake otumikira m'Nyumba ya Mulungu, adapita kwao.
24
Pambuyo pake mkazi wake Elizabeti adatenga pathupi, nabindikira miyezi isanu.
25
Adati, “Ambuye andichitira zotere: nthaŵi inoyi andiwonetsa chifundo chao, andichotsa manyazi pakati pa anthu.”
26
Elizabeti ali ndi pathupi pa miyezi isanu ndi umodzi, Mulungu adatuma mngelo Gabriele ku mudzi wina wa ku Galileya, dzina lake Nazarete.
27
Adamtuma kwa namwali wina wosadziŵa mwamuna amene anali atafunsidwa mbeta ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la mfumu Davide. Namwaliyo dzina lake anali Maria.
28
Mngelo uja adadza kwa iye nati, “Moni, inu amene Mulungu wakukomerani mtima kotheratu. Ambuye ali nanu.”
29
Maria adadzidzimuka nawo kwambiri mau ameneŵa, nayamba kusinkhasinkha kuti kodi moni umenewu ndi wa mtundu wanji?
30
Mngeloyo adamuuza kuti, “Musaope, Maria, Mulungu wakukomerani mtima.
31
Mudzatenga pathupi, ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Mudzamutcha dzina lake Yesu.
32
“Adzakhala wamkulu, ndipo adzatchedwa Mwana wa Mulungu Wopambanazonse. Ambuye Mulungu adzamlonga ufumu wa kholo lake Davide,
33
ndipo adzakhala Mfumu ya Aisraele mpaka muyaya. Ufumu wake sudzatha konse.”
34
Koma Maria adafunsa mngeloyo kuti, “Zimenezi zidzachitika bwanji, popeza kuti sindidziŵa mwamuna?”
35
Mngeloyo adayankha kuti, “Mzimu Woyera adzakutsikirani, ndipo mphamvu za Mulungu Wopambanazonse zidzakuphimbani. Nchifukwa chake Mwana wodzabadwayo adzakhala Woyera, ndipo adzatchedwa Mwana wa Mulungu.
36
“Onani, mbale wanu uja Elizabeti, nayenso akuyembekezera mwana wamwamuna mu ukalamba wake. Anthu amati ngwosabala, komabe uno ndi mwezi wake wachisanu ndi chimodzi.
37
Pajatu palibe kanthu kosatheka ndi Mulungu.”
38
Apo Maria adati, “Ndine mtumiki wa Ambuye; zindichitikire monga mwaneneramo.” Ndipo mngeloyo adamsiya.
39
Patapita masiku oŵerengeka, Maria adanyamuka napita mofulumira ku dera lamapiri, ku mudzi wina wa ku Yudeya.
40
Adakaloŵa m'nyumba ya Zakariya, malonjera Elizabeti.
41
Pamene Elizabeti adamva malonje a Maria, mwana adayamba kutakataka m'mimba mwake. Elizabeti adadzazidwa ndi Mzimu Woyera,
42
ndipo adalankhula mokweza mau kuti, “Ndinu odala kupambana akazi ena onse, ngwodalanso Mwana wanu.
43
Ine ndine yani kuti inu, mai wa Ambuye anga, mudzandiyendere?
44
Chifukwatu pamene ndinamva malonje anu, mwana anayamba kutakataka ndi chimwemwe m'mimba mwanga.
45
Ndinu odala chifukwa mudakhulupirira kuti zimene Ambuye adakuuzani, zidzachitadi.”
46
Pamenepo Maria adati, “Mtima wanga ukutamanda Ambuye,
47
ndipo mzimu wanga ukukondwera mwa Mulungu, Mpulumutsi wanga,
48
popeza kuti wayang'ana kutsika kwa mtumiki wake. Ndithu kuyambira tsopano anthu a mibadwo yonse adzanditcha wodala,
49
pakuti Iye amene ali wamphamvu wandichitira zazikulu, ndipo dzina lake nloyera.
50
Amaŵachitira chifundo anthu a mibadwo ndi mibadwo amene amamlemekeza.
51
Wachita zamphamvu ndi dzanja lake, wabalalitsa anthu a mtima wonyada.
52
Mafumu amphamvu waŵatsitsa pa mipando yao yachifumu, anthu wamba nkuŵakweza.
53
Anthu anjala waŵakhutitsa ndi zabwino, anthu olemera nkuŵabweza osaŵapatsa kanthu.
54
Wadzathandiza anthu ake Aisraele, pokumbukira chifundo chake.
55
Izi ndi zomwe adaalonjeza kuti adzaŵachitira makolo athu akale aja, Abrahamu ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.”
56
Maria atakhala ndi Elizabeti ngati miyezi itatu, adabwerera kwao.
57
Nthaŵi yakuti Elizabeti achire idakwana, ndipo adabala mwana wamwamuna.
58
Anzake ndi abale ake atamva kuti Ambuye amchitira chifundo chachikulu chotere, adakondwera naye pamodzi.
59
Pa tsiku lachisanu ndi chitatu mwanayo atabadwa, adadza naye kuti amuumbale, nafuna kumutcha dzina la bambo wake Zakariya.
60
Koma mai wake adakana, adati, “Iyai, koma atchedwe Yohane.”
61
Pamenepo anthuwo adamuuza kuti, “Koma pakati pa abale anu palibe amene ali ndi dzina limeneli.”
62
Tsono adalankhula ndi bambo wake ndi manja, namufunsa kuti, “Mukufuna kuti timutche dzina lanji?”
63
Zakariya adapempha cholemberapo, nalembapo kuti, “Dzina lake ndi Yohane.” Anthu onsewo adazizwa.
64
Pomwepo Zakariya adathanso kulankhula, nayamba kutamanda Mulungu.
65
Anzao onse aja adagwidwa ndi mantha, ndipo mbiri ya zimenezi idawanda ku dera lonse la mapiri a ku Yudeya.
66
Anthu onse amene ankazimva, ankazilingalira m'mitima mwao, ndi kumadzifunsa kuti, “Kodi mwana ameneyu adzakhala munthu wotani?” Pakuti zinkachita kuwonekeratu kuti Ambuye anali naye.
67
Tsono Zakariya, bambo wa Yohaneyo, adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau ochokera kwa Mulungu. Adati,
68
“Atamandike Ambuye, Mulungu wa Aisraele, chifukwa adadzayendera anthu ao, ndi kudzaŵaombola.
69
Adautsa wina, wa fuko la mtumiki wake Davide, kuti akhale Mpulumutsi wathu wamphamvu.
70
Izi ndi zomwe Iye adaaneneratu kalekale kudzera mwa aneneri ake oyera mtima.
71
Adaalonjeza kuti adzatipulumutsa kwa adani athu, ndi kwa onse odana nafe.
72
Choncho Iye waŵachitiradi chifundo makolo athu akale, ndipo wakumbukira chipangano chake choyera.
73
Adalonjezanso Abrahamu, kholo lathu, molumbira,
74
kuti adzatipulumutsa kwa adani athu, kuti tizimtumikira mopanda mantha,
75
kuti tikhale oyera mtima ndi olungama pamaso pake, masiku onse a moyo wathu.
76
Tsono mwana iwe, udzatchedwa mneneri wa Mulungu Wopambanazonse, chifukwa udzatsogola pamaso pa Ambuye, kuti ukonzeretu njira zao.
77
Udzadziŵitsa anthu ao kuti Mulungu adzaŵapulumutsa pakuŵakhululukira machimo ao.
78
Mulungu wathu ndi wa chifundo chachikulu, adzatitumizira kuŵala kwa dzuŵa lam'maŵa kuchokera Kumwamba.
79
Kuŵala kwake kudzaunikira onse okhala mu mdima wabii ngati wa imfa, kudzatitsogolera pa njira ya mtendere.”
80
Mwana uja Yohane ankakula nasanduka wa mkhalidwe wamphamvu. Pambuyo pake adakhala ku chipululu mpaka tsiku limene adadziwonetsa poyera pakati pa Aisraele.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24