bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 2
Luke 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 3 →
1
Masiku amenewo, Augusto, Mfumu ya ku Roma, adalamula kuti pakhale kalembera wa anthu a m'maiko ake onse.
2
Kalembera ameneyu anali woyamba, ndipo adachitika pamene Kwirinio anali bwanamkubwa wa dziko la Siriya.
3
Motero anthu onse adapita kukalembedwa, aliyense ku mudzi kwao.
4
Yosefe nayenso adanyamuka kuchokera ku Nazarete, mudzi wa ku Galileya. Adapita ku Yudeya, ku mudzi wa mfumu Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa anali wa m'banja ndi fuko la Davideyo.
5
Adapita kukalembedwa pamodzi ndi Maria, mkazi wake, amene anali ndi pathupi.
6
Pamene anali kumeneko, nthaŵi yake yoti Maria achire idakwana,
7
ndipo adabala mwana wake wachisamba wamwamuna. Adamkulunga m'nsalu namgoneka m'chodyera cha zoŵeta, chifukwa adaasoŵa malo m'nyumba ya alendo.
8
Ku dera lomwelo kunali abusa amene ankalonda zoŵeta zao ku dambo usiku.
9
Mwadzidzidzi mngelo wa Ambuye adadzaimirira pakati pao, ndipo ulemerero wa Ambuye udaŵala ponse pozungulira, mwakuti abusawo adaachita mantha kwambiri.
10
Koma mngeloyo adaŵauza kuti, “Musaope, ndadzakuuzani uthenga wabwino, umene udzakondweretsa anthu onse kwambiri.
11
Usiku womwe uno m'mudzi wa Davide wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.
12
Chitsimikizo chake ndi ichi: mukapeza mwana wakhanda, wokutidwa ndi nsalu, atagona m'chodyera cha zoŵeta.”
13
Mwadzidzidzi pamodzi ndi mngeloyo padaoneka gulu lalikulu la angelo ena. Ankatamanda Mulungu ndi mau akuti,
14
“Ulemerero kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene Iye amakondwera nawo.”
15
Angelowo atachoka kubwerera Kumwamba, abusa aja adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tipite ku Betelehemu, tikaone zachitikazi, zimene Ambuye atidziŵitsa.”
16
Tsono adapita mofulumira, nakapeza Maria ndi Yosefe, atagoneka mwana wakhandayo m'chodyera cha zoŵeta chija.
17
Pamene adamuwona, abusawo adaŵafotokozera zimene mngelo uja adaaŵauza za mwanayo.
18
Onse amene ankamva, ankadabwa ndi zimene abusawo ankaŵasimbira.
19
Koma Maria adasunga zonsezo namazilingalira mumtima mwake.
20
Pambuyo pake abusa aja adabwerera akuyamika ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha zonse zimene anali atamva ndi kuziwona. Zonse zinali monga momwe mngelo uja adaaŵauzira.
21
Patapita masiku asanu ndi atatu, mwana uja adamuumbala namutcha dzina lake Yesu. Dzinali ndi lomwe lija limene mngelo adaatchula, Maria asanatenge pathupi.
22
Kenaka idafika nthaŵi yoti Yosefe ndi Maria achite mwambo wakuyeretsedwa potsata Malamulo a Mose. Tsono mwanayo adapita naye ku Yerusalemu kuti akampereke kwa Ambuye.
23
Pajatu m'Malamulo a Ambuye muli mau akuti, “Mwana aliyense wamwamuna, woyamba kubadwa, apatulidwe kuti akhale wao wa Ambuye.”
24
Adakaperekanso nsembe potsata Malamulo a Ambuye akuti, “Apereke njiŵa ziŵiri kapena maunda aŵiri.”
25
Ku Yerusalemuko kunali munthu wina, dzina lake Simeoni. Anali munthu wolungama ndi woopa Mulungu. Ankayembekezera nthaŵi yoti Mulungu adzapulumutse Aisraele, ndipo Mzimu Woyera anali naye.
26
Mzimu Woyerayo adaamuululira kuti sadzafa asanaone Mpulumutsi amene Mulungu adaalonjeza.
27
Tsiku lina Mzimu Woyera adamlamula kuti apite ku Nyumba ya Mulungu. Makolo a Yesu adaloŵanso m'Nyumbamo ndi mwana waoyo kukamchitira mwambo potsata Malamulo a Mose.
28
Pamenepo Simeoni adalandira mwanayo m'manja mwake, nayamba kutamanda Mulungu ndi mau akuti,
29
“Ambuye, tsopano mundilole ine mtumiki wanu, ndipite ndi mtendere, pakuti mwachitadi zija mudaalonjezazi.
30
Ndi maso angaŵa ndachiwonadi chipulumutso chija,
31
chimene mudakonza kuti anthu a mitundu yonse achiwone.
32
Mwapereka kuŵala kodzaunikira anthu a mitundu ina, kodzakhala ulemerero wa anthu anu Aisraele.”
33
Atate ndi amai a mwanayo ankangodabwa nazo zimene Simeoni ankanena za mwanayo.
34
Kenaka Simeoniyo adaŵadalitsa, nauza Maria, mai wa mwanayo, kuti, “Mwanayu Mulungu wamuika kuti Aisraele ambiri adzagwe, ambirinso adzadzuke, chifukwa cha iyeyu. Adzakhala chizindikiro chochokera kwa Mulungu, chimene anthu ambiri adzatsutsana nacho,
35
kuti choncho maganizo amene ali m'mitima ya anthu ambiri adzaonekere poyera. Ndipo inunso mai, chisoni chidzabaya mtima wanu ngati lupanga.”
36
Kunalinso mneneri wina wamkazi, dzina lake Anna, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere. Anali wokalamba kwambiri. Anali atakhala pa banja zaka zisanu ndi ziŵiri zokha,
37
pambuyo pake nkukhala wamasiye kufikira msinkhu wa zaka 84. Sankachokatu ku Nyumba ya Mulungu, ankakonda kudzatumikira Mulungu usana ndi usiku pakupemphera ndi kusala zakudya.
38
Iye adafikako nthaŵi yomweyo, nayamba kuyamika Mulungu, nkumakamba za Mwanayo ndi anthu onse amene ankayembekezera nthaŵi yoti Mulungu adzapulumutse Yerusalemu.
39
Yosefe ndi Maria atachita zonse potsata Malamulo a Ambuye, adabwerera ku Galileya, kumudzi kwao ku Nazarete.
40
Mwanayo ankakula, nasanduka wamphamvu nkukhalanso wa nzeru zabasi. Ndipo Mulungu ankamudalitsa.
41
Makolo a Yesu ankapita ku Yerusalemu chaka ndi chaka ku chikondwerero cha Paska.
42
Pamene Yesu anali ndi zaka khumi ndi ziŵiri, iwo adapita kumeneko monga adaazoloŵera.
43
Masiku a chikondwererocho atatha, adanyamuka kumabwerera kwao, mnyamata uja Yesu nkutsalira ku Yerusalemu, makolo ake osadziŵa.
44
Iwo ankayesa kuti ali pamodzi ndi anzao aulendo, choncho adayenda ulendo wa tsiku limodzi. Tsono adayamba kumufunafuna pakati pa abale ao ndi abwenzi ao.
45
Ataona kuti sakumpeza, adabwerera ku Yerusalemu akumufunafuna ndithu.
46
Patapita masiku atatu, adampeza m'Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera mau ao, ndi kumaŵafunsa mafunso.
47
Onse amene ankamva mau ake, ankadabwa ndi mayankho ake anzeru.
48
Pamene makolo ake adamuwona, adadabwa, ndipo mai wake adamufunsa kuti, “Mwana iwe, watisautsiranji chotere? Ine ndi bambo wako tavutika nkukufunafuna.”
49
Koma Yesu adati, “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kani simumadziŵa kuti ndiyenera kupezeka m'nyumba ya Atate anga?”
50
Koma iwo sadamvetse zimene adaŵayankhazo.
51
Tsono Yesu adabwerera nawo pamodzi, nafika ku Nazarete, ndipo ankaŵamvera. Mai wake ankasunga zonsezi mumtima mwake.
52
Ndipo Yesu analikunka nakula m'nzeru ndi mu msinkhu, ndipo Mulungu ndi anthu omwe ankakondwera naye kwambiri.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24