bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 8
Luke 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 9 →
1
Pambuyo pake Yesu adanka nayendera mizinda ndi midzi akulalika ndi kuuza anthu Uthenga Wabwino wonena za ufumu wa Mulungu. Ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja anali naye.
2
Panalinso azimai ena amene Yesu adaaŵatulutsa mizimu yoipa ndi kuŵachiza nthenda zina. Azimaiwo ndi aŵa: Maria, wotchedwa Magadalena, (amene mwa iye mudaatuluka mizimu yoipa isanu ndi iŵiri);
3
Yohana, mkazi wa Kuza, kapitao wa Herode; Suzana, ndiponso azimai ena ambiri amene ndi ndalama zao ankathandiza Yesu ndi ophunzira ake.
4
Anthu ambirimbiri ochokera ku midzi yonse adasonkhana kumene kunali Yesu. Tsono Iye adaŵaphera fanizo. Adati,
5
“Munthu wina adaapita kukafesa mbeu. Akufesa choncho, mbeu zina zidagwera m'njira. Zidapondedwa, ndipo mbalame zidazitolatola.
6
Mbeu zina zidagwera pa nthaka yapathanthwe. Zidamera, koma nkufota, chifukwa zidaasoŵa chinyontho.
7
Mbeu zina zidagwera pa zitsamba zaminga. Zitsambazo pokula zidalanda chakudya cha mbeu zija.
8
Koma mbeu zina zidagwera pa nthaka yabwino. Zidakula nkubereka. Ngala iliyonse inali ndi njere makumi khumi.” Tsono Yesu adalankhula mokweza mau kuti, “Amene ali ndi makutu akumva, amve!”
9
Ophunzira a Yesu adamufunsa za tanthauzo la fanizoli.
10
Tsono Iye adati, “Inuyo Mulungu adakuululirani zobisika zokhudza Ufumu wake. Koma enaŵa amazimvera m'mafanizo chabe, kuti choncho ayang'ane, koma asapenye, ndipo amve, koma asamvetse.”
11
“Tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mbeu zija ndi mau a Mulungu.
12
Mbeu zogwera m'njira zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu. Koma Satana amabwera, nkuchotsa mau aja m'mitima mwao, kuwopa kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.
13
Mbeu zogwera pa nthaka yapathanthwe zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, nkuŵalandira ndi chimwemwe. Tsono popeza kuti alibe mizu yozama, amangokhulupirira kanthaŵi pang'ono chabe, mwakuti pa nthaŵi ya kuyesedwa, amabwerera m'mbuyo.
14
Mbeu zogwera pa zitsamba zaminga zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, koma pambuyo pake nkhaŵa, kukondetsa chuma, ndiponso khumbo la zokondweretsa za moyo uno zimaŵalepheretsa, ndipo zipatso zao sizikhwima.
15
Koma mbeu zogwera pa nthaka yabwino zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, naŵasunga mu mtima woona ndi wabwino, ndipo amalimbikira mpaka kubereka zipatso.”
16
“Palibe munthu amene amayatsa nyale nkuivundikira ndi mbiya, kapena kuibisa kunsi kwa bedi. Koma amaiika pa malo oonekera, kuti anthu oloŵa m'nyumba aone kuŵala kwake.
17
Pajatu chinthu chilichonse chobisika chidzaululuka, ndipo chilichonse chachinsinsi chidzadziŵika nkuwonekera poyera.
18
“Nchifukwa chake muzisamala m'mene mumamvera mau. Pajatu amene ali nako kanthu, adzamuwonjezera zina. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene akuyesa kuti ali nakoko adzamlandabe.”
19
Amai ake ndi abale ake a Yesu adabwera kunyumbako, koma chifukwa cha kuchuluka kwa anthu, adaalephera kufika pamene panali Iyepo.
20
Tsono munthu wina adauza Yesu kuti, “Amai anu ndi abale anu ali panjapa, akufuna kukuwonani.”
21
Koma Yesu adati, “Inetu amai anga ndi abale anga ndi anthu amene amamva mau a Mulungu, nkumachitadi zimene mauwo akunena.”
22
Tsiku lina Yesu adaloŵa m'chombo pamodzi ndi ophunzira ake. Adaŵauza kuti, “Tiyeni tiwoloke, tipite ku tsidya ilo la nyanja.” Ndipo adanyamukadi.
23
Pamene ankaoloka Yesu adagona tulo. Tsono padauka namondwe panyanjapo, mpaka chombo chija chidayamba kudzaza ndi madzi ndipo iwo anali pafupi kumira.
24
Pamenepo ophunzira aja adadza kwa Yesu namudzutsa, adati, “Ambuye, Ambuye, tikumiratu!” Iye adadzuka, naletsa mphepoyo ndi mafunde amphamvuwo. Zidalekadi ndipo padagwa bata.
25
Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi chikhulupiriro chanu chili kuti?” Koma iwo adaagwidwa ndi mantha nathedwa nzeru, nkumafunsana kuti, “Kodi ameneyu ndi munthu wotani? Angolamula mphepo ndi madzi omwe, izo nkumumveradi.”
26
Iwo adafika ku dziko la Ageregesa, limene lidapenyana ndi Galileya.
27
Pamene Yesu adafika pa mtunda, munthu wina wochokera ku mudzi wakomweko, adadzakumana naye. Munthuyo adaali ndi mizimu yoipa, ndipo kuyambira kale sankavalanso zovala. Sankakhala m'nyumba, koma ku manda.
28
Pamene iye adaona Yesu, adafuula nadzigwetsa ku mapazi ake, ndipo adanena mokweza mau kuti, “Kodi ndakuputani chiyani Inu Yesu, Mwana wa Mulungu Wopambanazonse? Ndakupembani, musandizunze.”
29
Adaatero chifukwa Yesu anali atalamula mzimu woipawo kuti utuluke mwa munthuyo. (Ndiye kuti kaŵirikaŵiri ukamugwira, anthu ankamumanga manja ndi maunyolo, nkumumanganso miyendo ndi zitsulo kuti amugwiritse bwino. Koma iyeyo ankazingomwetsula zomangirazo, ndipo mzimuwo unkamupirikitsira ku thengo.)
30
Tsono Yesu adamufunsa munthuyo kuti, “Dzina lako ndani?” Iye adayankha kuti, “Dzina langa ndine Chigulu,” chifukwa mizimu yoipa yochuluka inali itamuloŵa.
31
Kenaka mizimuyo idapempha Yesu kuti asailamule kuti ikaloŵe ku chiphompho chao.
32
Pafupi pomwepo, pachitunda poteropo, pankadya gulu lalikulu la nkhumba. Tsono mizimu yoipa ija idapempha Yesu kuti ailole ikaloŵe m'nkhumbazo. Yesu adailoladi.
33
Iyo idatuluka, nkukaloŵadi m'nkhumbazo. Pomwepo gulu lonselo lidaguduka kutsika chitunda chija mwaliŵiro, nkukadziponya m'nyanja, mpaka kufera m'madzimo.
34
Oŵeta nkhumbazo ataona zimenezi, adathaŵa, nakauza anthu ku mzinda ndi ku midzi.
35
Anthuwo adatuluka kuti akaone zimene zidaachitikazo. Atafika kumene kunali Yesuko, adapeza munthu amene adaamtulutsa mizimu yoipa uja, atakhala pansi ku mapazi a Yesu, atavala, misala ija itatha. Anthuwo adagwidwa ndi mantha.
36
Anzao amene adaaonerera zonse zikuchitika, adaŵasimbira m'mene munthu wamizimuyo adaamchiritsira.
37
Apo anthu onse a ku malo ozungulira Geregesa adapempha Yesu kuti achoke kumeneko, chifukwa iwo anali ndi mantha aakulu. Choncho Yesu adaloŵa m'chombo, nkumabwerera ku tsidya.
38
Munthu amene adaamtulutsa mizimu yoipa uja adapempha Yesu kuti apite nao. Koma Yesu adamubweza namuuza kuti,
39
“Iyai, iwe bwerera kwanu, ukafotokoze zazikulu zimene Mulungu wakuchitira.” Munthuyo adapitadi kwao nkumakalengeza mumzinda monse zazikulu zimene Yesu adaamchitira.
40
Pamene Yesu adafikanso ku tsidya, chinamtindi cha anthu chidamchingamira, popeza kuti onse ankamudikira.
41
Tsono kudafika munthu wina, dzina lake Yairo, amene anali mmodzi mwa akulu a nyumba yamapemphero. Iye adadzigwetsa ku mapazi a Yesu, nayamba kumdandaulira kuti apite kunyumba kwake,
42
chifukwa mwana wake wamkazi anali pafupi kufa. Anali wa zaka khumi ndi ziŵiri, ndipo mwana anali yekhayo. Pamene Yesu ankapita kumeneko, anthu aja ankamupanikiza.
43
Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri. Adaamwaza chuma chake chonse kulipira asing'anga, koma panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kumchiza.
44
Iyeyu adafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza mphonje ya chovala chake, ndipodi nthaŵi yomweyo matenda a msambowo adaleka.
45
Pompo Yesu adafunsa kuti, “Ndani wandikhudza?” Poti onse ankangoti, “Kaya,” Petro adati, “Aphunzitsi, anthu onseŵa akuzungulirani ndipo akukupanikizani.”
46
Koma Yesu adati, “Iyai, wina wandikhudza ndithu. Ndazindikira kuti mphamvu zina zatuluka mwa Ine.”
47
Pamene mai uja adaona kuti sangathenso kudzibisa, adadza monjenjemera nadzigwetsa ku mapazi a Yesu. Adafotokoza pamaso pa anthu onse aja chifukwa chimene adaakhudzira Yesu, ndiponso m'mene adachirira nthaŵi yomweyo.
48
Apo Yesu adamuuza kuti, “Inu mwana wanga, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani. Pitani ndi mtendere.”
49
Yesu akulankhulabe, kudafika munthu wina kuchokera kunyumba kwa mkulu wa nyumba yamapemphero uja. Adamuuza mkuluyo kuti, “Mwana uja watsirizika. Musaŵavutenso Aphunzitsiŵa.”
50
Yesu atamva mauwo adauza Yairo kuti, “Musaope ai, inu mungokhulupira, ndipo mwanayo akhalanso bwino.”
51
Pamene Yesu adafika kunyumba kuja, sadalole kuti wina aliyense aloŵe naye, koma Petro, Yohane ndi Yakobe, ndiponso bambo wake wa mwanayo ndi mai wake.
52
Anthu onse ankalira ndi kubuma. Koma Yesu adati, “Musalire, mwanayutu sadamwalire ai, ali m'tulo chabe.”
53
Pamenepo anthuwo adayamba kumseka monyodola, chifukwa ankadziŵa kuti mwanayo wamwalira basi.
54
Yesu adagwira mwanayo pa dzanja nanena mokweza mau kuti, “Mwana iwe, dzuka!”
55
Pomwepo moyo wake udabwereramo, iyeyo nkudzukadi nthaŵi yomweyo. Kenaka Yesu adaŵauza kuti ampatse chakudya mtsikanayo.
56
Makolo ake aja adazizwa kwambiri, koma Yesu adaŵalamula kuti asauze wina aliyense zimene zidaachitikazo.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24