bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 5
Luke 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 6 →
1
Tsiku lina Yesu adaaimirira pamphepete pa nyanja ya Genesarete, anthu ambirimbiri nkumamupanikiza kuti amve mau a Mulungu.
2
Iye adaona zombo ziŵiri pamphepetepo. Asodzi anali atatulukamo, ndipo ankatsuka makoka ao.
3
Yesu adaloŵa m'chombo chimodzi, chimene chinali cha Simoni, nampempha kuti asunthire pang'ono ku nyanja. Adakhala pansi, ndipo ali m'chombo momwemo, adayamba kuŵaphunzitsa anthuwo.
4
Atatsiriza kulankhula, adauza Simoni kuti, “Sunthirani kozamako, muponye makoka anu kuti muphe nsomba.”
5
Simoni adati, “Aphunzitsi, usiku wonsewu takhalira kugwira ntchito, osapha kanthu, koma chifukwa Inuyo mwatero, chabwino ndiponya makoka.”
6
Tsono iwo adaponyadi makoka, napha nsomba zambirimbiri, kotero kuti makokawo ankayamba kung'ambika.
7
Adachita kukodola anzao a m'chombo china chija kuti adzaŵathandize. Iwo adabwera, ndipo adadzaza zombo ziŵiri zonse zija mpaka zinali pafupi kumira.
8
Pamene Simoni Petro adaona zimenezo, adagwada nkuŵerama kwambiri pamaso pa Yesu nati, “Pepani Ambuye, mundichokere, ndine munthu wochimwa.”
9
Adaatero popeza kuti iye, pamodzi ndi onse amene anali naye, adaazizwa nako kuchuluka kwa nsomba zimene adaaphazo.
10
Yakobe ndi Yohane, ana a Zebedeo, anzake a Simoni, nawonso adaazizwa. Tsono Yesu adauza Simoni kuti, “Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.”
11
Motero, atakokera zombozo ku mtunda, adasiya zonse namatsata Yesu.
12
Pamene Yesu anali m'mudzi wina, kudabwera munthu wina wa khate thupi lonse. Pamene adaona Yesu, adadzigwetsa moŵerama pansi pamaso pake nayamba kumdandaulira. Adati, “Ambuye, mutafuna, mungathe kundichiritsa.”
13
Yesu adatambalitsa dzanja nkumukhudza, nati, “Chabwino, ndikufuna, chira!” Pomwepo khate lake lija lidatha.
14
Tsono Yesu adamuuza kuti, “Chenjera, usakambire wina aliyense zimenezi. Ingopita, ukadziwonetse kwa wansembe ndipo ukapereke nsembe adalamula Mose ija. Imeneyo ikhale yotsimikizira anthu onse kuti wachiradi.”
15
Komabe mbiri ya Yesu inkawandirawandira, ndipo makamu ambiri a anthu ankasonkhana kuti amve mau ake, ndiponso kuti aŵachize nthenda zao.
16
Koma Iye adapita kumalo kosapitapita anthu, namakapemphera kumeneko.
17
Tsiku lina Yesu ankaphunzitsa. Pomwepo padaakhala Afarisi ena ndi aphunzitsi ena a Malamulo, ochokera ku midzi yonse ya ku Galileya, ndi ya ku Yudeya, ndiponso ku Yerusalemu. Mphamvu zochokera kwa Ambuye zinali mwa Iye kuti azichizira odwala.
18
Tsono kudafika anthu ena ndi munthu wofa ziwalo, atamnyamulira pa machira. Adayesa kuloŵa naye m'nyumba kuti amkhazike pamaso pa Yesu.
19
Koma chifukwa anthu adaachuluka, sadapeze poloŵera naye. Motero adakwera pa denga, nachotsapo mapale ena, nkumutsitsa ndi machira ake omwe kumufikitsa pansi pakati pa anthu, pamaso pa Yesu.
20
Poona chikhulupiriro chaocho, Yesu adati, “Mbale wanga, machimo ako akhululukidwa.”
21
Apo aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi aja adayamba kudzifunsa mumtima mwao kuti, “Ndaninso kodi amene akunyoza Mulungu mwachipongweyu? Ndani angakhululukire machimo, si Mulungu yekha kodi?”
22
Yesu adaadziŵa maganizo ao, ndiye adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuganiza zimenezo mumtima mwanu?
23
Chapafupi koposa nchiti, kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Dzuka, yamba kuyenda?’
24
Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa Munthu ali nazo mphamvu pansi pano zokhululukira machimo, onani.” Pamenepo adauza wofa ziwalo uja kuti, “Iwe, ndikuti dzuka, tenga machira ako, uzipita kumudzi.”
25
Pomwepo wodwalayo adadzukadi onse akupenya, ndipo adatenga machira aja amene adaagonapo, namapita kwao akutamanda Mulungu.
26
Anthu onse aja adazizwa kwambiri, nayamba kutamanda Mulungu. Adagwidwa ndi mantha nati, “Taona zodabwitsa lero.”
27
Pambuyo pake Yesu adatuluka naona munthu wokhometsa msonkho, dzina lake Levi, ali pa ntchito m'nyumba ya msonkho. Adamuuza kuti, “Iwe, unditsate.”
28
Iye adanyamuka, nasiya zonse, nkumamutsatadi.
29
Tsono Levi adamkonzera Yesu phwando lalikulu kunyumba kwake. Okhometsa msonkho ambirimbiri, pamodzi ndi anthu ena, anali nao paphwandopo.
30
Afarisi pamodzi ndi aphunzitsi ao a Malamulo adayamba kuŵinya, nafunsa ophunzira ake kuti, “Bwanji mukudya ndi kumwa pamodzi ndi okhometsa msonkho, ndi anthu ochimwa?”
31
Yesu adaŵayankha kuti, “Anthu amene ali bwino sasoŵa sing'anga ai, koma amene akudwala.
32
Inetu sindidabwere kudzaitana anthu olungama, koma anthu ochimwa, kuti atembenuke mtima.”
33
Anthu ena adauza Yesu kuti, “Ophunzira a Yohane amasala zakudya kaŵirikaŵiri nkumapemphera, chimodzimodzinso ophunzira a Afarisi. Koma ophunzira anu amangodya ndi kumwa.”
34
Yesu adati, “Kani anzake a mkwati angathe kumasala zakudya pamene mkwati ali nao pomwepo? Chosatheka!
35
Koma idzafika nthaŵi pamene adzaŵachotsera mkwatiyo. Pamenepo ndiye azidzasala zakudya.”
36
Yesu adaŵapheranso fanizo, adati, “Munthu sang'amba chigamba ku chovala chatsopano nkuchisokerera pa chovala chakale. Chifukwa akatero, waononga chovala chatsopanocho, ndipo chigamba chatsopanocho sichidzayenerana ndi chovala chakale chija.
37
“Ndiponso munthu sathira vinyo watsopano m'matumba achikopa akale. Chifukwa akatero, vinyo watsopanoyo amaphulitsa matumba aja. Choncho vinyoyo adzatayika, matumbawo nkutha ntchito.
38
Koma vinyo watsopano amamuthira m'matumba atsopanonso.
39
“Ndipo munthu akangolaŵa vinyo wakale, watsopano sangamufune. Pajatu amati, ‘Wakale ndiye vinyo chaiye.’ ”
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24