bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 7
Luke 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 8 →
1
Yesu atatsiriza kulankhula zonsezi ndi anthu aja, adapita ku Kapernao.
2
Tsono mkulu wina wa gulu la asilikali achiroma 100 anali ndi wantchito amene ankamukonda kwambiri. Wantchitoyo ankadwala, ndipo anali pafupi kufa.
3
Mkuluyo atamva za Yesu, adatuma akulu ena a Ayuda kwa Iye kukampempha kuti adzachiritse wantchito wakeyo.
4
Pamene adafika kwa Yesu, adampempha kolimba namuuza kuti, “Ameneyu ngwoyeneradi kuti mumchitire zimenezi,
5
chifukwa amaukonda mtundu wathu, mwakuti adatimangira nyumba yamapemphero.”
6
Tsono Yesu adapita nawo. Pamene Iye ankayandikira nyumba yake, mkulu wa asilikali uja adatuma abwenzi ake kwa Yesu kukamuuza kuti, “Ambuye, musadzivute, pakuti sindili woyenera kuti Inu nkuloŵa m'nyumba mwanga.
7
Nchifukwa chake sindidadziyesenso woyenera kudza kwa Inu. Koma mungonena mau okha kuti wantchito wanga achire.
8
Inetu ndili ndi akuluakulu ondilamulira, komanso ndili ndi asilikali amene ineyo ndimaŵalamulira. Ndimati ndikauza wina kuti, ‘Pita’, amapitadi. Ndikauzanso wina kuti, ‘Bwera’, amabweradi. Ndipo ndikauza kapolo wanga kuti, ‘Chita chakuti’, amachitadi.”
9
Yesu atamva zimenezi, adachita naye chidwi. Adatembenuka nauza chinamtindi cha anthu amene ankamutsata aja kuti, “Ndithudi, ngakhale pakati pa Aisraele sindidapeze chikhulupiriro chotere.”
10
Otumidwa aja adabwerera kunyumba, nakapeza wantchito uja atachiritsidwa.
11
Pambuyo pake Yesu adapita ku mudzi wina, dzina lake Naini. Ophunzira ake pamodzi ndi anthu ena ambirimbiri adatsagana naye.
12
Pamene Yesu ankayandikira chipata cha mudziwo, adakumana ndi anthu atanyamula maliro. Womwalirayo anali mwana wamwamuna. Mai wake wa mwanayo anali wamasiye, ndipo mwana wake anali yekhayo. Anthu ambirimbiri am'mudzimo anali naye.
13
Pamene Ambuye adamuwona, adamumvera chisoni, namuuza kuti, “Mai, musalire.”
14
Tsono adafika pafupi nakhudza chithathacho. Anthu amene ankanyamula malirowo adaima, ndipo Yesu adati, “Mnyamata iwe, ndikukuuza kuti, Uka.”
15
Pamenepo wakufayo adakhala tsonga nayamba kulankhula, Yesu nkumupereka kwa mai wake.
16
Anthu onse adachita mantha, nayamba kutamanda Mulungu. Adati, “Mneneri wamkulu waoneka pakati pathu.” Adatinso, “Mulungu wadzathandiza anthu ake.”
17
Mbiri ya Yesuyi idawanda m'dziko lonse la Yudeya, ndi ku madera onse ozungulira.
18
Ophunzira a Yohane adamsimbira zonsezi Yohaneyo.
19
Tsono iye adaitanapo ophunzira ake ena aŵiri, naŵatuma kwa Ambuye kukaŵafunsa kuti, “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?”
20
Pamene iwo adafika kwa Yesu, adamuuza kuti, “Yohane Mbatizi watituma kwa Inu kuti tidzakufunseni kuti, ‘Kodi Inuyo ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?’ ”
21
Nthaŵi imeneyo nkuti Yesu akuchiritsa kumene nthenda zosiyanasiyana za anthu ambiri. Ankatulutsa mizimu yoipa, nkumapenyetsa anthu akhungu ambiri.
22
Tsono Iye adayankha ophunzira a Yohane aja kuti, “Pitani, kamuuzeni Yohane zimene mwaona ndi kuzimva. Akhungu akupenya, opunduka miyendo akuyenda, akhate akuchira, agonthi akumva, akufa akuukitsidwa, ndipo amphaŵi akumva Uthenga Wabwino.
23
Ngwodala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.”
24
Amithenga a Yohane aja atachoka, Yesu adayamba kufunsa makamu a anthu aja za Yohane kuti, “Kodi m'mene mudaapita ku chipululu, mudaati mukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?
25
Nanga mudaati mukaona chiyani? Munthu wovala zofeŵa kodi? Iyai, anthu ovala zakaso ndi okonda madyerero amakhala m'nyumba za mafumu.
26
Tanenanitu, mudaati mukaona chiyani? Mneneri kodi? Zoonadi, ndipo ndikunenetsa kuti mudakaona woposa mneneri.
27
Ameneyu ndiye uja Malembo akunena zakeyu kuti, “ ‘Nayitu nthumwi yanga, ndikuituma m'tsogolo mwako, kuti ikakonzeretu njira yodzadzeramo iwe.’
28
“Ndithu ndikunenetsa kuti mwa anthu onse amene adabadwa pansi pano, palibe ndi mmodzi yemwe woposa Yohane. Komabe ngakhale amene ali wamng'onong'ono mu Ufumu wa Mulungu amampambana.
29
Anthu onse, ndi okhometsa msonkho omwe, adamva mau a Yohane, ndipo pakubatizidwa ndi Yohaneyo adavomereza kuti Mulungu ngwolungama.
30
Koma Afarisi ndi akatswiri a Malamulo, pakukana kubatizidwa ndi iye, adakana okha zimene Mulungu adafuna kuŵachitira.
31
“Kaya anthu amakonoŵa ndingaŵafanizire ndi chiyani? Ali ngati chiyani?
32
Ali ngati ana okangana pa msika, ena akufunsa anzao kuti, “ ‘Tidaakuimbirani ng'oma yaukwati, bwanji inu osavina? Tidaabuma maliro, bwanji inu osalira?’
33
“Paja Yohane Mbatizi atabwera, ankasala zakudya ndipo sankamwa vinyo, inu nkumati, ‘Adagwidwa ndi mizimu yoipa.’
34
Mwana wa Munthu adabwera, nkumadya ndi kumwa ndithu, inu mumvekere, ‘Tamuwonani, munthuyu ndi wadyera, chidakwa, ndiponso bwenzi la anthu amsonkho ndi anthu osasamala Malamulo.’
35
Komabe chilungamo cha nzeru za Mulungu chimatsimikizika ndi zochita zake.”
36
Wina wa m'gulu la Afarisi adaitana Yesu kuti akadye kwao. Yesu adapita nakaloŵa m'nyumba ya Mfarisiyo nkukakhala podyera.
37
M'mudzimo mudaali mai wachiwerewere. Iyeyu atamva kuti Yesu akudya m'nyumba ya Mfarisi uja, adabwera ndi nsupa yagalasi ya mafuta onunkhira.
38
Adakagwada kumbuyo, ku mapazi a Yesu, akulira, nayamba kukhetsera misozi pa mapazi a Yesu, nkumaŵapukuta ndi tsitsi la kumutu kwake. Adampsompsonanso mapazi akewo, naŵadzoza ndi mafuta aja.
39
Koma Mfarisi amene adaaitana Yesu uja ataona zimenezi, adayamba kuganiza kuti, “Munthuyu akadakhaladi mneneri, bwenzi atamdziŵa mai amene akumkhudzayu, kuti ndi wachiwerewere.”
40
Apo Yesu adamuuza kuti, “Simoni, ndili ndi nkhani yoti ndikuuze.” Iye adati, “Aphunzitsi, nenani.”
41
Yesu adati, “Panali anthu aŵiri amene adaakongola ndalama kwa munthu wokongoza ndalama. Wina adaakongola ndalama makumi asanu, wina ndalama zisanu.
42
Popeza kuti adaalibe choti abwezere, adaŵakhululukira ngongolezo onse aŵiri. Tsono iweyo ukuganiza kuti mwa aŵiriŵa ndani adzakonde wokongozayo koposa?”
43
Simoni adati, “Ndiyesa koma amene adamkhululukira zambiri uja.” Yesu adamuuza kuti, “Wayankha bwino.”
44
Atatero, Yesu adacheukira mai uja, nauza Simoni kuti, “Ukumuwona maiyu? Ine ndaloŵa m'nyumba mwako muno, iwe sudandipatse madzi otsukira mapazi anga. Koma iyeyu wakhala akukhetsera misozi pa mapazi anga, nkumaŵapukuta ndi tsitsi lake.
45
Iwe sudandimpsomphsone, koma iyeyu chiloŵere changa muno, wakhalira kumpsompsona mapazi anga osalekeza.
46
Iwe sudandidzoze kumutu kwanga ndi mafuta, koma iyeyu wadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira.
47
Mwakuti kunena zoona, chikondi chachikulu chimene iyeyu waonetsa, chikutsimikiza kuti Mulungu wamkhululukiradi machimo ake amene ali ochuluka. Koma munthu amene wakhululukidwa zochepa, amangokonda pang'ono.”
48
Ndipo Yesu adauza mai uja kuti, “Machimo ako akhululukidwa.”
49
Apo amene ankadya naye adayamba kudzifunsa mumtima mwao kuti, “Kodi ndani uyu wokhululukira ndi machimo omweyu?”
50
Koma Yesu adauza maiyo kuti, “Chikhulupiriro chanu chakupulumutsani. Pitani ndi mtendere.”
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24