bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 12
Luke 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 13 →
1
Nthaŵi imeneyo nkuti chikhamu cha anthu zikwi ndi zikwi chikusonkhana, kotero kuti anthuwo ankangopondana. Yesu adayamba kulankhula ndi ophunzira ake poyamba, Adati, “Chenjerani ndi chofufumitsira buledi cha Afarisi, chimene chili chiphamaso.
2
Kanthu kalikonse kovundikirika kadzaululuka, ndipo kalikonse kobisika kadzadziŵika.
3
Nchifukwa chake zonse zimene mwalankhula pa mdima, zidzamveka poyera, ndipo zonse zimene mwanong'oneza anthu m'kati mwa nyumba, adzazilengeza pa bwalo.”
4
“Ndikukuuzani inu, abwenzi anga, kuti musamaopa anthu. Iwo angathe kupha thupi lokha, koma pambuyo pake alibenso china choti angachitepo.
5
Koma ndikuchenjezeni: amene muyenera kumuwopa ndi Mulungu. Iye atalanda moyo wa munthu, ali nazonso mphamvu za kumponya m'Gehena. Ndithu ndi ameneyo amene muzimuwopa.
6
“Suja amagulitsa atimba asanu tindalama tiŵiri? Komabe Mulungu saiŵala ndi mmodzi yemwe.
7
Ndipo tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.”
8
“Ndithu kunena zoona, aliyense wondivomereza pamaso pa anthu, Inenso Mwana wa Munthune ndidzamuvomereza pamaso pa angelo a Mulungu.
9
Koma aliyense wondikana pamaso pa anthu kuti sandidziŵa, Inenso Mwana wa Munthune ndidzamkana pamaso pa angelo a Mulungu kuti sindimdziŵa.
10
“Aliyense wonenera zoipa Mwana wa Munthu, Mulungu adzamkhululukira, koma wonyoza Mzimu Woyera ndi mau achipongwe, Mulungu sadzamkhululukira.
11
“Akadzakutengerani ku milandu ku nyumba zamapemphero, kapena kwa mafumu ndiponso kwa akulu a Boma, musati mudzavutike nkumati, ‘Kaya ndikayankha bwanji? Ndikanena chiyani?’
12
Popeza kuti Mzimu Woyera adzakudziŵitsani pa nthaŵi yomweyo zimene mudzayenera kunena.”
13
Munthu wina pakati pa anthu onse aja adapempha Yesu kuti, “Aphunzitsi, takandiwuzirani mbale wanga kuti andigaŵireko chuma chamasiye.”
14
Koma Yesu adati, “Munthu iwe, ndani adandipatsa ntchito yokuweruzani kapena kumakugaŵirani chuma chanu chamasiye?”
15
Atatero adauza anthu aja kuti, “Chenjerani, ndipo mupewe khumbo lililonse lofuna zambiri. Pajatu ngakhale munthu akhale ndi chuma chochuluka chotani, chumacho sichingatchinjirize moyo wake.”
16
Tsono Yesu adaŵaphera fanizo. Adati, “Munthu wina wachuma m'munda mwake mudabereka dzinthu dzambiri.
17
Ndiye iye uja adayamba kuganiza kuti, ‘Nditani, poti ndilibe mosungira dzinthu dzanga?’
18
Tsono adati, ‘Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga nkumanga zina zazikulu, ndipo ndidzasungira dzinthu dzanja dzonse ndi chuma changa m'menemo.
19
Kenaka ndidzauza mtima wanga kuti, Iwe mtima wanga, uli ndi chuma chambiri chimene chidzakukwanira zaka zambiri. Upumule, uzidya, uzimwa ndi kusangalala!’
20
Koma Mulungu adamuuza kuti, ‘Wopusawe! Usiku womwe uno akulanda moyo wako. Nanga zonse zimene wadzisungirazi zidzakhala za yani?’ ”
21
Potsiriza Yesu adati, “Zimatero ndi munthu amene amadziwunjikira chuma, koma sali wachuma konse pamaso pa Mulungu.”
22
Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji.
23
Pakuti moyo umaposa chakudya, ndipo thupi limaposa zovala.
24
Onani makwangwala. Safesa, sakolola, alibe nyumba yosungiramo zinthu, kapena nkhokwe, komabe Mulungu amaŵadyetsa. Inu mumazipambana mbalamezo kutali.
25
Ndani mwa inu ndi maganizo ankhaŵa angathe kuwonjezera ngakhale tsiku limodzi pa moyo wake?
26
Tsono ngati simungathe kuchita ngakhale kanthu kakang'ono kotere, bwanji mukudera nkhaŵa zinazo?
27
Onani maluŵa m'mene amakulira. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu ai. Komatu kunena zoona, ngakhale mfumu Solomoni yemwe, mu ulemerero wake wonse, sankavala zokongola kulingana ndi limodzi lomwe mwa maluŵa ameneŵa.
28
Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wakuthengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu?
29
Nchifukwa chake musamadera nkhaŵa ndi kufunafuna zoti mudye, kapena zoti mumwe.
30
Paja zimenezi amazifunafuna ndi anthu a mitundu yonse yapansipano. Atate anu amadziŵa kuti mumazisoŵa zimenezi.
31
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.”
32
“Inu nkhosa zanga, ngakhale muli oŵerengeka, musaope, pakuti kudakomera Atate anu kuti akupatseni Ufumu wake.
33
Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupatse amphaŵi. Mudzipezere matumba a ndalama amene safwifwa, ndi kudziwunjikira chuma chokhalitsa Kumwamba; kumeneko mbala sizingafikeko, ndipo njenjete sizingachiwononge.
34
Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.”
35
“Khalani okonzeka kutumikira, ndipo nyale zanu zikhale zoyaka.
36
Khalani ngati antchito amene akudikira mbuye wao wochokera ku phwando la ukwati, kuti pamene afike ndi kugogoda, iwo amtsekulire msanga.
37
Ngodala antchito amene mbuye wao pofika, aŵapeza ali maso. Ndithu ndikunenetsa kuti adzadzikonzekera, nadzaŵakhazika podyera, ndipo adzabwera nkumaŵatumikira.
38
Ngodala antchitowo mbuye waoyo akadzaŵapeza ali choncho pamene iye adzafike, ngakhale pakati pa usiku kapena kuli pafupi kucha.
39
“Koma kumbukirani kuti, mwini nyumba akadadziŵiratu nthaŵi yoti mbala ifika, sibwenzi atalola kuti ithyole nyumba yake.
40
Choncho inunso khalani okonzeka, pakuti Mwana wa Munthu adzabwera pa nthaŵi imene simukuyembekeza.”
41
Pamenepo Petro adati, “Ambuye, kodi fanizoli mukuphera ife tokha, kapena mukuuza onse?”
42
Yesu adati, “Tsono kapitao wokhulupirika ndi wanzeru ndani, amene mbuye wake adzamuike kuti aziyang'anira onse a m'nyumba mwake, nkumaŵagaŵira chakudya chao pa nthaŵi yake?
43
Ngwodala wantchito ameneyo, ngati mbuye wake pofika adzampeza akuchitadi zimenezi.
44
Ndithu ndikunenetsa kuti adzamuika woyang'anira chuma chake chonse.
45
“Koma ngati ndi wantchito woipa, mumtima mwake azidzati, ‘Mbuye wanga akuchedwa kubwera.’ Ndiye adzayamba kumenya antchito anzake, amuna ndi akazi, ndiponso kumadya, kumamwa ndi kuledzera.
46
Tsono mbuye wake adzangoti mbwe mwadzidzidzi, pa tsiku limene iye sakumuyembekeza. Choncho adzamlanga koopsa, ndipo adzamtaya ku malo a anthu osakhulupirika.
47
“Wantchito amene akudziŵa zimene mbuye wake amafuna, koma osakonzekera kuzichita, adzamkwapula kwambiri.
48
Koma wantchito amene sadziŵa zimene mbuye wake amafuna, tsono nkumachita zoyenera kumlanga nazo, adzamkwapula pang'ono. Aliyense amene adalandira zambiri, adzayenera kubweza zambiri. Ndipo amene adamsungiza zambiri, adzamlamula kuti abweze zochuluka koposa.”
49
“Ndidabwera kudzaponya moto pa dziko lapansi, ndipo ndikadakonda utayaka kale.
50
Koma ndiyenera kuyamba ndaloŵa m'masautso akulu, ndipo mtima wanga sukhazikika mpaka zitachitika.
51
Kodi mukuyesa kuti ndidadzapereka mtendere pansi pano? Iyai, kunena zoona, osati mtendere koma kugaŵikana.
52
Kuyambira tsopano m'banja limodzi mudzakhala anthu asanu ogaŵikana, atatu adzakangana ndi aŵiri, ndipo aŵiri adzakangana ndi atatu.
53
Bambo adzakangana ndi mwana wake wamwamuna, mwana wamwamuna adzakangana ndi bambo wake. Mai adzakangana ndi mwana wake wamkazi, mwana wamkazi adzakangana ndi mai wake. Apongozi adzakangana ndi mkazi wa mwana wao, ndipo mkaziyo adzakangana ndi apongozi akewo.”
54
Yesu adauzanso anthu onse aja kuti, “Mukaona mtambo ukukwera kuzambwe, pompo mumati, ‘Mvula ikubwera,’ ndipo imabweradi.
55
Mphepo yakumwera ikamaomba, mumati, ‘Kutentha,’ ndipo kumatenthadi.
56
Inu anthu achiphamaso, mumatha kuzindikira maonekedwe a dziko lapansi ndi a kuthambo, koma bwanji simutha kuzindikira tanthauzo la zimene zikuchitika masiku omwe ano?”
57
“Bwanji simutsimikiza nokha zoyenera kuchita?
58
Monga pamene ukupita ndi mnzako wamlandu kwa woweruza, uyesetse kukonza mlanduwo mukali pa njira, kuwopa kuti angakupereke kwa woweruza, woweruzayo angakakupereke kwa msilikali, ndipo msilikaliyo angakakuponye m'ndende.
59
Ndithu ndikunenetsa kuti sudzatulukamo mpaka utalipira zonse.”
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
Recommended Reading
Commentary
Luke Commentaries
→
Devotional
Luke Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→