bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 6
Luke 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 7 →
1
Pa tsiku lina la Sabata Yesu ankadutsa m'minda ya tirigu. Ophunzira ake ankathyolako ngala za tirigu, namazifikisa ndi manja, nkumadya.
2
Apo Afarisi ena adafunsa kuti, “Bwanji mukuchita zimene siziloledwa pa tsiku la Sabata?”
3
Yesu adati, “Kani simudaŵerenge zimene adaachita Davide, pamene iye ndi anzake adaazingwa nayo njala?
4
Suja adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, natenga buledi woperekedwa kwa Mulungu, naadya, nkupatsakonso anzake aja? Chonsecho nkosaloledwa kuti buledi ameneyo wina aliyense nkumudya kupatula ansembe okha.”
5
Tsono Yesu popitiriza adaŵauza kuti, “Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro wonse pa zokhudza tsiku la Sabata.”
6
Pa tsiku lina la Sabata Yesu adaloŵa m'nyumba yamapemphero nkumaphunzitsa. M'menemo munali munthu wina wopuwala dzanja lamanja.
7
Aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi ankafuna chifukwa choti akamnenezere Yesuyo, motero ankamuyang'anitsitsa kuti aone ngati achiritse munthu pa tsiku la Sabata.
8
Koma Yesu adaadziŵa maganizo ao, tsono adalamula munthu wopuwala dzanja uja kuti, “Tabwera, udzaime kutsogolo kuno.” Iye adanyamuka nakaima kutsogoloko.
9
Pamenepo Yesu adauza anthu aja kuti, “Ntakufunsani, kodi Malamulo amalola chiti pa tsiku la Sabata, kuchitira munthu zabwino, kapena kumchita zoipa? Kupulumutsa moyo wa munthu, kapena kuuwononga?”
10
Adaŵayang'ana onsewo, kenaka adalamula munthu uja kuti, “Tambalitsa dzanja lako.” Iye adalitambalitsa, ndipo dzanja lakelo lidakhalanso bwino.
11
Koma akuluakulu aja adakwiya kwambiri, nayamba kukambirana zoti achite naye Yesu.
12
Masiku amenewo Yesu adapita ku phiri kukapemphera, ndipo adachezera usiku wonse akupemphera kwa Mulungu.
13
Kutacha adaitana ophunzira ake, nasankhapo khumi ndi aŵiri. Adaŵatcha “atumwi.”
14
Anthu ake anali aŵa: Simoni (amene Yesu adamutcha dzina loti Petro) ndi mbale wake Andrea; Yakobe ndi Yohane; Filipo ndi Bartolomeo;
15
Mateyo ndi Tomasi; Yakobe (mwana wa Alifeyo) ndi Simoni (wa m'chipani chandale cha Azelote;)
16
Yudasi (mwana wa Yakobe) ndiponso Yudasi Iskariote (amene pambuyo pake adapereka Yesu kwa adani ake.)
17
Yesu adatsika phiri pamodzi ndi ophunzira ake, naima pa chidikha. Panali khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi anthu ena ambirimbiri ochokera ku dera lonse la Yudeya ndi ku Yerusalemu, ndi ku mbali yakunyanja, ku Tiro, ndi ku Sidoni.
18
Iwo adabwera kudzamva mau ake, ndiponso kuti Iye aŵachiritse. Anthu amene ankasautsidwa ndi mizimu yoipa, amenewonso Iye ankaŵachiritsa.
19
Anthu onsewo ankafuna kumkhudza, chifukwa mphamvu zinkatuluka mwa Iye ndi kuŵachiritsa onse.
20
Yesu adayang'ana ophunzira ake, naŵauza kuti, “Ndinu odala, inu osaukanu, Ufumu wa Mulungu ndi wanu.
21
“Ndinu odala, inu amene mukumva njala tsopano, chifukwa mudzakhuta. “Ndinu odala, inu amene mukulira tsopano, chifukwa mudzakondwa.
22
“Ndinu odala anthu akamadana nanu, akamakusalani ndi kukuchitani chipongwe, ndipo akamaipitsa dzina lanu chifukwa cha Ine Mwana wa Munthu.
23
Nthaŵi imeneyo sangalalani ndi kuvina ndi chimwemwe, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi zomwenso makolo ao ankaŵachita aneneri kale.
24
“Koma ndinu atsoka, anthu achumanu, chifukwa mwalandiriratu zokusangalatsani.
25
Ndinu atsoka, amene mukukhuta tsopanonu, chifukwa mudzamva njala. Ndinu atsoka, amene mukukondwa tsopanonu, chifukwa mudzamva chisoni ndiponso mudzalira.
26
“Ndinu atsoka, anthu onse akamakuyamikani. Paja makolo ao ankachitira aneneri onama akale zomwezi.”
27
“Koma inu amene mukumva mau anga, ndikukuuzani kuti, Muzikonda adani anu, muziŵachitira zabwino amene amadana nanu.
28
Muziŵafunira madalitso amene amakutembererani, muziŵapempherera amene amakuvutitsani.
29
Ngati munthu akumenya pa tsaya, uperekere linalonso. Ndipo munthu akakulanda mwinjiro wako, umlole atenge ndi mkanjo womwe.
30
Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akatenga zinthu zako, usamlamule kuti abweze.
31
Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo.
32
“Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amakondanso amene amaŵakonda.
33
Ngati muchitira zabwino okhawo amene amakuchitirani zabwino, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amachita chimodzimodzi.
34
Ndipo ngati mukongoza okhawo amene mukudziŵa kuti adzakubwezerani, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amakongoza anzao ochimwa, kuti akalandirenso momwemo.
35
Iyai, inu muzikonda adani anu, muzichita zabwino, ndipo muzikongoza osayembekeza kulandirapo kanthu. Mukatero mudzalandira mphotho yaikulu, ndiye kuti mudzakhala ana a Mulungu Wopambanazonse. Pajatu Iye amachitira zabwino anthu osayamika ndi oipa omwe.
36
Monga Atate anu akumwamba ali achifundo, inunso mukhale achifundo.”
37
“Musamaweruza anthu ena kuti ngolakwa, ndipo Mulungu sadzakuweruzani. Musamaimba ena mlandu, ndipo Mulungu sadzakuimbani mlandu. Muzikhululukira ena, ndipo Mulungu adzakukhululukirani.
38
Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.”
39
Yesu adaŵapheranso fanizo, adati, “Kodi wakhungu nkutsogolera wakhungu mnzake? Nanga onse aŵiri sadzagwa m'dzenje kodi?
40
Wophunzira saposa mphunzitsi wake, koma aliyense pamene watsiriza maphunziro ake, adzafanafana ndi mphunzitsi wake.
41
“Umaoneranji kachitsotso kamene kali m'maso mwa mnzako, koma osaganizako za chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe?
42
Ungamuuze bwanji mbale wako kuti, ‘Mbale wanga, taima ntakuchotsa kachitsotso kali m'maso mwakoka,’ pamene iweyo sukuchiwona chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m'maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m'maso mwa mbale wako.”
43
“Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapenanso mtengo woipa kubala zipatso zabwino.
44
Mtengo uliwonse umadziŵika ndi zipatso zake. Sathyola nkhuyu pa minga, kapenanso mphesa pa mtula.
45
Munthu wabwino amatulutsa zabwino m'chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m'chuma choipa cha mumtima mwake. Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.”
46
“Bwanji mumangoti, ‘Ambuye, Ambuye,’ koma chonsecho simuchita zimene ndimanena?
47
Munthu aliyense wodza kwa ine, namva mau anga nkumaŵagwiritsa ntchito, ndikuuzani amene amafanafana naye.
48
Amafanafana ndi munthu womanga nyumba, amene adaakumba mozama, naika maziko pa thanthwe. Tsono chigumula chitafika, madzi ake adagunda nyumbayo, koma sadaigwedeze, chifukwa adaaimanga bwino.
49
Koma munthu wongomva mau anga, osaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu amene adaamanga nyumba pamwamba pa nthaka, osakumba maziko. Pamene madzi a chigumula adagunda nyumbayo, pompo idagwa, ndipo kuwonongeka kwake kunali kotheratu.”
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24