bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 3
Luke 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 4 →
1
Pa chaka cha khumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio, mfumu ya ku Roma, Ponsio Pilato anali bwanamkubwa ku Yudeya. Herode ankalamulira ku dera la Galileya. Filipo, mbale wake, ankalamulira ku dera la Itureya ndi ku dera la Trakoniti. Lisaniasi ankalamulira ku dera la Abilene,
2
ndipo Anasi ndi Kayafa anali akulu a ansembe onse. Pa nthaŵi imeneyo Mulungu adampatsira uthenga Yohane uja, mwana wa Zakariya, m'chipululu.
3
Choncho Yohaneyo adayendera dziko lonse lozungulira mtsinje wa Yordani, akulalika. Ankauza anthu kuti, “Tembenukani mtima ndi kubatizidwa, kuti Mulungu akukhululukireni machimo anu.”
4
Izi zidachitika monga zidaalembedwera m'buku la mneneri Yesaya kuti, “Liwu la munthu wofuula m'chipululu: akunena kuti, ‘Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo.
5
Dzazani chigwa chilichonse, chepetsani phiri lililonse ndi mtunda uliwonse. Ongolani njira zokhotakhota, salazani njira zazigolowondo.
6
Motero anthu onse adzaona chipulumutso chochokera kwa Mulungu.’ ”
7
Anthu ambirimbiri ankabwera kuti iye aŵabatize. Tsono iyeyo ankati, “Ana a njoka inu, adakuchenjezani ndani kuti muthaŵe chilango cha Mulungu chikudzachi?
8
Chitanitu ntchito zosonyeza kuti mwatembenukadi mtima. Ndipo m'mitima mwanu musayambe zomanena kuti, ‘Atate athu ndi Abrahamu.’ Ndithu ndikunenetsa kuti Mulungu angathe kusandutsa ngakhale miyala ili apayi kuti ikhale ana a Abrahamu.
9
Pali pano nkhwangwa ili kale patsinde pa mitengo. Choncho mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, adzaudula nkuuponya pa moto.”
10
Pamenepo anthu aja adafunsa Yohane kuti, “Tsono ife tizichita zabwino zanji?”
11
Iye adati, “Amene ali ndi miinjiro iŵiri, apatseko mnzake amene alibe. Ndipo amene ali nacho chakudya, achitenso chimodzimodzi.”
12
Kudabweranso okhometsa msonkho kuti Yohane aŵabatize. Iwo adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ife tizichita zabwino zanji?”
13
Iye adati, “Musamakhometsa msonkho moonjezera pa zimene adakulamulani.”
14
Asilikali omwe adamufunsa kuti, “Nanga ifeyo tizichita zabwino zanji?” Iye adati, “Musamalanda za munthu aliyense pakuwopseza kapena pakumnamizira. Muzikhutira ndi malipiro anu.”
15
Chiyembekezo cha anthu chidayamba kukula, ndipo onse ankaganiza za Yohane kuti kapena ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
16
Tsono Yohane ankaŵauza onse kuti, “Ine ndimakubatizani ndi madzi, koma akubwera wina woposa ine. Ameneyo ine ndine wosayenera ngakhale kumasula zingwe za nsapato zake. Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera ndiponso m'moto.
17
Chopetera chake chili m'manja kuti apete tirigu wake. Tsono adzathira tirigu m'nkhokwe, koma mankhusu adzaŵatentha m'moto wosazimika.”
18
Yohane ankalalikira anthu Uthenga Wabwino pakuŵalangiza motero, ndiponso mwa njira zina zambiri.
19
Komanso adadzudzula mfumu Herode chifukwa chokwatira Herodiasi, mkazi wa mbale wake, ndiponso chifukwa cha zoipa zina zambiri zimene ankachita.
20
Pambuyo pake, kuwonjezera pa zonsezi, Herode adatsekera Yohaneyo m'ndende.
21
Tsiku lina anthu onse aja atabatizidwa, Yesu nayenso adabatizidwa. Pamene Iye ankapemphera, kuthambo kudatsekuka,
22
ndipo Mzimu Woyera adatsikira pa Iye, akuwoneka ndi thupi ngati la nkhunda. Tsono kudamveka mau ochokera Kumwamba akuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera nawe kwambiri.”
23
Yesu anali ndi zaka ngati makumi atatu pamene adayamba ntchito yake ya kuphunzitsa. Anthu ankamuyesa mwana wa Yosefe, amene anali mwana wa Eli,
24
mwana wa Matati, mwana wa Levi, mwana wa Meliki, mwana wa Yanai, mwana wa Yosefe,
25
mwana wa Matatiasi, mwana wa Amosi, mwana wa Nahumu, mwana wa Hesili, mwana wa Nagai,
26
mwana wa Mahati, mwana wa Matatiasi, mwana wa Semeini, mwana wa Yoseke, mwana wa Yoda,
27
mwana wa Yohanani, mwana wa Resa, mwana wa Zerubabele, mwana wa Salatiele, mwana wa Neri,
28
mwana wa Meliki, mwana wa Adi, mwana wa Kosamu, mwana wa Elimadama, mwana wa Ere,
29
mwana wa Yose, mwana wa Eliezere, mwana wa Yorimu, mwana wa Matati, mwana wa Levi,
30
mwana wa Simeoni, mwana wa Yudasi, mwana wa Yosefe, mwana wa Yonamu, mwana wa Eliyakimu,
31
mwana wa Melea, mwana wa Mena, mwana wa Matata, mwana wa Natamu, mwana wa Davide,
32
mwana wa Yese, mwana wa Obede, mwana wa Bowazi, mwana wa Sala, mwana wa Nasoni,
33
mwana wa Aminadabu, mwana wa Adimini, mwana wa Arini, mwana wa Hesiromu, mwana wa Perezi, mwana wa Yuda,
34
mwana wa Yakobe, mwana wa Isaki, mwana wa Abrahamu, mwana wa Tera, mwana wa Nahoro,
35
mwana wa Serugi, mwana wa Reu, mwana wa Pelegi, mwana wa Ebere, mwana wa Sela,
36
mwana wa Kainani, mwana wa Arifaksadi, mwana wa Semu, mwana wa Nowa, mwana wa Lameki,
37
mwana wa Metusela, mwana wa Enoki, mwana wa Yaredi, mwana wa Mahalalele, mwana wa Kainani,
38
mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana wa Adamu, amene anali mwana wa Mulungu.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24