bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 17
Luke 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 18 →
1
Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Zochimwitsa anthu sizingalephere kuwoneka, koma tsoka kwa munthu wobwera nazoyo.
2
Kukadakhala kwabwino kuti ammangirire chimwala cha mphero m'khosi ndi kukamponya m'nyanja, kupambana kuti achimwitse mmodzi mwa ana ang'onoang'onoŵa.
3
Chenjerani tsono! “Mbale wako akachimwa, umdzudzule. Akatembenuka mtima, umkhululukire.
4
Akakuchimwira kasanunkaŵiri pa tsiku, nabwera kasanunkaŵiri kudzanena kuti, ‘Pepani,’ umkhululukire ndithu.”
5
Atumwi adapempha Ambuye kuti, “Mutiwonjezere chikhulupiriro.”
6
Koma Ambuye adati, “Mukadakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa kwambiri ngati kambeu ka mpiru, bwenzi mutauza mkuyu uwu kuti, ‘Zuka, kadzibzale m'nyanja,’ ndipo ukadakumverani ndithu.”
7
Yesu adatinso, “Utha kukhala ndi wantchito wolima ku munda kapena woŵeta nkhosa. Pamene iye wafika kuchokera ku munda, kodi ungamuuze kuti, ‘Bwera msanga, udzadye?’
8
Sungatero ai, koma udzamuuza kuti, ‘Konzere chakudya. Ukonzeke kunditumikira mpaka ineyo ndidye ndi kumwa. Iweyo udya ndi kumwa pambuyo pake.’
9
Kodi ungamthokoze wantchitoyo chifukwa chakuti wachita zimene unamlamula?
10
Choncho inunso, mutachita zonse zimene adakulamulani, muziti, ‘Ndife antchito osayenera kulandira kanthu. Tangochita zimene tinayenera kuchita.’ ”
11
Pa ulendo wake wopita ku Yerusalemu, Yesu adadzera m'malire a Samariya ndi Galileya.
12
Pamene ankaloŵa m'mudzi wina, anthu khumi akhate adadzamchingamira. Adaima kutali,
13
nanena mokweza mau kuti, “Yesu Ambuye, tichitireni chifundo.”
14
Pamene Yesu adaŵaona, adaŵauza kuti, “Pitani, kadziwonetseni kwa ansembe.” Pamene iwo ankapita, adachira.
15
Tsono mmodzi mwa iwo, ataona kuti wachira, adabwerera nayamba kuyamika Mulungu mokweza mau.
16
Adagwada nkuŵerama kwambiri pamaso pa Yesu, namthokoza. Koma munthuyo anali Msamariya.
17
Apo Yesu adati, “Kodi achira aja si khumi? Nanga asanu ndi anai ena aja ali kuti?
18
Ndiye kuti sadabwerere wina aliyense kudzayamika Mulungu, koma mlendo yekhayu?”
19
Kenaka Yesu adauza munthuyo kuti, “Nyamuka, pita. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”
20
Afarisi ena adafunsa Yesu kuti, “Kodi Mulungu adzakhazikitsa liti ufumu wake?” Yesu adaŵayankha kuti, “Mulungu sakhazikitsa ufumu wake mooneka ndi maso ai.
21
Anthu sadzati, ‘Suuwu, uli pano,’ kapena, ‘Suuwo,’ pakuti ngakhale tsopano Mulungu akukhazikitsa ufumu wake pakati panu.”
22
Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Akudza masiku pamene mudzalakalaka kuwona nthaŵi ya kudza kwa Mwana wa Munthu ngakhale tsiku limodzi lokha, koma simudzaloledwa ai.
23
Anthu azidzakuuzani kuti, ‘Suuwo uli uko,’ kapena, ‘Suuwu uli pano,’ musadzapiteko kapena kuŵatsatira ai.
24
Pajatu monga mphezi imang'anipa nkuŵala kuchokera mbali ina ya kuthambo kufikira mbali yake ina, Mwana wa Munthu adzateronso pa tsiku la kubwera kwake.
25
Koma Iye ayenera kuti ayambe wamva zoŵaŵa zambiri, ndipo kuti anthu amakono amkane.
26
“Monga momwe zidaachitikira pa nthaŵi ya Nowa, zidzateronso pa nthaŵi ya Mwana wa Munthu.
27
Masiku amenewo anthu ankangodya ndi kumwa, ankakwatira ndi kumakwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa adaloŵa m'chombo. Pamenepo chigumula chidafika nkuŵaononga onse.
28
Monga momwe zidaachitikiranso pa nthaŵi ya Loti. Anthu ankangodya ndi kumwa, ankagulitsana malonda, ankabzala mbeu, ankamanga nyumba.
29
Koma tsiku limene Loti adatuluka m'Sodomu, Mulungu adagwetsa moto ndi miyala yoyaka ya sulufule nkuŵaononga onsewo.
30
Zidzateronso pa tsiku limene Mwana wa munthu adzaoneke.
31
“Tsiku limenelo, amene ali pa denga, asadzatsike kukatenga katundu wake m'nyumba. Chimodzimodzinso amene ali ku munda, asadzabwerere ku nyumba.
32
Kumbukirani za mkazi wa Loti.
33
Aliyense woyesa kudzisungira moyo wake, adzautaya, koma woutaya adzausunga.
34
Kunena zoona, usiku umenewo, padzakhala anthu aŵiri pa bedi limodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya.
35
Azimai aŵiri adzakhala akusinja pamodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya,
36
Anthu aŵiri adzakhala ali m'munda, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya.”
37
Apo ophunzira ake adamufunsa kuti, “Kodi zimenezi zidzachitikira kuti, Ambuye?” Yesu adati, “Kumene kwafera chinthu, nkumeneko kumasonkhana miphamba.”
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
Recommended Reading
Commentary
Luke Commentaries
→
Devotional
Luke Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→