bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 24
Luke 24
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
1
M'mamaŵa pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, azimai aja adapita ku manda, atatenga zonunkhira zimene adaakakonza.
2
Adapeza chimwala chija chili chogubuduza kale kuchoka pakhomo pa manda aja.
3
Adaloŵa m'mandamo koma sadaupeze mtembo wa Ambuye Yesu.
4
Akadali othedwa nzeru choncho pa zimenezo, adangoona anthu aŵiri ovala zovala zonyezimira ataimirira pafupi ndi iwo.
5
Akazi aja adachita mantha naŵeramitsa nkhope zao pansi. Anthuwo adaŵafunsa kuti, “Mukudzafuniranji munthu wamoyo pakati pa anthu akufa?
6
Sali muno ai, wauka. Kumbukirani zimene adaakuuzani akadali ku Galileya.
7
Paja adaakuuzani kuti, ‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa m'manja mwa anthu ochimwa, kupachikidwa pa mtanda, ndi kuuka kwa akufa patapita masiku atatu.’ ”
8
Apo akazi aja adaŵakumbukiradi mauwo,
9
ndipo atabwerako kumanda kuja, adasimbira zonsezo ophunzira khumi ndi mmodzi aja, ndi anthu ena onse.
10
Azimaiwo anali Maria wa ku Magadala, Yohana, ndi Maria, amake a Yakobe. Iwo pamodzi ndi anzao ena adasimbira atumwi aja zonsezi.
11
Koma zimenezo atumwiwo adangoziyesa zam'kutu, mwakuti sadaŵakhulupirire azimaiwo. [
12
Komabe Petro adanyamuka nathamangira ku manda. Adaŵeramiramo naona nsalu zamaliro zokha, kenaka nkubwerera kunyumba akudabwa ndi zimene zidaachitikazo.]
13
Tsiku lomwelo ophunzira aŵiri ankapita ku mudzi wotchedwa Emausi. Kuchokera ku Emausi kufika ku Yerusalemu ndi mtunda wokwanira ngati makilomita khumi ndi limodzi.
14
Ankakambirana za zonse zimene zidaachitika.
15
Akukambirana choncho nkumafunsana, Yesu mwiniwake adayandikira nkumatsagana nawo.
16
Koma maso ao adaachita chidima, mwakuti sadamzindikire.
17
Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi mukunka mukukambirana zotani panjira pano?” Apo iwo adaima, nkhope zao zili zakugwa ndi chisoni,
18
kenaka mmodzi, dzina lake Kleopa, adamufunsa kuti, “Kodi mlendo ndinu nokha m'Yerusalemu muno, wosadziŵa zimene zachitika m'menemo masiku apitaŵa?”
19
Yesu adaŵafunsa kuti, “Zotani?” Iwo adati, “Za Yesu wa ku Nazarete. Iye anali mneneri amene mau ake ndi zochita zake zinali zamphamvu pamaso pa Mulungu ndi pa anthu omwe.
20
Akulu a ansembe ndi akulu athu ena adampereka kuti azengedwe mlandu ndi kuphedwa, ndipo adampachika pa mtanda.
21
Ife tinkayembekeza kuti Iyeyo ndiye adzaombole Aisraele, koma ha! Ndi dzana pamene zidachitika zonsezi.
22
Komanso azimai ena a m'gulu lathu anatidabwitsa. Iwowo anapita ku manda m'mamaŵa,
23
ndiye amati sadaupeze mtembo wake. Tsono atabwerako amadzasimba kuti anaona angelo amene anaŵauza kuti Yesu ali moyo.
24
Ena mwa ife anapita kumandako, ndipo anakapezadi monga momwe azimai aja amasimbira, koma Iyeyo sadamuwone ai.”
25
Apo Yesu adati, “Ha! Koma ndiye ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira msanga zonse zija zimene aneneri adanena.
26
Kodi inu simukudziŵa kuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adaayenera kumva zoŵaŵa zonsezi kuti aloŵe mu ulemerero wake?”
27
Kenaka Yesu adayamba kuŵatanthauzira zimene zidalembedwa za Iye m'Malembo onse, kuyambira pa mabuku a Mose mpaka mabuku a aneneri onse.
28
Atayandikira kumudzi kumene ankapita, Yesu adachita ngati akupitirira.
29
Koma iwo adamuumiriza kuti, “Mukhale nafe konkuno, poti kwayamba kuda; onani dzuŵa likuloŵa.” Apo Iye adakaloŵa m'nyumba nakakhala nawo.
30
Pamene adakhala nawo podyera, Yesu adatenga buledi, ndipo atathokoza Mulungu, adamnyema naŵagaŵira.
31
Nthaŵi yomweyo maso ao adatsekuka, namuzindikira, Iye nkuzimirira.
32
Tsono iwo adayamba kukambirana kuti, “Zoonadi ndithu, mitima yathu inachita kuti phwii, muja amalankhula nafe panjira paja, nkumatitanthauzira Malembo.”
33
Nthaŵi yomweyo adanyamuka kubwerera ku Yerusalemu. Adakapeza ophunzira khumi ndi mmodzi aja atasonkhana pamodzi ndi anzao ena,
34
akunena kuti, “Ambuye adaukadi, ndipo Simoni waŵaona.”
35
Tsono nawonso aŵiri aja adafotokoza zimene zidaachitika panjira paja, ndiponso m'mene iwo adaamzindikirira pamene Iye ankanyema buledi.
36
Iwo akulankhula choncho, Yesu mwiniwake adadzaimirira pakati pao nati, “Mtendere ukhale nanu.”
37
Koma iwo adadzidzimuka, nkuchita mantha poyesa kuti akuwona mzukwa.
38
Tsono Yesu adati, “Mukuvutikiranji, mukudzipheranji ndi mafunso m'mitima mwanu?
39
Onani manja anga ndi mapazi anga, kuti ndine ndithu. Khudzeni muwone, paja mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuwona kuti Ine ndili nazo.”
40
Atanena zimenezi adaŵaonetsa manja ake ndi mapazi ake.
41
Iwo sankakhulupirirabe chifukwa cha chimwemwe, ndipo adaathedwa nzeru. Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi pano muli nako kanthu kakudya?”
42
Adampatsa chidutsu cha nsomba yootcha.
43
Iye atalandira nsombayo, adaidya iwo akuwona.
44
Kenaka adaŵauza kuti, “Nzimenezitu zimene ndinkakuuzani pamene ndinali nanu. Paja ndinkanena kuti zonse ziyenera kuchitikadi zimene zidalembedwa za Ine m'Malamulo a Mose, m'mabuku a aneneri, ndi m'buku la Masalimo.”
45
Tsono adaŵathandiza kuti amvetse bwino Malembo.
46
Adaŵauza kuti, “Zimene zidalembedwa ndi izi: zakuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adayenera kumva zoŵaŵa, nkuuka kwa akufa patapita masiku atatu,
47
kuti m'dzina lake mau alalikidwe kwa anthu a mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.
48
Inuyo ndinu mboni zake za zimenezi.
49
Ine ndidzakutumizirani mphatso imene Atate anga adalonjeza. Koma inu bakhalani mumzinda muno mpaka mutalandira mphamvu zochokera Kumwamba.”
50
Atatero Yesu adaŵatsogolera kuchokera mumzindamo mpaka ku mudzi wa Betaniya. Kumeneko adakweza manja ake naŵadalitsa.
51
Akuŵadalitsa choncho, adalekana nawo, natengedwa kupita Kumwamba.
52
Iwo adampembedza, pambuyo pake nkubwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu.
53
Tsono ankasonkhana m'Nyumba ya Mulungu nthaŵi ndi nthaŵi akutamanda Mulungu.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
Recommended Reading
Commentary
Luke Commentaries
→
Devotional
Luke Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→