bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 15
Luke 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 16 →
1
Anthu onse okhometsa msonkho ndi Ayuda enanso onyozera Malamulo ankabwera kwa Yesu kudzamva mau ake.
2
Tsono Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo adayamba kuŵinya nkumanena kuti, “Munthu uyu amalandira anthu ochimwa, nkumadya nawo pamodzi.”
3
Tsono Yesu adaŵaphera fanizo ili, adati,
4
“Ndani mwa inu ali ndi nkhosa 100, imodzi itatayikapo, sangasiye nkhosa zina zonse 99 zija ku busa, nkukafunafuna yotayikayo mpaka ataipeza?
5
Ndipo ataipeza, amaisenza pamapewa pake mokondwa.
6
Pofika kwao, amasonkhanitsa abwenzi ake ndi anzake oyandikana nawo, naŵauza kuti, ‘Mukondwere nane pamodzi, chifukwa ndaipeza nkhosa yanga idaatayika ija.’ ”
7
Yesu adapitiriza mau kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti momwemonso Kumwamba kudzakhala chimwemwe chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima, kuposa anthu olungama 99 amene alibe chifukwa chotembenukira mtima.”
8
“Mwinanso mai amakhala ndi tindalama khumi, kamodzi nkutayika. Kodi suja amayatsa nyale nasesasesa m'nyumba nkufunafuna mosamala mpaka atakapeza?
9
Atakapeza amasonkhanitsa abwenzi ake ndi anzake oyandikana nawo, naŵauza kuti, ‘Mukondwere nane pamodzi, chifukwa ndakapeza kandalama kanga kaja kadaatayikaka.’ ”
10
Yesu popitiriza mau adati, “Ndikunenetsa kuti ndi m'menenso angelo a Mulungu amakondwerera munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima.”
11
Yesu adatinso, “Munthu wina adaali ndi ana aamuna aŵiri.
12
Wamng'ono adapempha bambo wake kuti, ‘Atate, bwanji mugaŵiretu tsopano chuma chanu, ine mundipatsiretu chigawo changa.’ Bamboyo adaŵagaŵiradi ana ake aja chuma chake.
13
Patangopita masiku oŵerengeka wamng'ono uja adagulitsa chigawo chake chonse, nachoka kwaoko ndi ndalama zake kupita ku dziko lakutali. Kumeneko adamwaza chuma chakecho ndi mayendedwe oipa.
14
Chitamthera chuma chake chonse, mudaloŵa njala yaikulu m'dziko limeneli, mwakuti iye yemwe adayamba kusauka.
15
Pamenepo adapita kukakhala nao kwa nzika ina ya m'dzikomo. Nzikayo idamtuma ku busa kukaŵeta nkhumba zake.
16
Mnyamata uja ankalakalaka kudya makoko amene nkhumba zinkadya, koma panalibe munthu wompatsako ngakhale makokowo.
17
“Atakhalakhala adadzidzimuka mumtima mwake, ndipo adati, ‘Achulukirenji antchito a bambo wanga amene ali ndi chakudya chokwanira mpaka kutsalako, pamene ine kuno ndikufa ndi njala.
18
Basi ndinyamuka, ndipita kwa bambo wanga, ndipo ndikanena kuti: Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe.
19
Sindili woyenera kutchedwanso mwana wanu. Mundilole ndisanduke mmodzi mwa antchito anu.’
20
“Choncho adanyamukadi napita kwa bambo wake. Koma akubwera patali, bambo wake adamuwona, namumvera chisoni. Adamthamangira, namkumbatira, nkumamumpsompsona.
21
Mwanayo adati, ‘Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kuchedwanso mwana wanu.’
22
Koma bambo wake adauza antchito ake kuti, ‘Thamangani mukatenge mkanjo wabwino kwambiri, mumuveke. Mumuvekenso mphete ku chala, ndi nsapato ku mapazi.
23
Ndipo katengeni mwanawang'ombe wonenepa uja, muphe kuti tidye, tikondwere.
24
Chifukwa mwana wangayu adaafa, koma tsopano wakhalanso moyo; adaatayika, koma tsopano wapezeka.’ Ndiye pompo chikondwerero chidayamba.
25
“Koma mwana wake wamkulu uja anali ku munda. Pochokera kumundako, atafika pafupi ndi nyumba, adamva anthu akuimba ndi kuvina.
26
Adaitana wantchito mmodzi namufunsa kuti, ‘Kodi kwagwanji?’
27
Iye adati, ‘Mng'ono wanu uja wabwera, ndiye bambo apha mwanawang'ombe wonenepa uja chifukwa amlandira ali wamoyo.’
28
Atamva zimenezo mwana wamkuluyo adapsa mtima, nakana kuloŵa. Apo bambo wake adatuluka, nkumupempha mopemba kuti aloŵe.
29
Koma iye adayankha bambo akewo kuti, ‘Ine zaka zonsezi ndakhala ndikukugwirirani ntchito ndipo sindidalakwirepo lamulo lanu. Komabe inu simudandipatsepo ndi katonde komwe kuti ndikondwere pamodzi ndi anzanga.
30
Koma mwana wanuyu, chuma chanu chonse adaonongera akazi achiwerewere, ndipo pamene wabwera, mwamuphera mwanawang'ombe wonenepa uja!’
31
“Bambo wakeyo adamuyankha kuti, ‘Mwana wanga, iwe uli ndi ine nthaŵi zonse, ndipo zanga zonse nzako.
32
Kunayenera kuti tikondwere ndi kusangalala, chifukwa mng'ono wakoyu adaafa, koma tsopano wakhalanso moyo; adaatayika, koma tsopano wapezeka.’ ”
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24