bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 19
Luke 19
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 20 →
1
Yesu adaloŵa m'Yeriko, ulendo wake wobzola mzindawo.
2
Kudafika munthu wina, dzina lake Zakeyo. Iyeyo anali mkulu wa okhometsa msonkho, ndipo anali wolemera.
3
Ankafunitsitsa kuwona Yesu kuti ngwotani. Koma pakuti Zakeyoyo anali wamfupi, adalephera kumuwona chifukwa cha kuchuluka kwa anthu.
4
Tsono adathamangira kutsogolo, nakakwera mu mkuyu kuti amuwone, chifukwa Yesu ankayenera kudzera pamenepo.
5
Ndiye pamene Yesu adafika pamalopo, adayang'ana m'mwamba, namuuza kuti, “Zakeyo, fulumira, tsika, chifukwa lero ndikuyenera kukakhala nao kunyumba kwako.”
6
Pompo Zakeyo adafulumira, natsika, kenaka nkukamlandiradi Yesu mokondwa kwambiri.
7
Poona zimenezi, anthu onse adayamba kung'ung'udza. Adati, “Wakakhala kunyumba kwa munthu wochimwa.”
8
Koma Zakeyo adaimirira nauza Ambuye kuti, “Ambuye, ndithudi ndidzapereka hafu la chuma changa kwa amphaŵi. Ndipo ngati ndidalandira kanthu kwa munthu aliyense monyenga, ndidzamubwezera kanai.”
9
Apo Yesu adamuuza kuti, “Chipulumutso chafika m'banja lino lero, popeza kuti ameneyunso ndi mwana wa Abrahamu.
10
Pajatu Mwana wa Munthu adabwera kudzafunafuna ndi kudzapulumutsa amene adatayika.”
11
Anthu ankamva zimene Yesu ankalankhula. Tsono adaŵaphera fanizo, popeza kuti anali pafupi ndi Yerusalemu, ndipo anthuwo ankaganiza kuti Mulungu akhazikitsa ufumu wake posachedwa.
12
Adati, “Munthu wina, wa fuko lomveka, adapita ku dziko lakutali kukalandira ufumu kuti pambuyo pake abwerenso kwao.
13
Adaitana khumi mwa antchito ake naŵapatsa ndalama zasiliva khumi, aliyense yakeyake. Adaŵauza kuti, ‘Bachita nazoni malonda mpaka nditabwera.’
14
Koma anthu ake ankadana naye, choncho m'mbuyo muno adatuma nthumwi kuti zipite ku dziko lomwelo nkukanena kuti, ‘Ife sitikufuna konse kuti munthu ameneyu akhale mfumu yathu.’
15
“Komabe iye adalandira ufumu uja. Tsono atabwerera kwao, adaitanitsa antchito aja adaaŵapatsa ndalamaŵa kuti adziŵe zimene adapindula.
16
Woyamba adadza nati, ‘Ambuye, ndalama yanu ija idapindula ndalama makumi khumi.’
17
Mbuye wake adamuuza kuti, ‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zochepa kwambiri, udzalamulira midzi khumi.’
18
Wachiŵiri adadza nati, ‘Ambuye, ndalama yanu ija idapindula ndalama makumi asanu.’
19
Iyenso mbuye wake adamuuza kuti, ‘Iwe udzalamulira midzi isanu.’
20
Koma wina adadza nati, ‘Ambuye, nayi ndalama yanu ija. Ndidaaimanga pa kansalu.
21
Ndinkakuwopani, popeza kuti ndinu munthu wankhwidzi. Mumalonjerera zimene simudaikize, ndiponso mumakolola zimene simudabzale.’
22
Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa, ndikutsutsa ndi mau ako omwe. Kani unkadziŵa kuti ndine munthu wankhwidzi, amene ndimalonjerera zimene sindidaikize, ndipo ndimakolola zimene sindidabzale.
23
Nanga bwanji osaiika ku banki ndalama yangayo, kuti ine pobwera ndiilandire pamodzi ndi chiwongoladzanja chake?’
24
Atatero adauza anthu amene anali pomwepo kuti, ‘Mlandeni ndalamayi muipereke kwa amene ali ndi ndalama makumi khumiyo.’
25
“Iwo adamuyankha kuti, ‘Pepani, ambuye, ameneyu ali kale ndi ndalama makumi khumi.’
26
Koma iye adati, ‘Ndikunenetsa kuti aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina. Koma amene alibe, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe.
27
Koma adani angaŵa, aja ankakana kuti ndikhale mfumu yaoŵa, bwera nawoni kuno, muŵaphe ine ndikuwona.’ ”
28
Yesu atanena zimenezi, adatsogolera ophunzira ake kupita ku Yerusalemu.
29
Atafika pafupi ndi midzi ya Betefage ndi Betaniya, pafupi ndi phiri lotchedwa Phiri la Olivi, adatuma ophunzira aŵiri,
30
naŵauza kuti, “Pitani m'mudzi mukuwonawo. Mukakangoloŵamo mukapeza mwanawabulu ali chimangire, amene munthu sanakwerepo chikhalire. Mukammasule, nkubwera naye kuno.
31
Wina akakakufunsani kuti, ‘Mukummasuliranji?’ Mukati, ‘Ambuye ali naye ntchito.’ ”
32
Aŵiriwo adapita, nakapezadi monga momwe Yesu adaaŵauzira.
33
Pamene ankamasula mwanawabuluyo, eniake adaŵafunsa kuti, “Mukummasuliranji mwanawabuluyu?”
34
Iwo adati, “Ambuye ali naye ntchito.”
35
Tsono adapita naye kwa Yesu, nayamba kuyala zovala zao pa buluyo, nakwezapo Yesu.
36
Pamene Yesu ankapita, anthu adamchitira ulemu pakuyala zovala zao mu mseu.
37
Pamene ankayandikira Yerusalemu, pa matsitso a Phiri la Olivi, gulu lonse la omutsatira aja lidayamba kukondwerera. Adakweza mau, natamanda Mulungu chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu zimene iwo adaziwona.
38
Adati, “Ndi yodala Mfumu imene ilikudza m'dzina la Ambuye. Mtendere Kumwamba, ulemu kwa Mulungu kumwambamwamba.”
39
Apo Afarisi ena amene adaali m'khamumo adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, auzeni ophunzira anuŵa aleke zimenezi.”
40
Iye adati, “Ndikutitu iwoŵa akangokhala chete, ifuula ndi miyalayi.”
41
Yesu atayandikira, nkuwona Yerusalemu, adalira chifukwa cha mzindawo.
42
Adati, “Ha, iwenso ukadangodziŵa lero lino zinthu zopatsa mtendere! Koma ai, tsopano maso ako sangathe kuziwona.
43
Nthaŵi idzakufikira pamene adani ako adzakuzinga ndi machemba, nadzakuzungulira, nkukutsekereza ponseponse.
44
Adzakusakaziratu iweyo pamodzi ndi anthu ako onse. Sadzasiya mwa iwe mwala pamwamba pa unzake, chifukwa chakuti sudazindikire nthaŵi imene Mulungu adaati adzakupulumutse.”
45
Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nayamba kutulutsa anthu amene ankachita malonda m'menemo.
46
Adaŵauza kuti, “Malembo akuti, ‘Nyumba yanga idzakhala nyumba yopemphereramo.’ Koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba.”
47
Yesu ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu tsiku ndi tsiku. Akulu a ansembe, aphunzitsi a Malamulo ndiponso akulu a Ayuda ankafuna kumupha,
48
koma adaasoŵa chochita, chifukwa anthu onse ankatengeka nawo mtima mau ake.
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
Recommended Reading
Commentary
Luke Commentaries
→
Devotional
Luke Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→