bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 20
Luke 20
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 21 →
1
Tsiku lina Yesu ankaphunzitsa anthu m'Nyumba ya Mulungu nkumalalika Uthenga Wabwino. Tsono akulu a ansembe, aphunzitsi a Malamulo ndiponso akulu a Ayuda adabwera
2
namufunsa kuti, “Mutiwuze, kodi mphamvu zoti muzichita zimenezi mudazitenga kuti? Kaya ndani adakupatsani mphamvu zimenezi?”
3
Yesu adati, “Nanenso ntakufunsani funso limodzi. Tandiwuzani,
4
kodi Yohane Mbatizi kuti azibatiza, mphamvu zake adaazitenga kwa yani, kwa Mulungu kapena kwa anthu?”
5
Iwo aja adayamba kukambirana nkumati, “Tikati adaazitenga kwa Mulungu, Iyeyu anena kuti, ‘Nanga bwanji tsono sumudamkhulupirire?’
6
Komanso tikati adaazitenga kwa anthu, anthu onseŵa atiponya miyala, chifukwa mumtima mwao amatsimikiza kuti Yohane adaali mneneri.”
7
Ndiye adangomuyankha kuti, “Kaya, ife sitikudziŵa kumene adaazitenga.”
8
Apo Yesu adati, “Nanenso tsono sindikuuzani kumene ndidazitenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi.”
9
Pamenepo Yesu adaphera anthu aja fanizo lina. Adati, “Munthu wina adaalima munda wamphesa. Adaubwereka alimi, iye nkunyamuka ulendo wa ku dziko lina, nakakhalako nthaŵi yaitali.
10
Nyengo yothyola zipatso itafika, munthu uja adatuma wantchito wake kwa alimi aja, kuti akampatsireko zipatso za m'munda muja. Koma alimiwo adammenya, nkumubweza osampatsa kanthu.
11
Adatumanso wantchito wina. Nayenso alimi aja adammenya, namchita chipongwe, nkumubweza osampatsa kanthu.
12
Adatumanso wachitatu, koma uyunso alimiwo adamuvulaza, namtaya kunja.
13
Pambuyo pake mwini munda uja adati, ‘Ndichite chiyani tsopano? Ndidzatuma mwana wanga amene ndimamkonda uja. Mwina mwake iye yekhayu akamchitira ulemu.’
14
Koma alimi aja atamuwona, adayamba kuuzana kuti, ‘Uyu ndiye amene adzamsiyire chumachi. Tiyeni timuphe kuti chidzakhale chathu.’
15
Tsono adamuponya kunja kwa mundawo, namupha. Kodi mwini munda wamphesa uja adzaŵatani alimi aja?
16
Ndithu adzabwera naŵapha alimiwo, munda uja nkuubwereka ena.” Anthu aja atamva zimenezi adati, “Ai, msatero.”
17
Koma Yesu adaŵayang'ana nati, “Nanga tsono tanthauzo lake nchiyani Malembo aŵa akuti, “ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba adaaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya, wofunika koposa?’
18
Aliyense wogwera pa mwala umenewo adzathyokathyoka. Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwere, udzangomutswanyiratu.”
19
Aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a ansembe adaadziŵa kuti fanizolo Yesu ankaphera iwowo. Nchifukwa chake ankafuna kumugwira nthaŵi yomweyo, koma ankaopa anthu.
20
Tsono iwo ankangomuŵenda, choncho adatuma anthu omuzonda, odziwonetsa ngati anthu olungama, kuti akamutape m'kamwa. Ankafuna kukamneneza kwa bwanamkubwa, pakuti iyeyo ndiye anali ndi mphamvu ndi ulamuliro wonse.
21
Ozondawo adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti Inu mumalankhula ndi kuphunzitsa molungama, simuyang'anira kuti uyu ndani. Mumaphunzitsa malamulo a Mulungu moona.
22
Kodi Malamulo a Mulungu amatilola kuti tizikhoma msonkho kwa Mfumu ya ku Roma, kapena ai?”
23
Koma Yesu podziŵa maganizo ao andale adati,
24
“Tandiwonetsani ndalama. Kodi ili ndi nkhope ya yani, ndipo ili ndi dzina la yani?”
25
Iwo aja adati, “Zonse ndi za Mfumu ya ku Roma.” Apo Yesu adaŵauza kuti, “Tsono perekani kwa Mfumu zake za Mfumu, ndiponso kwa Mulungu zake za Mulungu.”
26
Choncho adalephera kumutapa m'kamwa pamaso pa anthu pa zimene Iye adalankhula. Iwo adathedwa nzeru ndi zimene Yesu adaayankha, nkungoti chete.
27
Asaduki ena adadza kwa Yesu. Paja iwo amati akufa sadzauka. Adamufunsa Yesu kuti,
28
“Aphunzitsi, Mose adatilembera lamulo lakuti, ‘Ngati munthu amwalira, nasiya mkazi wake, koma opanda ana, mbale wake wa womwalirayo aloŵe chokolo, kuti amuberekere ana mbale wake uja.’
29
Tsono padaali anthu asanu ndi aŵiri pachibale pao. Woyamba adaakwatira mkazi, koma adamwalira osamsiyira mwana.
30
Chimodzimodzinso wachiŵiri,
31
ndipo wachitatu nayenso adaloŵa chokolo. Onse aja asanu ndi aŵiri adachita chimodzimodzi, koma onse adamwalira osamsiyira ana mkaziyo.
32
Potsiriza pake mai uja nayenso adamwalira.
33
Nanga tsono pa tsiku lodzauka akufa, mwini mkaziyo adzakhala utiwuti, popeza kuti abale asanu ndi aŵiri onse aja adaamkwatirapo?”
34
Yesu adaŵayankha kuti, “Anthu okhala pansi pano amakwatira ndi kukwatiwa.
35
Koma amene amaŵayesa oyenera kukakhala ndi moyo kutsogoloko, anthu atauka kwa akufa, sadzakwatiranso kapena kukwatiwa ai.
36
Iwo adzakhala ngati angelo, mwakuti sangafenso ai. Iwo ndi ana a Mulungu popeza kuti Iye adaŵaukitsa kwa akufa.
37
Koma zakuti anthu adzauka kwa akufa, Mose yemwe adaanenapo kale. Paja pa mbiri ija ya chitsamba choyaka moto, iye akuŵatchula Ambuye kuti, ‘Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobe.’
38
Ndiye kutitu sali Mulungu wa anthu akufa ai, koma wa anthu amoyo, chifukwa kwa Iye anthu onsewo ndi amoyo.”
39
Apo ena mwa aphunzitsi a Malamulo adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, mwanena bwino.”
40
Adaatero popeza kuti Asaduki aja sadalimbenso mtima kuti amufunse mafunso ena.
41
Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi inu, bwanji amati Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndi mwana wa Davide?
42
Paja Davide yemwe m'buku la Masalimo akuti, “ ‘Chauta adauza Mbuye wanga kuti: Khala ku dzanja langa lamanja
43
mpaka nditasandutsa adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.’
44
“Davide akutchula Mpulumutsi wolonjezedwa uja kuti Mbuye wake. Tsono angakhale mwana wakenso bwanji?”
45
Pamene anthu onse ankamvetsera zimene Yesu ankalankhula, Iye adauza ophunzira ake kuti,
46
“Chenjera nawoni aphunzitsi a Malamulo. Amakonda kuyenda atavala mikanjo yaitali, ndi kuti anthu aziŵalonjera mwaulemu pa misika. Amakonda mipando yaulemu kwambiri m'nyumba zamapemphero ndiponso malo olemekezeka pa maphwando.
47
Koma amaŵadyera chuma chao azimai amasiye, nkumapemphera mapemphero ataliatali monyengezera. Anthu ameneŵa adzalangidwa koposa.”
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
Recommended Reading
Commentary
Luke Commentaries
→
Devotional
Luke Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→