bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 4
Luke 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 5 →
1
Yesu, ali wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, adabwerako ku mtsinje wa Yordani kuja. Mzimu Woyerayo ankamutsogolera m'chipululu
2
masiku makumi anai, ndipo kumeneko Satana ankamuyesa. Yesu sankadya kanthu masiku amenewo, ndipo pamene masikuwo adatha, adamva njala.
3
Tsono Satana adamuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, lamulani mwala uli apawu kuti usanduke chakudya.”
4
Koma Yesu adati, “Malembo akuti, ‘Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha.’ ”
5
Pambuyo pake Satana adatenga Yesu kupita naye pa malo okwera, ndipo pa kamphindi kakang'ono adamuwonetsa maiko a mafumu onse a pansi pano.
6
Tsono adamuuza kuti, “Ndidzakupatsani ulamuliro ndi ulemerero wonsewu, chifukwa zidapatsidwa kwa ine, ndipo ndimazipatsa aliyense amene ndifuna.
7
Choncho mukandipembedza, zonsezi zidzakhala zanu.”
8
Apo Yesu adati, “Malembo akuti, ‘Uzipembedza Ambuye Mulungu wako, ndipo uziŵatumikira Iwo okha.’ ”
9
Potsiriza Satana adatenga Yesu kupita naye ku Yerusalemu, nakamuimika pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. Adamuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, mudziponye pansi.
10
Paja Malembo akuti, “ ‘Mulungu adzalamula angelo ake kuti akusamaleni.’ Ndiponso,
11
“ ‘Iwo adzakunyamulani m'manja mwao, kuti mapazi anu angapweteke pa miyala.’ ”
12
Koma Yesu adati, “Malembo akuti, ‘Usaŵayese Ambuye, Mulungu wako.’ ”
13
Tsono Satana atatha kumuyesa mwa zonsezi, adalekana naye, kudikira nthaŵi ina.
14
Yesu adabwereranso ku Galileya ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Mbiri yake idawanda kuzungulira dziko lonselo.
15
Ankaphunzitsa m'nyumba zao zamapemphero, ndipo anthu onse ankamutamanda.
16
Nthaŵi ina Yesu adafika ku Nazarete kumene adaaleredwa. Ndipo pa tsiku la Sabata adaloŵa m'nyumba yamapemphero, monga adaazoloŵera, naimirira kuti aŵerenge mau.
17
Adampatsa buku la mneneri Yesaya. Tsono Iye adafutukula bukulo, napeza pamene padalembedwa kuti,
18
“Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa,
19
ndi kukalalika za nthaŵi imene Ambuye adzapulumutsa anthu ao.”
20
Yesu adatseka bukulo nkulipereka kwa mtumiki wa nyumba yamapemphero, nakhala pansi. Anthu onse amene adaasonkhana m'nyumbamo ankangomupenyetsetsa.
21
Tsono Yesu adaŵauza kuti, “Lero zachitikadi zimene adaaneneratu Malembo amene mwamvaŵa.”
22
Anthu onse adamtamanda, nkumadabwa ndi mau ogwira mtima amene Iye ankalankhula. Anthuwo ankati, “Kodi uyu si mwana uja wa Yosefeyu?”
23
Apo Yesu adaŵauza kuti, “Ndithudi mudzandiwuza mwambi uja wakuti, ‘Iwe sing'anga, dzichiritse wekha.’ Mudzatinso, ‘Tidamva zimene mudachita ku Kapernao, tsono muchitenso zomwezo kwanu kuno.’ ”
24
Adaŵauzanso kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti palibe mneneri amene amalandiridwa bwino kumudzi kwao.
25
Kunena zoona, paja panali azimai amasiye ambiri pakati pa Aisraele pa nthaŵi ya mneneri Eliya, pamene mvula siidagwe zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, kotero kuti munali njala yaikulu m'dziko lonse.
26
Eliya sadatumidwe ndi kwa mmodzi yemwetu mwa iwo aja, koma adatumidwa kwa mai wamasiye wa ku mudzi wa Sarepta, m'dziko la Sidoni.
27
Panalinso akhate ambiri pakati pa Aisraele nthaŵi ya mneneri Elisa, komabe panalibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo aja amene adachiritsidwa. Amene adachiritsidwa ndi Namani yekha wa ku dziko la Siriya.”
28
Anthu onse amene anali m'nyumba yamapemphero muja atamva mau ameneŵa, adapsa mtima kwambiri.
29
Adaimirira namtulutsira kunja kwa mudzi, nkupita naye pamwamba pa phiri pamene adaamangapo mudzi wao. Adaati akamponye kunsi,
30
koma Iye adangodzadutsa pakati pao, nkumapita.
31
Yesu adapita ku Kapernao, mudzi wina wa ku Galileya, nkumaphunzitsa pa tsiku la Sabata.
32
Zophunzitsa zake anthu zidaaŵagwira mtima kwambiri, chifukwa ankalankhula moonetsa ulamuliro ngati mwiniwake.
33
M'nyumba yamapempheroyo munali munthu wogwidwa ndi mzimu womuipitsa. Adalankhula mokuwa kuti,
34
“Aah, kodi takuputani chiyani, Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadzatiwononga? Ndakudziŵani, ndinu Woyera uja wa Mulungu.”
35
Koma Yesu adazazira mzimu woipawo, adati, “Khala chete, tuluka mwa munthuyu.” Apo mzimu womuipitsa uja udamugwetsa pansi munthuyo pakati pa anthu, nkutuluka, osamupweteka konse.
36
Anthu onse aja adazizwa, mpaka kumafunsana kuti, “Mau ameneŵa ngotani? Ngakhale mizimu yoipitsa anthu yomwe akuilamula ndi mphamvu ndi ulamuliro, ndipo ikutulukadi.”
37
Motero mbiri ya Yesu idawanda ku dera lonselo.
38
Yesu adanyamuka nachoka ku nyumba yamapemphero kuja, nakaloŵa m'nyumba ya Simoni. Apongozi a Simoni ankadwala malungo aakulu, ndipo anthu adapempha Yesu kuti achitepo kanthu.
39
Yesu adaŵeramira pa iye, nazazira malungowo, ndipo malungo aja adatha. Pomwepo amai aja adadzuka nayamba kukonzera anthu chakudya.
40
Dzuŵa likuloŵa, anthu onse amene anali ndi anzao odwala nthenda zosiyanasiyana, adabwera nawo kwa Yesu. Iye adasanjika manja pa wodwala aliyense, naŵachiritsa onse.
41
Nayonso mizimu yoipa inkatuluka mwa anthu ambiri ikufuula nkumanena kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.” Koma Iye adaidzudzula, osailola kuti ilankhule, chifukwa idaadziŵa kuti analidi Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
42
Kutacha, Yesu adachoka ku Kapernao kuja napita ku malo kosapitapita anthu. Makamu a anthu adayamba kumufunafuna, ndipo atampeza, adayesa kumletsa kuti asaŵasiye.
43
Koma Iye adaŵauza kuti, “Ndiyenera kukalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu ku midzi inanso, pakuti ndizo zimene Mulungu adanditumira.”
44
Motero Iye ankalalika m'nyumba zamapemphero za ku Yudeya.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24