bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 23
Luke 23
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 24 →
1
Gulu lonse lija lidanyamuka nkupita naye Yesu kwa Pilato.
2
Iwo adayamba kuneneza Yesu kuti, “Munthu uyu tidampeza akusokeza anthu a mtundu wathu. Amatiletsa kuti tisamakhome msonkho kwa Mfumu ya ku Roma. Amanenanso kuti ati Iyeyu ndi Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndiponso mfumu.”
3
Pilato adafunsa Yesu kuti, “Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu adati, “Mwanena nokha.”
4
Pamenepo Pilato adauza akulu a ansembe ndi anthu onse aja kuti, “Sindikumpeza mlandu munthuyu.”
5
Koma iwo adaumirira nati, “Ameneyu amautsa mitima ya anthu ndi zimene amaphunzitsa m'dziko lonse la Yudeya. Adayambira ku Galileya, mpaka konse kuno.”
6
Pamene Pilato adamva zimenezi, adaŵafunsa kuti, “Kodi munthuyu ndi wa ku Galileya?”
7
Tsono atamva kuti ngwochokeradi ku dera limene Herode amalamulira, adamtumiza kwa Herodeyo, amene nayenso anali m'Yerusalemu masiku omwewo.
8
Herode poona Yesu, adakondwa kwambiri, chifukwa ankamva za Iye, mwakuti kwa nthaŵi yaitali ankafuna atamuwona. Ankayembekeza kuti aone Yesu akuchita chozizwitsa china.
9
Herode adamufunsa mafunso ambiri, koma Yesu sadamuyankhe kanthu.
10
Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adaimirira pomwepo nkumaneneza Yesu kwambiri.
11
Herode pamodzi ndi asilikali ake adayamba kumseka Yesu ndi kumamnyoza. Adamuveka chovala chachifumu, namubwezera kwa Pilato.
12
Tsiku lomwelo Herode ndi Pilato adayamba kuyanjana, chonsecho kale ankadana.
13
Pilato adasonkhanitsa akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda ndi anthu wamba.
14
Adaŵauza kuti, “Mwadzampereka munthuyu kwa ine kuti ndi munthu wosokeza anthu. Ndipo onani, ine ndamufunsa pamaso panu, koma sindikumpeza mlandu pa zonse zimene mukumnenezazi.
15
Herode yemwe sadampeze mlandu, nchifukwa chake wamubweza kwa ife. Ameneyu sadachite kanthu koyenera kumuphera.
16
Motero ndingomukwapula kenaka nkumumasula.” [
17
Pilatoyo ankayenera kuŵamasulira mkaidi mmodzi pa nthaŵi ya chikondwerero cha Paska.]
18
Koma anthu onse aja adayamba kufuula pamodzi kuti, “Mchotseni ameneyu, mutimasulire Barabasi.”
19
Barabasi anali atamponya m'ndende chifukwa cha kuyambitsa chipolowe mu mzinda, ndiponso kupha munthu.
20
Pilato adafuna kumasula Yesu, motero adakakamba nawonso anthu aja.
21
Koma iwo adafuulirafuulira kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!”
22
Pilato adaŵafunsa kachitatu kuti, “Koma wachimwanji Iyeyu? Sindikumpeza mlandu woyenera kumuphera. Motero ndingomukwapula kenaka ndimmasula.”
23
Koma iwo adamuumiriza mokweza mau kuti Yesu apachikidwe, kufuula kwao kunkakulirakulira.
24
Tsono Pilato adagamula kuti zimene anthu aja ankapempha zichitike.
25
Adaŵamasulira munthu amene ankamupempha uja, amene adaaponyedwa m'ndende chifukwa cha chipolowe ndi kupha munthu. Koma Yesu adampereka kwa iwo kuti akamchite zimene ankafuna.
26
Asilikali adamtenga Yesu napita naye kuti akampachike. Pa njira adagwira munthu wina wa ku Kirene, dzina lake Simoni. Iye ankachokera ku midzi. Adamsenzetsa mtanda wa Yesu kuti aunyamule, azitsatira pambuyo pa Yesuyo.
27
Anthu ambirimbiri ankamutsatira. Pakati pao panalinso akazi amene ankadzigunda pa chifuwa ndi chisoni nkumalira chifukwa cha Iye.
28
Koma Yesu adaŵacheukira naŵauza kuti, “Inu azimai a ku Yerusalemu, musandilire Ine ai, koma mulire chifukwa cha inu nomwe ndi ana anu.
29
Pakuti masiku akubwera pamene anthu azidzati, ‘Ngodala azimai ouma, azimai osabala, azimai amene sadayamwitseko mwana.’
30
Nthaŵi imeneyo adzapempha mapiri kuti, ‘Tigwereni,’ ndiponso magomo kuti, ‘Tiphimbeni.’
31
Pakuti ngati mtengo wauŵisi auchita zimenezi, nanga mtengo wouma ndiye adzauchita zotani?”
32
Asilikali aja adaatenganso anthu ena aŵiri, amene anali zigaŵenga, kuti akaphedwe pamodzi ndi Yesu.
33
Pamene adafika ku malo otchedwa Chibade cha Mutu, adapachika Yesu komweko pa mtanda. Komwekonso adapachika zigaŵenga zija, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere.
34
Yesu adati, “Atate, muŵakhululukire anthuŵa, chifukwa sakudziŵa zimene akuchita.” Iwo aja adagaŵana zovala zake pakuchita maere.
35
Anthu ena onse adaimirira pomwepo nkumaonerera. Komanso akulu a Ayuda ankamunyodola nkumanena kuti, “Adapulumutsa ena, adzipulumutse yekha ngati ndiyedi Mpulumutsi uja amene Mulungu adamsankha.”
36
Nawonso asilikali adayamba kumseka. Adadza pafupi ndi Iye, nampatsa vinyo wosasa kuti amwe.
37
Adati, “Ngati ndiwedi mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.”
38
Pamwamba pa mtanda panali kalata yolembedwa m'Chigriki, m'Chilatini, ndi m'Chiyuda. Mau ake anali akuti, “Uyu ndi mfumu ya Ayuda.”
39
Chigaŵenga chimodzi chimene chidaapachikidwa nao, chidayamba kunyoza Yesu nkumanena kuti, “Ha! Kodi iwe sindiwe Mpulumutsi Wolonjezedwa uja? Udzipulumutse wekha ndi ife tomwe.”
40
Koma mnzake uja adamdzudzula, adati, “Kodi iwe, suwopa ndi Mulungu yemwe, chidziŵirecho kuti nawenso ukulandira chilango chomwechi?
41
Tsonotu ife zikutiyeneradi zimenezi, tikulandira zolingana ndi zimene tidachita. Koma aŵa sadachite cholakwa chilichonse.”
42
Ndipo adati, “Inu, mukandikumbikire mukakafika mu Ufumu wanu.”
43
Yesu adamuyankha kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino ukhala nane ku Malo a Chisangalalo, Kumwamba.”
44
Nthaŵi itakwana ngati 12 koloko masana, padaagwa mdima pa dziko lonse mpaka pa 3 koloko,
45
dzuŵa litangoti bii kuda. Pamenepo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati.
46
Tsono Yesu adanena mokweza mau kuti, “Atate ndikupereka mzimu wanga m'manja mwanu.” Atanena zimenezi, adatsirizika.
47
Mkulu wa asilikali ataona zimene zidaachitikazo, adatamanda Mulungu, adati, “Ndithudi munthuyu adaalidi wosalakwa konse.”
48
Anthu onse amene adaasonkhana kudzaonerera zimene zinkachitikazo, ataona zonsezi, adabwerera kwao akudzigunda pa chifuwa ndi chisoni.
49
Anthu onse amene ankadziŵana ndi Yesu, ndiponso azimai amene adaamtsatira kuchokera ku Galileya, adaima patali nkumaona zimenezi.
50
Panali munthu wina, dzina lake Yosefe, wa ku Arimatea, mudzi wina wa Ayuda. Anali munthu wabwino ndi wolungama, ndipo anali wa m'Bungwe Lalikulu la Ayuda.
51
Komatu sankavomereza zimene anzake a m'Bungweli ankapangana, iye ankayembekeza kudza kwa Ufumu wa Mulungu.
52
Iyeyu adapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu.
53
Tsono adautsitsa naukulunga m'nsalu yoyera yabafuta, nkuuika m'manda. Mandawo anali asanaikemo munthu wina aliyense.
54
Linali tsiku la chikonzero, tsiku la Sabata likuti liziyamba kumene.
55
Azimai aja amene adaabwera ndi Yesu kuchokera ku Galileya, adatsatira Yosefe, naona manda ndi m'mene adaaikira mtembo wa Yesu.
56
Kenaka adabwerera nakayamba kukonza zonunkhira ndiponso mafuta abwino. Tsono pa tsiku la Sabata adapumula malinga ndi Malamulo a Mose.
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 24 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
Recommended Reading
Commentary
Luke Commentaries
→
Devotional
Luke Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→