bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 21
Luke 21
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 22 →
1
Yesu atakweza maso, adaona anthu olemera akuponya zopereka zao m'bokosi la ndalama m'Nyumba ya Mulungu.
2
Adaonanso mai wina wamasiye akuponyamo tindalama tiŵiri.
3
Pamenepo Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti mai wamasiye wosaukayu waponyamo koposa ena onseŵa.
4
Chifukwa ena onseŵa angoponyamo zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma maiyu, mwa umphaŵi wake, waponyamo zonse zimene anali nazo, ngakhale zimene akadagulira chakudya.”
5
Anthu ena ankalankhula za Nyumba ya Mulungu kuti adaikongoletsa ndi miyala yokoma, ndiponso ndi mitulo yopereka kwa Mulungu. Yesu adati,
6
“Kunena za zinthu mukuziwonazi, masiku adzabwera mwakuti sipadzatsala konse mwala ndi umodzi womwe pamwamba pa mwala unzake: yonse adzaigumula.”
7
Anthu aja adafunsa Yesu kuti, “Aphunzitsi, zimenezi zidzachitika liti? Tidzaonera chiyani kuti zonsezi zili pafupi kuchitika?”
8
Yesu adati, “Chenjerani kuti anthu angakusokezeni. Chifukwa kudzafika anthu ambiri m'dzina langa namadzanena kuti, ‘Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndine.’ Azidzatinso, ‘Nthaŵi yayandikira.’ Amenewo musadzaŵatsate.
9
Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi za zipoloŵe, musadzachite mantha. Zimenezi zidzayenera kuyamba zaoneka, koma sindiye kuti chimalizo chifika nthaŵi yomweyo.”
10
Yesu adaŵauzanso kuti, “Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo.
11
Kudzachita zivomezi zazikulu. Kudzakhala njala ndi mliri ku malo osiyanasiyana. Kudzakhalanso zoopsa ndi zizindikiro zodabwitsa mu mlengalenga.
12
“Koma zisanachitike zonsezi, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzapita nanu ku milandu ku nyumba zamapemphero, nadzakuponyani m'ndende. Adzakuperekani kwa mafumu ndi kwa akulu ena a Boma chifukwa chotsatira Ine.
13
Umenewu udzakhala mpata wanu wondichitira umboni.
14
Tsono mudziŵiretu kuti musadzachite kukonzekera mau oti mudzaŵayankhe pamlandupo.
15
Ineyo ndidzakupatsani mau ndi nzeru zimene adani anuwo sadzatha konse kuzikana kapena kuzitsutsa.
16
Makolo anu omwe, abale anu, anansi anu, ndi abwenzi anu, amenewo adzakuperekani kwa adani anu, ndipo ena mwa inu mudzaphedwa.
17
Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha Ine.
18
Koma silidzatayikapo tsitsi lanu ndi limodzi lomwe.
19
Mukadzalimbikira, ndiye mudzapate moyo wanu.”
20
“Pamene mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, dziŵani kuti chiwonongeko chake chafika.
21
Pamenepo amene ali m'Yudeya athaŵire ku mapiri, amene ali mumzinda atulukemo, ndipo amene ali ku minda asadzaloŵenso mumzindamo.
22
Chifukwa masiku amenewo adzakhala masiku akulipsira, kuti zonse zija zimene zidaalembedwa m'Malembo zipherezere.
23
Ali ndi tsoka azimai amene adzakhale ndi pathupi, ndiponso azimai oyamwitsa ana masiku amenewo. Pakuti padzagwa masautso aakulu pa dziko lino, ndipo Mulungu adzaŵakwiyira Aisraeleŵa.
24
Adzaphedwa pa nkhondo yoopsa, nkutengedwa ngati akapolo a anthu a mitundu ina. Kenaka Yerusalemu akunja adzampondereza mpaka pa mapeto ake a nthaŵi ya akunjawo.” Dan. 9.26; Mika 3.12; Zak. 11.6.
25
“Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuŵa, pa mwezi ndi pa nyenyezi. Pansi pano anthu a mitundu yonse adzada nkhaŵa nkutha nzeru, pomva kukokoma kwa nyanja ndi mafunde ake.
26
Ena adzakomoka ndi mantha poyembekezera zimene zikudza pa dziko lonse lapansi, pakuti mphamvu zonse zakuthambo zidzagwedezeka.
27
Pamenepo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo, ali ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.
28
Zimenezi zikadzayamba kuchitika, mudzaimirire nkukweza mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chayandikira.”
29
Pambuyo pake Yesu adaŵaphera fanizo adati, “Yang'anani mkuyu ndi mitengo ina yonse.
30
Mukamaona kuti masamba akuphuka, mumadziŵa kuti chilimwe chayandikira kale.
31
Momwemonso, mukadzaona zija ndanenazi zikuchitika, mudzadziŵe kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi.
32
Ndithu ndikunenetsa kuti zonsezi zidzaoneka anthu a mbadwo unoŵa asanamwalire onse.
33
Thambo ndi dziko lapansi zidzatha, koma mau anga sadzatha mphamvu konse.”
34
“Chenjerani kuti mitima yanu ingapusitsidwe ndi maphwando, kuledzera, ndi kudera nkhaŵa za moyo uno, kuti tsikulo lingakufikireni modzidzimutsa.
35
Pajatu lidzaŵagwera ngati msampha anthu onse okhala pa dziko lonse lapansi.
36
Muzikhala maso tsono, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse, kuti mukhale ndi mphamvu zopulumukira ku zonsezi zimene ziti zidzachitike, ndiponso kuti mukaimirire pamaso pa Mwana wa Munthu.”
37
Masiku onse Yesu ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu, koma usiku ankatuluka kukakhala ku phiri lotchedwa Phiri la Olivi.
38
Tsono anthu onse ankalaŵirira m'mamaŵa kubwera kwa Iye ku Nyumba ya Mulungu kudzamva mau ake.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
Recommended Reading
Commentary
Luke Commentaries
→
Devotional
Luke Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→