bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 22
Luke 22
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 23 →
1
Nthaŵi yochitira chikondwerero cha buledi wosafufumitsa inkayandikira. Chikondwererocho chimatchedwa Paska.
2
Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo ankafunafuna njira yoti aphere Yesu. Paja iwo ankaopa anthu.
3
Tsono Satana adamuloŵa Yudasi wotchedwa Iskariote, amene anali mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja a Yesu.
4
Yudasiyo adapita kukapangana ndi akulu a ansembe ndi atsogoleri a alonda a ku Nyumba ya Mulungu za njira yoti aperekere Yesu kwa iwo.
5
Iwo adakondwa, nalonjeza kumpatsa ndalama.
6
Yudasi adavomera, nayamba kufunafuna mpata woti amuperekere kwa iwo, anthu onse osadziŵa.
7
Tsiku la buledi wosafufumitsa lidafika, ndiye kuti tsiku limene anthu ankapha mwanawankhosa wochitira phwando la Paska.
8
Yesu adatuma Petro ndi Yohane naŵauza kuti, “Pitani mukatikonzere phwando la Paska kuti tikadye.”
9
Koma iwo adamufunsa kuti, “Kodi tikakonzere kuti?”
10
Yesu adati, “Mvetsani! Mukangoloŵa m'mudzimu, mukumana ndi munthu wamwamuna atasenza mtsuko wa madzi. Mukamtsatire mpaka kunyumba kumene akaloŵe.
11
Mukauze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa kuti, kodi nchiti chipinda chimene Iwowo adzadyeremo phwando la Paska ndi ophunzira ao?’
12
Iyeyo akakuwonetsani chipinda chachikulu cham'mwamba, momwe akonzamo zonse zofunikira. M'menemo mukatikonzere chakudya.”
13
Tsono iwo adapita nakachipezadi monga momwe adaaŵauzira, ndipo adakonza phwando la Paska.
14
Nthaŵi itakwana, Yesu adakakhala podyera pamodzi ndi atumwi ake aja.
15
Tsono adaŵauza kuti, “Ndafunitsitsa kudya phwando ili la Paska pamodzi ndi inu ndisanayambe kumva zoŵaŵa.
16
Pakuti kunena zoona, sindidzadyanso konse Paska, mpaka Paskayi itadzafika pake penipeni mu Ufumu wa Mulungu.”
17
Atatero Yesu adatenga chikho, ndipo atathokoza Mulungu, adati, “Kwayani, imwani nonsenu.
18
Ndithu ndikunenetsa kuti kuyambira tsopano sindidzamwanso konse chakumwa cha mtengo wamphesa, mpaka Mulungu atadzakhazikitsa ufumu wake.”
19
Kenaka Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagawira ophunzira aja, ndipo adati, “Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.”
20
Atatha kudya, adaŵapatsanso chikho, nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chimene magazi anga, omwe akukhetsedwa chifukwa cha inu, akuchitsimikizira.
21
“Koma ndithudi wondipereka kwa adani akudya nane pamodzi pompano.
22
Mwana wa Munthu akukaphedwadi, monga momwe Mulungu adazikonzeratu kale. Komabe ali ndi tsoka munthu amene akukapereka Mwana wa Munthuyo.”
23
Apo onse adayamba kumafunsana kuti, “Kodi ndani mwa ife angachite zotere?”
24
Tsono ophunzira aja adayamba kutsutsana kuti, “Kodi mwa ife amati wamkulu ndani?”
25
Yesu adaŵauza kuti, “Pakati pa anthu akunja, mafumu amadyera anthu ao masuku pa mutu, ndipo amene amaŵaonetsa mphamvu zao, amatchedwa mfulu zopatsa.”
26
Koma pakati pa inu zisamatero ai. Kwenikweni wamkulu mwa inu azikhala ngati wamng'ono mwa onse, ndipo mtsogoleri azikhala ngati wotumikira.
27
Kodi wamkulu ndani? Ndi amene alikudya, kapena amene akumtumikira? Si amene alikudyayo nanga? Koma Ine ndili pakati panu ngati wotumukira.
28
“Inu ndinu amene mwakhala ndi Ine pa masautso anga onse.
29
Nchifukwa chake, monga Atate anga adandipatsa ufumu, Inenso ndikukupatsani ufumu.
30
Ndikadzaloŵa mu ufumu wanga, muzidzadya ndi kumwa pamodzi nane, ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu nkumaweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israele.”
31
“Simoni, Simoni, chenjera! Mulungu walola Satana kuti akupeteni nonse ngati tirigu.
32
Koma Ine ndakupempherera, kuti usaleke kundikhulupirira. Ndipo iweyo utatembenuka mtima, ukaŵalimbitse abale akoŵa.”
33
Apo Petro adati, “Ambuye, ndili wokonzeka kupita nanu ku ndende, ngakhale kufa kumene.”
34
Koma Yesu adamuyankha kuti, “Ndikukuuza, iwe Petro, kuti lero lomwe lino, tambala asanalire, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziŵa.”
35
Yesu adaŵafunsa kuti, “Nthaŵi ina ndidaakutumani opanda thumba la ndalama, kapena thumba lapaulendo, kapenanso nsapato. Kodi pamene paja mudaasoŵapo kanthu?” Iwo adati, “Iyai.”
36
Yesu adaŵauza kuti, “Koma tsopano amene ali ndi thumba la ndalama, asalisiye. Chimodzimodzinso thumba lake lapaulendo. Ndipo amene alibe lupanga, agulitse mwinjiro wake nkugula lupanga.
37
Ndithu ndikunenetsa kuti ziyenera kuchitikadi mwa Ine zimene Malembo adanena kuti, ‘Ankamuyesa mmodzi mwa anthu ophwanya malamulo.’ Ndipo zonse zimene zidalembedwa za Ine zikuchitikadi.”
38
Ophunzirawo adati, “Ambuye, aŵa malupanga, tili nawo kale aŵiri.” Yesu adaŵauza kuti, “Chabwino, basi.”
39
Pambuyo pake Yesu adatuluka mu mzinda napita ku Phiri la Olivi monga adaazoloŵera. Ndipo ophunzira ake adapita naye.
40
Pamene adafika kumeneko, Yesu adaŵauza kuti, “Pempherani, kuti mungagwe m'zokuyesani.”
41
Tsono adapatukana nawo kadera, kutalika kwake ngati pamene mwala ungafike munthu atauponya. Apo adagwada pansi nayamba kupemphera.
42
Adati, “Atate, ngati mukufuna, mundichotsere chikho chamasautsochi. Komabe muchite zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”
43
[Pamenepo mngelo wochokera Kumwamba adamuwonekera namlimbitsa mtima.
44
Koma Yesu adavutikabe koopsa mu mtima, nkumapemphera kolimba kuposa kale. Ndipo thukuta limene ankadza linali ngati madontho akuluakulu a magazi ogwera pansi.]
45
Atapemphera, adaimirira napita kwa ophunzira ake. Adaŵapeza ali m'tulo chifukwa cha chisoni,
46
ndipo adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukugona? Dzukani ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani.”
47
Yesu akulankhula choncho, padabwera khamu la anthu. Amene ankaŵatsogolera anali Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Iyeyu adadza pafupi ndi Yesu kuti amumpsompsone.
48
Koma Yesu adamufunsa kuti, “Yudasi, mongadi ukupereka Mwana wa Munthu kwa adani pakumumpsompsona?”
49
Ophunzira amene anali pafupi ndi Yesu ataona zimene zinalikudzachitika, adafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi tiŵateme ndi lupanga?”
50
Apo mmodzi mwa iwo adatemadi wantchito wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu la ku dzanja lamanja.
51
Koma Yesu adati, “Basi, lekani zimenezi.” Atatero adakhudza khutu la munthuyo namchiritsa.
52
Kenaka Yesu adalankhula nawo onse amene adaabwera kudzamugwira, akulu a ansembe ndi atsogoleri a alonda a ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso akulu a Ayuda. Adaŵafunsa kuti, “Bwanji mwachita kunditengera malupanga ndi zibonga ngati kuti ndine chigaŵenga?
53
Tsiku ndi tsiku ndidaali nanu m'Nyumba ya Mulungu, inuyo osandigwira. Koma ino ndi nthaŵi yanu ndiponso ya mphamvu za mdima.”
54
Anthu aja adamugwira Yesu, napita naye ku nyumba ya mkulu wa ansembe onse. Petro ankaŵatsatira chapatali.
55
Iwo adasonkha moto m'kati mwa bwalo la nyumbayo, nakhala pansi pamodzi. Petro nayenso adakakhala pakati pao.
56
Mtsikana wina wantchito adamuwona atakhala nao pamotopo. Adamuyang'anitsitsa, nati, “Aŵansotu anali naye.”
57
Koma Petro adakana, adati, “Mai iwe, sindimdziŵa ameneyu.”
58
Patapita kanthaŵi pang'ono, munthu wina pomuwona adati, “Akulu inu, ndinunso mmodzi mwa iwo aja.” Koma Petro adati, “Munthu iwe, ai ndithu sindine.”
59
Patapita ngati ora limodzi, munthu winanso adanenetsa kuti, “Ndithudi akulu aŵanso anali naye, pakuti ndi a ku Galileya.”
60
Koma Petro adati, “Munthu iwe, sindikuzidziŵa zimene ukunenazi.” Ndipo pompo, akulankhulabe, tambala adalira.
61
Ambuye adacheuka nayang'ana Petro. Pamenepo Petro adakumbukira mau aja amene Ambuye adaamuuza kuti, “Lero lomwe lino, tambala asanalire, ukhala utandikana katatu.”
62
Pamenepo adatuluka, nakalira kwambiri chifukwa cha chisoni chachikulu.
63
Tsono anthu amene ankalonda Yesu aja adayamba kumseka ndi kumammenya.
64
Adammanga nsalu m'maso nkumamufunsa kuti, “Lota, wakumenya ndani?”
65
Ndipo adamnenanso mau ena ambiri achipongwe.
66
Kutacha, a m'Bungwe Lalikulu la Ayuda adasonkhana, ndiye kuti akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Adatenga Yesu napita naye ku Bwalo lao.
67
Adamuuza kuti, “Ngati ndiwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, utiwuze mosabisa.” Koma Iye adaŵayankha kuti, “Ngakhale ntakuuzani, simungandikhulupirire konse,
68
ndipo nditakufunsani funso, inu simungaliyankhe.
69
Koma kuyambira tsopano Mwana wa Munthune ndidzakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvuzonse.”
70
Apo onse aja adati, “Tsono ndiye kutitu ndiwe Mwana wa Mulungu, ati?” Yesu adati, “Mwanena nokha kuti ndine amene.”
71
Pamenepo iwo aja adati, “Tikufuniranji umboni wina? Tadzimvera tokha mau akeŵa.”
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
Recommended Reading
Commentary
Luke Commentaries
→
Devotional
Luke Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→