bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 18
Luke 18
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 19 →
1
Yesu adaŵaphera fanizo pofuna kuŵaphunzitsa kuti azipemphera nthaŵi zonse, osataya mtima.
2
Adati, “M'mudzi mwina mudaali woweruza wina amene sankaopa Mulungu kapena kulabadako za munthu.
3
M'mudzi momwemo mudaalinso mai wamasiye. Iyeyu ankabwera kwa woweruza uja kudzampempha kuti, ‘Mundiweruzireko mlandu umene uli pakati pa ine ndi mdani wanga.’
4
Kwa nthaŵi yaitali woweruza uja ankakana, koma pambuyo pake adaganiza kuti, ‘Ngakhale sindiwopa Mulungu kapena kusamala munthu,
5
komabe chifukwa mai wamasiyeyu akundivuta, ndimuweruzira mlandu wake, kuwopa kuti angandilemetse nako kubwerabwera kwake.’ ”
6
Tsono Ambuye adati, “Mwamvatu mau a woweruza wosalungama uja.
7
Nanga Mulungu, angaleke kuŵaweruzira mlandu wao osankhidwa ake, amene amamdandaulira usana ndi usiku? Kodi adzangoŵalekerera?
8
Iyai, kunena zoona adzaŵaweruzira mlandu wao msanga. Komabe Mwana wa Munthu pobwera, kodi adzapezadi chikhulupiriro pansi pano?”
9
Yesu adaŵapheranso fanizo anthu ena amene ankadziyesa olungama nkumanyoza anzao.
10
Adati, “Anthu aŵiri adaapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera. Wina anali Mfarisi, wina anali wokhometsa msonkho.
11
Mfarisiyo adaimirira nayamba kupemphera motere mumtima mwake: ‘Mulungu, ndikukuyamikani kuti ine sindili monga anthu ena onse ai. Iwowo ndi anthu akuba, osalungama ndi adama. Sindilinso monga wokhometsa msonkho uyu ai.
12
Ine ndimasala zakudya kaŵiri pa mlungu, ndipo ndimapereka chachikhumi pa zonse zimene ndimapata.’
13
Koma wokhometsa msonkho uja adaima kutali, osafuna nkuyang'ana kumwamba komwe. Ankangodzigunda pa chifuwa ndi chisoni nkumanena kuti, ‘Mulungu, mundichitire chifundo ine wochimwane.’ ”
14
Yesu popitiriza mau adati, “Kunena zoona, wokhometsa msonkhoyu adabwerera kwao ali wolungama pamaso pa Mulungu, osati Mfarisi uja ai. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo wodzichepetsa, adzamkuza.”
15
Anthu ena ankabwera ndi ana omwe kwa Yesu kuti aŵakhudze. Ophunzira ake poona zimenezi, ankaŵazazira.
16
Koma Yesu adaŵaitana nati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere.
17
Ndithu ndikunenetsa kuti amene salandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, ameneyo sadzaloŵamo.”
18
Mkulu wina adafunsa Yesu kuti, “Aphunzitsi abwino, kodi ndizichita chiyani kuti ndikalandire moyo wosatha?”
19
Yesu adamuyankha kuti, “Ukunditchuliranji wabwino? Wabwinotu ndi mmodzi yekha, Mulungu basi.
20
Malamulo ukuŵadziŵa: Usachite chigololo, usaphe, usabe, usachite umboni wonama, lemekeza atate ako ndi amai ako.”
21
Munthu uja adati, “Zonsezi ndakhala ndikuzitsata kuyambira ndili mwana.”
22
Pamene Yesu adamva zimenezi, adamuuza kuti, “Ukusoŵabe chinthu chimodzi: kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”
23
Koma pamene munthu uja adamva zimenezi, adavutika mu mtima, pakuti adaali wolemera kwambiri.
24
Yesu adamuyang'ana, nanena kuti, “Nkwapatali kwambiri kwa anthu achuma kuti akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.
25
Nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”
26
Anthu amene adamva zimenezi adafunsa kuti, “Tsono nanga angathe kupulumuka ndani?”
27
Yesu adati, “Zimene zili zosatheka ndi anthu, zimatheka ndi Mulungu.”
28
Pamenepo Petro adati, “Ifetu paja tidasiya zonse kuti tizikutsatani.”
29
Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wosiya nyumba, kapena mkazi, kapena abale, kapena makolo, kapena ana chifukwa cha Ufumu wa Mulungu,
30
ameneyo pansi pompano adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri koposa kale, kenaka kutsogoloko adzalandira moyo wosatha.”
31
Yesu adatengera ophunzira ake pambali, naŵauza kuti, “Tilitu pa ulendo wopita ku Yerusalemu, ndipo zonse zidzachitika zimene aneneri adalemba zokhudza Mwana wa Munthu.
32
Akampereka kwa anthu akunja. Amenewo akamchita chipongwe, akamnyazitsa, ndi kumthira malovu.
33
Akamkwapula, nkumupha, koma mkucha wake Iye adzauka.”
34
Ophunzira aja sadamvetse konse zimenezi. Tanthauzo la mau ameneŵa linali lobisika kwa iwo, nchifukwa chake sadamvetsetse zimene Yesu ankanenazo.
35
Pamene Yesu ankayandikira ku Yeriko, munthu wina wakhungu adaakhala pamphepete pa mseu akupemphapempha kwa anthu.
36
Atamva anthu ambirimbiri akupita mumseumo, adafunsa kuti, “Kodi kuli chiyani?”
37
Adamuyankha kuti, “Kukupita Yesu wa ku Nazarete.”
38
Apo iye adanena mokweza mau kuti, “Inu Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”
39
Anthu amene anali patsogolo adamzazira, adati, “Khala chete!” Koma iye adafuulirafuulira kuti, “Inu Mwana wa Davide, chitireni chifundo!”
40
Yesu adaima nalamula kuti abwere naye kwa Iye. Atafika pafupi, Yesu adamufunsa kuti,
41
“Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Iye adati, “Ambuye, ndikufuna kuti ndizipenyanso.”
42
Yesu adamuuza kuti, “Penya. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”
43
Nthaŵi yomweyo adapenyanso nayamba kutsata Yesu, akuthokoza Mulungu. Anthu onse aja ataona zimenezi, adatamanda Mulungu.
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
Recommended Reading
Commentary
Luke Commentaries
→
Devotional
Luke Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→