bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 13
Luke 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 14 →
1
Anthu ena amene anali pomwepo adadza kwa Yesu, nayamba kumsimbira za Agalileya amene Pilato adaalamula kuti aphedwe, pamene iwo ankapereka nsembe zao kwa Mulungu.
2
Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi mukuyesa kuti Agalileyawo anali ochimwa koposa Agalileya ena onse, popeza kuti adaphedwa motere?
3
Iyai, koma mukapanda kutembenuka mtima, inunso mudzaonongedwa ngati iwo aja.
4
Nanga anthu aja 18 amene nyumba yosanja idaŵagwera ku Siloamu nkuŵapha? Kodi mukuyesa kuti iwowo anali ophwanya malamulo koposa anthu ena onse okhala m'Yerusalemu?
5
Iyai, koma mukapanda kutembenuka mtima, inunso mudzaonongedwa ngati iwo aja.”
6
Yesu adaŵaphera fanizo, adati, “Munthu wina anali ndi mkuyu wobzalidwa m'munda wake wamphesa. Adakafunamo zipatso, koma osazipeza.
7
Tsono adauza wosamala mundawo kuti, ‘Papita zaka zitatu tsopano ndikufuna zipatso mu mkuyu uwu, koma osazipeza. Udule tsono. Ukugugitsiranji nthaka?’
8
Koma iye adati, ‘Ambuye, baulekani chaka chino chokha. Ndiukumbira pa tsinde nkuuthira manyowa.
9
Ukadzabala zipatso chaka chamaŵa, zidzakhala bwino. Koma ukakapanda kubala, apo mudzaudule.’ ”
10
Tsiku lina la Sabata Yesu ankaphunzitsa m'nyumba ina yamapemphero.
11
M'menemo munali mai wina amene anali ndi mzimu woipa umene udamudwalitsa zaka 18. Anali ndi msana wokhota, mwakuti sankatha konse kuŵeramuka.
12
Pamene Yesu adamuwona, adamuitana namuuza kuti, “Mai inu, mwamasuka ku matenda anu.”
13
Adamsanjika manja, ndipo pompo maiyo adaongoka, nayamba kutamanda Mulungu.
14
Koma mkulu wa nyumba yamapemphero ija adakwiya, poona kuti Yesu wachiritsa munthu pa tsiku la Sabata. Tsono mkuluyo adauza anthu onse kuti, “Pali masiku asanu ndi limodzi antchito. Muzibwera masiku ameneŵa kudzachiritsidwa, osati pa tsiku la Sabata ai”
15
Koma Ambuye adati, “Anthu achiphamaso inu, kodi suja nonsenu mumamasula ng'ombe zanu kapena abulu anu pa tsiku la Sabata kukaŵamwetsa madzi?
16
Nanga maiyu, amene ali mwana wa Abrahamu, ndipo Satana adaamumanga zaka 18, kodi sikunayenera kuti amasulidwe ku nsinga imeneyi pa tsiku la Sabata?”
17
Yesu atanena zimenezi, adani ake onse adachita manyazi. Koma anthu ena onse adakondwera chifukwa cha ntchito zodabwitsa zimene Iye ankachita.
18
Yesu adati, “Kodi Ufumu wa Mulungu uli ngati chiyani, ndipo ndingauyerekeze ndi chiyani?
19
Uli ngati njere ya mbeu ya mpiru imene munthu adakaifesa m'munda mwake. Idamera nisanduka mtengo, mbalame zamumlengalenga nkumabwera kudzamanga zisa pa nthambi zake.”
20
Yesu adatinso, “Ndingayerekezenso ndi chiyani Ufumu wa Mulungu?
21
Ulinso ngati chofufumitsira buledi, chimene mai wina adachisanganiza ndi ufa wokwanira miyeso itatu, mpaka mtanda wonse udafufuma.”
22
Pa ulendo wake wopita ku Yerusalemu, Yesu ankayendera mizinda ndi midzi akuphunzitsa.
23
Munthu wina adamufunsa kuti, “Ambuye, kodi adzapulumuka ndi anthu oŵerengeka okha?” Yesu adayankha kuti,
24
“Yesetsani kuloŵera pa khomo lophaphatiza, pakuti kunena zoona anthu ambiri adzafuna kuloŵa, koma adzalephera.
25
“Mwini nyumba adzanyamuka nkutseka pa khomo. Pamenepo, okhala panjanu mudzayamba kugogoda nkumanena kuti, ‘Ambuye, titsekulireni.’ Koma Iye adzakuyankhani kuti, ‘Sindikudziŵa kumene mukuchokera.’
26
Apo inuyo mudzayamba kunena kuti, ‘Pajatu tinkadya ndi kumamwa nanu pamodzi, ndipo Inuyo munkaphunzitsa m'miseu ya m'mizinda mwathu.’
27
Koma Iye adzakuuzani kuti, ‘Pepani, sindikudziŵa kumene mukuchokera. Chokani apa nonsenu, anthu ochita zoipa.’
28
Apo mudzayamba kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzaona Abrahamu ndi Isaki ndi Yakobe ndi aneneri onse mu Ufumu wa Mulungu, inuyo mukuponyedwa kunja.
29
Anthu adzachokera kuvuma ndi kuzambwe, kumpoto ndi kumwera, nadzakhala podyera mu Ufumu wa Mulungu.
30
Pamenepo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira, ndipo amene ali oyambirira adzakhala otsirizira.”
31
Nthaŵi yomweyo Afarisi ena adadzauza Yesu kuti, “Muchokeko kuno, chifukwa Herode akufuna kukuphani.”
32
Yesu adati, “Pitani kaiwuzeni nkhandweyo kuti ndikutulutsa mizimu yoipa ndiponso ndikuchiritsa anthu lero ndi maŵa, ndipo mkucha mpamene nditsirize ntchito yanga.
33
Komabe ndiyenera kupitirira ndi ulendo wanga lero ndi maŵa ndi mkucha, pakuti mneneri sangafere kwina koma ku Yerusalemu.
34
“Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri nkuŵaponya miyala anthu amene Mulungu amakutumizira. Nkangati ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa anthu ako, monga momwe nkhuku imasonkhanitsira anapiye ake pansi pa mapiko ake, iwe nkumakana.
35
Ndithu nyumba yanu yaikuluyi idzasanduka bwinja. Ndipo ndikunenetsa kuti simudzandiwonanso konse mpaka mudzati, ‘Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye.’ ”
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
Recommended Reading
Commentary
Luke Commentaries
→
Devotional
Luke Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→