bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 10
Luke 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 11 →
1
Pambuyo pake Ambuye adasankha anthu 72, naŵatuma aŵiriaŵiri kuti atsogole kupita ku mudzi uliwonse ndi ku malo aliwonse kumene Iye ankati apiteko.
2
Adaŵauza kuti, “Dzinthu ndzambiri, koma antchito ngochepa. Nchifukwa chake pemphani Mwini dzinthu kuti atume antchito kukatuta dzinthudzo.
3
Pitani tsono. Ndikukutumani ngati anaankhosa pakati pa mimbulu.
4
Musatenge chikwama cha ndalama, kapena thumba lapaulendo, kapenanso nsapato zapadera ai. Musaimenso kuti mupereke moni pa njira.
5
Kunyumba kulikonse kumene mukaloŵe, muyambe mwanena kuti, ‘Mtendere ukhale m'nyumba muno.’
6
Ngati m'nyumbamo muli munthu wofuna mtendere, mtendere umene mwanenawo udzakhala pa iyeyo. Koma ngati mulibe munthu wofuna mtendere, mtendere umene mwanenawo udzabwerera kwa inu.
7
Khalani m'nyumba yomweyo. Mudye ndi kumwa zimene akupatsani, pakuti wantchito ngwoyenera kulandira malipiro ake. Musamachoka kumene mwafikirako nkukaloŵa ku nyumba zina ai.
8
Mukaloŵa m'mudzi, anthu nakulandirani, mudye zimene akukonzerani.
9
Muchiritse anthu odwala amene ali m'mudzimo, ndipo muŵauze kuti, ‘Tsopano ufumu wa Mulungu wakufikirani.’
10
Koma kumudzi kumene mukaloŵe, anthu nkupanda kukulandirani bwino, mukapite m'miseu yam'mudzimo, nkukanena kuti,
11
‘Tikukusansirani ngakhale fumbi la m'mudzi mwanu muno limene linamamatira ku mapazi athu. Komabe dziŵani kuti ufumu wa Mulungu wafika.’
12
Kunena zoona, pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Sodomu koposa polanga mudzi umenewo.
13
“Uli ndi tsoka, iwe Korazini! Uli ndi tsoka, iwe Betsaida! Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa inu, achikhala zidaachitikira ku Tiro ndi ku Sidoni, bwenzi anthu ake atavala kale ziguduli nkudzithira phulusa, kuwonetsa kuti atembenukadi mtima.
14
Koma pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Tiro ndi Sidoni, koposa polanga inu.
15
Ndipo iwe Kapernao, kodi ukuyesa kuti adzakukweza mpaka Kumwamba? Iyai, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa.”
16
Yesu adauza anthu 72 aja kuti, “Wokumverani inu, akumvera Ine amene. Wokukanani inu akukana Ine amene. Ndipo wondikana Ine, akukananso Atate amene adandituma.”
17
Anthu 72 aja adabwerako ndi chimwemwe nati, “Ambuye, ngakhale mizimu yoipa yomwe imatigonjera tikamailamula m'dzina lanu.”
18
Yesu adaŵauza kuti, “Ndidaona Satana alikugwa ngati mphezi kuchokera Kumwamba.
19
Ndakupatsanitu mphamvu kuti muziponda njoka ndi zinkhanira, ndi kumagonjetsa mphamvu zonse za mdani uja. Palibe kanthu kamene kangakupwetekeni.
20
Komabe musakondwere chifukwa choti mizimu yoipa ikukugonjerani, koma muzikondwera kuti maina anu adalembedwa Kumwamba.”
21
Nthaŵi yomweyo Mzimu Woyera adadzaza Yesu ndi chimwemwe, mwakuti Yesuyo adati, “Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaululira anthu osaphunzira nkubisira anthu anzeru ndi ophunzira. Chabwino Atate, pakuti mudafuna kutero mwa kukoma mtima kwanu.
22
“Atate adaika zonse m'manja mwanga. Palibe wina wodziŵa Mwana kupatula Atate okha. Palibenso wina wodziŵa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuululira.”
23
Pambuyo pake Yesu adatembenukira ophunzira ake, naŵauza iwo okha kuti, “Ngodala maso amene akuwona zimene mukuwonazi.
24
Kunena zoona aneneri ambiri ndi mafumu ambiri adaafunitsitsa kuwona zimene inu mukupenyazi, koma sadaziwone. Adaafunitsitsa kumva zimene inu mukumvazi, koma sadazimve.”
25
Katswiri wina wa Malamulo adaimirira kuti ayese Yesu. Adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?”
26
Yesu adati, “Kodi m'Malamulo mudalembedwa chiyani? Mumaŵerengamo zotani?”
27
Iye adayankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi nzeru zako zonse, ndiponso mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
28
Yesu adati, “Mwayankha bwino. Kachiteni zimenezi ndipo mudzakhala ndi moyo.”
29
Koma munthu uja pofuna kudziwonetsa ngati wolungama, adafunsa Yesu kuti, “Nanga mnzangayo ndani?”
30
Apo Yesu adati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira achifwamba adamgwira. Adamuvula zovala, nammenya, nkumusiya ali thasa, ali pafupi kufa.
31
“Ndiye zidangochitika kuti wansembe wina ankapita pa njira yomweyo. Pamene adaona munthu uja, adangolambalala.
32
Chimodzimodzinso Mlevi wina adafika pamalopo, ndipo pamene adaona munthuyo, nayenso adangolambalala.
33
Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, adafikanso pamalo pomwepo. Pamene adaona munthu uja, adamumvera chisoni.
34
Adabwera kwa wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa mabala ake, nkuŵamanga. Atatero adamkweza pa bulu wake, nkupita naye ku nyumba ya alendo, namsamalira bwino.
35
M'maŵa mwake adatulutsa ndalama ziŵiri zasiliva, nazipereka kwa mwini nyumba ya alendoyo. Adamuuza kuti, ‘Msamalireni bwino, ndipo mukamwazanso ndalama zina, ndidzakubwezerani pobwera.’ ”
36
Tsono Yesu adafunsa katswiri wa Malamulo uja kuti, “Inu pamenepa mukuganiza bwanji? Mwa anthu atatuŵa, ndani adakhala ngati mnzake wa munthu uja achifwamba adaamugwirayu?”
37
Iye adati, “Amene adamchitira chifundo uja.” Apo Yesu adamuuza kuti, “Pitani tsono, nanunso muzikachita chimodzimodzi.”
38
Pamene Yesu ndi ophunzira ake anali pa ulendo wao, Iye adaloŵa m'mudzi wina. Tsono mai wina, dzina lake Marita, adamlandira kunyumba kwake.
39
Iyeyu anali ndi mng'ono wake, dzina lake Maria, amene adaadzakhala pansi ku mapazi a Ambuye, namamva mau ake.
40
Koma Marita ankatanganidwa ndi ntchito zambiri. Choncho adapita kwa Yesu nati, “Ambuye, kodi simukusamalako kuti mng'ono wangayu akundilekera ndekha ntchito? Muuzeni adzandithandize.”
41
Ambuye adati, “Iwe Marita iwe, ukutekeseka nkuvutika ndi zinthu zambiri,
42
koma chofunika nchimodzi chokha. Maria ndiye wasankhula chinthu chopambana, ndipo chimenechi palibe wina angamlande ai.”
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
Recommended Reading
Commentary
Luke Commentaries
→
Devotional
Luke Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→