bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 11
Luke 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 12 →
1
Nthaŵi ina Yesu ankapemphera pamalo pena. Pamene adatsiriza, wophunzira wake wina adampempha kuti, “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera, monga Yohane Mbatizi adaphunzitsira ophunzira ake.”
2
Yesu adati, “Pamene mukupemphera muziti, “ ‘Atate, dzina lanu lilemekezedwe. Ufumu wanu udze.
3
Mutipatse ife tsiku lililonse chakudya chathu chamasikuwonse.
4
Mutikhululukire ife machimo athu, pakuti ifenso timakhululukira aliyense wotilakwira. Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa.’ ”
5
Adaŵauzanso kuti, “Tangoganizani: wina mwa inu ali ndi bwenzi lake, nkupita kunyumba kwake pakati pa usiku, nakamuuza kuti, ‘Iwe mnzanga, kodi ungakhale ndi buledi mtatu?
6
Kwafika bwenzi langa, ali pa ulendo, ndipo ndilibe choti ndingampatse.’
7
Koma wam'nyumbayo nkuyankha kuti, ‘Usandivute, ndatseka kale pa khomo, ndipo ine ndi ana anga tagona, sindingadzukenso kuti ndikupatse bulediyo.’
8
Ndithu ndikunenetsa kuti adzauka nkumupatsa, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha khama la wopempha uja. Ndipo adzampatsa zonse zimene akusoŵa.
9
“Motero ndikukuuzani kuti, Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
10
Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira, amene amafunafuna, ndiye amapeza, ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira.
11
Ndani mwa atatenu, mwana wake atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka?
12
Kapena atampempha dzira, iye nkumupatsa chinkhanira?
13
Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene aŵapempha.”
14
Tsiku lina Yesu ankatulutsa mzimu woipa woletsa munthu kulankhula. Mzimuwo utatuluka, munthu amene anali wosalankhulayo adayamba kulankhula, mwakuti anthu ambirimbiri amene anali pomwepo adazizwa kwabasi.
15
Koma ena mwa iwo adati, “Mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipazi nzochokera kwa Belezebulu, mkulu wa mizimu yoipayo.”
16
Enanso pofuna kumuyesa, adampempha kuti aŵaonetse chizindikiro chozizwitsa chochokera kumwamba.
17
Koma Yesu adaadziŵa maganizo ao, motero adaŵauza kuti, “Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo kutha kwake nkomweko. Ndipo m'banja akayamba kukangana, banjalo limapasuka.
18
Tsono ngati a mu ufumu wa Satana ayamba kuukirana, Satanayo ufumu wake ungalimbe bwanji? Paja inu mukuti Ine ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Belezebulu.
19
Ngati Ineyo ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Belezebulu, nanga ophunzira anu amaitulutsa ndi mphamvu za yani? Nchifukwa chake ophunzira anu omwewo ndi amene adzakuweruzani kuti ndinu olakwa.
20
Koma ngati Ine ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Mulungu, ndiye kuti Mulungu wayamba kukhazikitsa ufumu wake pakati panu.
21
“Munthu wamphamvu akamalonda nyumba yake ali ndi zida zankhondo, katundu wake amakhala pabwino.
22
Koma pakabwera wina wamphamvu zoposa, namgonjetsa, amalanda zida zimene ankazidalirazo, nkugaŵagaŵa katundu amene walandayo.
23
“Munthu wosavomerezana ndi Ine, ndiye kuti ngwotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ndiye kuti ameneyo ngwomwaza.
24
“Mzimu woipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo opanda madzi, kufunafuna malo opumulirako. Ndipo ukapanda kuŵapeza, umati, ‘Ndibwerera kunyumba kwanga komwe ndidatuluka kuja.’
25
Tsono ukafika, umapeza m'nyumba muja muli mosesasesa ndi mokonza bwino.
26
Pamenepo umakatenga mizimu ina isanu ndi iŵiri yoipa koposa uwowo, kenaka yonseyo imaloŵa nkukhazikika momwemo. Choncho mkhalidwe wotsiriza wa munthu uja umaipa koposa mkhalidwe wake woyamba.”
27
Pamene Yesu ankalankhula zimenezi, mai wina pakati pa anthu ambiri aja adakweza mau namuuza kuti, “Ngwodala mai amene adabalani nkukuyamwitsani.”
28
Koma Yesu adati, “Iyai, odala ndi anthu amene amamva mau a Mulungu naŵagwiritsa ntchito.”
29
Pamene anthu ankachulukirachulukira, Yesu adati, “Anthu a mbadwo uno ngoipa, amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa. Komabe sadzachiwona chizindikirocho, kupatula cha mneneri Yona chija.
30
Monga Yona uja anali chizindikiro kwa anthu a ku Ninive, chomwechonso Mwana wa Munthu adzakhala chizindikiro kwa anthu a mbadwo uno.
31
Pa tsiku lachiweruzo mfumukazi yakumwera ija idzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nidzaŵatsutsa. Paja iyo idaachita kuchokera ku mathero a dziko lapansi kudzamva zolankhula zanzeru za mfumu Solomoni. Ndipotu pano pali woposa Solomoni amene.
32
Pa tsiku lachiweruzo anthu a ku Ninive aja adzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nadzaŵatsutsa. Paja iwowo adaatembenuka mtima, atamva malaliko a Yona. Ndipotu pano pali woposa Yona amene.”
33
“Munthu sati akayatsa nyale, nkuiika m'chipinda chapansi kapena kuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, kuti anthu oloŵa m'nyumbamo aone kuŵala kwake.
34
Maso ndiwo nyale zounikira thupi lako. Ngati maso ako ali bwino, m'thupi mwako monse mumakhala kuŵala. Koma ngati maso ako sali bwino, m'thupi mwako monse mumakhala mdima.
35
Chenjera tsono kuti kuŵala kumene kuli mwa iwe kusasanduke mdima.
36
Ngati kuŵala kukhala m'thupi monse, popanda mdima pena paliponse, apo thupi lonse lidzakhala loŵala, monga pamene nyale ikukuunikira ndi kuŵala kwake.”
37
Pamene Yesu adatsiriza kulankhula, wina wa m'gulu la Afarisi adamuitana kuti akadye naye. Tsono Yesu adaloŵa m'nyumba nakakhala podyera.
38
Mfarisiyo adadabwa poona kuti Yesu wayamba kudya osatsata mwambo wao wa kasambidwe ka m'manja.
39
Koma Ambuye adamuuza kuti, “Inu Afarisi mumatsuka kunja kwa chikho ndi mbale, koma m'kati ndinu odzaza ndi zonyenga ndi zankhanza.
40
Ndinu anthu opusa! Kodi Mulungu amene adapanga zakunja, si yemweyo adapanganso zam'kati?
41
Popereka zachifundo kwa amphaŵi, muzipereka zimene zili m'kati, ndiye pamenepo zanu zonse zidzakhala zoyera.
42
“Muli ndi tsoka, inu Afarisi, chifukwa mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, cha timbeu tokometsera chakudya, ndiponso cha mbeu zakudimba za mtundu uliwonse. Koma simulabadako kuchita chilungamo, kapena kukonda Mulungu. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo.
43
Muli ndi tsoka, inu Afarisi, chifukwa mumakonda mipando yaulemu m'nyumba zamapemphero, ndiponso kuti anthu azikupatsani moni waulemu pa misika.
44
Muli ndi tsoka, chifukwa muli ngati manda osazindikirika, amene anthu amapondapo osadziŵa kanthu.”
45
Apo katswiri wina wa Malamulo adati, “Aphunzitsi, mukamanena zimenezi, mukunyozatu ndi ife tomwe.”
46
Yesu adati, “Muli ndi tsokanso, inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mumasenzetsa anthu katundu wosautsa kunyamula, pamene inuyo simumkhudzako mpang'ono pomwe.
47
Muli ndi tsoka, chifukwa mumamanga ziliza za aneneri, pamene ndi makolo anu omwe akale amene adapha aneneriwo.
48
Apo mukutsimikiza kuti mukuvomereza ntchito za makolo anuwo, popeza kuti iwowo adapha aneneriwo, inuyo nkumamanga ziliza zao.
49
Nchifukwa chake Nzeru ya Mulungu idati, ‘Ndidzaŵatumizira aneneri ndi atumwi, koma anthu adzapha ena mwa iwo, nkuzunza ena.’
50
Motero anthu amakono adzakhala ndi mlandu chifukwa cha aneneri onse amene adaphedwa chilengedwere dziko lapansi,
51
kuyambira kuphedwa kwa Abele, mpaka kuphedwa kwa Zakariya amene adaphedwera m'Nyumba ya Mulungu pakati pa guwa la nsembe ndi malo opatulika kopambana. Ndithu ndikunenetsa kuti anthu amakono adzakhaladi ndi mlandu chifukwa cha ophedwawo.
52
“Muli ndi tsoka, inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mudalanda kiyi yotsekulira anthu nzeru. Inu nomwe sumudaloŵe, ndipo mudatsekereza amene ankafuna kuloŵa.”
53
Pamene Yesu adatuluka m'nyumbamo, aphunzitsi a Malamulo pamodzi ndi Afarisi adayamba kumzonda ndi kumpanikiza ndi mafunso ambiri ozunguza.
54
Cholinga chao chinali chofuna kumtapa m'kamwa.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
Recommended Reading
Commentary
Luke Commentaries
→
Devotional
Luke Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→