bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Luke 14
Luke 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 15 →
1
Pa tsiku lina la Sabata Yesu adakadya kwa mkulu wina wa m'gulu la Afarisi, ndipo Afarisi anzake ankamupenyetsetsa.
2
Pomwepo pamaso pake panali munthu wina wambulu.
3
Yesu adafunsa akatswiri a Malamulo ndi Afarisi kuti, “Kodi Malamulo amalola kuchiritsa munthu pa tsiku la Sabata, kapena ai?”
4
Koma iwo adangoti chete. Tsono Yesu adatenga munthuyo, ndipo atamchiritsa, adamuuza kuti azipita.
5
Kenaka adaŵafunsa kuti, “Ndani mwa inu, bulu wake kapena ng'ombe yake itagwa m'chitsime pa tsiku la Sabata, sangaitulutse pa Sabata pomwepo?”
6
Iwo adasoŵa poyankha.
7
Yesu adaaona kuti anthu amene adaaitanidwa kudzadya nao ankadzisankhira malo aulemu. Tsono adaŵaphera fanizo, adati,
8
“Wina akakuitana ku phwando la ukwati, usamakhala pa malo aulemu ai, chifukwa mwina kapena adaitananso wina waulemu kuposa iwe.
9
Ndiye iye uja amene adaitana aŵiri nonsenu nkudzakuuza kuti, ‘Pepani, patsani aŵa maloŵa.’ Apo iweyo udzachita manyazi pokakhala pa malo otsika.
10
Koma akakuitana, kakhale pa malo otsika, kuti amene adakuitana uja adzakuuze kuti, ‘Bwenzi langa, dzakhale pa malo aulemu pano.’ Apo udzalandira ulemu pamaso pa onse amene uli nao podyera.
11
Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamkuza.”
12
Yesu adauzanso Mfarisi uja amene adaamuitana kudzadya naye kuti, “Ukamakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamaitana abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anzako achuma, chifukwa mwina iwonso adzakuitanako, motero udzalandiriratu mphotho yako.
13
Koma iwe ukamakonza phwando, uziitana amphaŵi, otsimphina, opunduka ndi akhungu.
14
Apo udzakhala wodala, chifukwa iwo alibe kanthu koti nkukubwezera. Mulungu ndiye adzakubwezera, pamene anthu olungama adzauka kwa akufa.”
15
Munthu wina amene ankadya nao, atamva zimenezi, adauza Yesu kuti, “Ngwodala munthu amene adzadye nao mu Ufumu wa Mulungu.”
16
Koma Yesu adamuphera fanizo, adati, “Munthu wina adaakonza phwando lalikulu, naitana anthu ambiri.
17
Nthaŵi ya phwando itakwana adatuma wantchito wake kukauza oitanidwa aja kuti, ‘Bwerani, pakuti zonse zakonzeka.’
18
Koma onsewo mmodzimmodzi adayamba kupereka zifukwa zokanira. Woyamba adati, ‘Ndidagula munda, tsono ndikuyenera kupita kuti ndikauwone. Pepani sindibwera.’
19
Wina adati, ‘Ndidagula ng'ombe khumi zapagoli, ndiye ndikukaziyesa. Pepani sindibwera.’
20
Ndipo wina adati, ‘Ndangokwatira tsopano apa, choncho sinditha kubwera.’
21
Tsono wantchitoyo atabwerako adadzasimbira mbuye wake zonsezo. Apo mwini nyumbayo adapsa mtima, nauza wantchito wakeyo kuti, ‘Pita msanga ku miseu yaikulu ndi yaing'ono ya mumzinda muno ukapeze anthu osauka, otsimphina, akhungu ndi opunduka, ukabwere nawo kuno.’
22
Atabwerako wantchito uja adati, ‘Bwana, ndachita zija munandilamulazi, koma malo akalipobe.’
23
Apo mbuye uja adamuuza wantchitoyo kuti, ‘Pita ku miseu ndi ku njira za kunja kwa mudzi, ukaŵakakamize anthu kubwera kuno, kuti nyumba yanga idzaze.
24
Kunena zoona, mwa anthu amene ndidaaŵaitana aja palibe ndi mmodzi yemwe amene adzalilaŵe phwando langali.’ ”
25
Chikhamu cha anthu chinkatsagana ndi Yesu. Tsono Iye adatembenuka naŵauza kuti,
26
“Aliyense wofuna kukhala wophunzira wanga, azikonda Ine koposa atate ake ndi amai ake, mkazi wake ndi ana ake, abale ake ndi alongo ake, ndiponso koposa ngakhale moyo wake womwe.
27
Aliyense amene sasenza mtanda wake nkumanditsata, sangakhale wophunzira wanga.
28
“Wina mwa inu akafuna kumanga nyumba yosanja, kodi suja amayamba wakhala pansi nkuŵerenga ndalama zofunika, kuti aone ngati ali nazo zokwanira kuitsiriza?
29
Akapanda kutero, mwina adzaika maziko, nkulephera kuitsiriza. Apo anthu onse, poona zimenezi, adzayamba kumseka.
30
Adzati, ‘Mkulu uyu adaayamba kumanga nyumba, koma adalephera kuitsiriza.’
31
“Chimodzimodzinso kodi ndi mfumu iti, popita ku nkhondo kukamenyana ndi mfumu ina, siiyamba yakhala pansi nkuganiza bwino? Imaganiziratu ngati ndi asilikali zikwi khumi ingathe kukamenyana ndi mfumu ina ija, imene ikubwera ndi asilikali zikwi makumi aŵiri.
32
Tsono ngati siingathe, idzatuma nthumwi kukapempha mtendere, mfumu ina ija ikali kutali.
33
“Chonchonso aliyense mwa inu amene sasiya zonse zimene ali nazo, sangakhale wophunzira wanga.”
34
“Mchere ndi wabwino. Koma ngati mcherewo watha mphamvu, mphamvu zakezo nkuzibwezeranso nchiyani?
35
Ulibenso ntchito ngakhale pa munda, kapena pa dzala. Amangoutaya basi. Amene ali ndi makutu akumva, amve!”
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
Recommended Reading
Commentary
Luke Commentaries
→
Devotional
Luke Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→