bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Proverbs 10
Proverbs 10
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 11 →
1
Mwana wanzeru akondweretsa atate; Koma mwana wopusa amvetsa amace cisoni.
2
Cuma ca ucimo sicithangata: Koma cilungamo cipulumutsa kuimfa.
3
Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama; Koma amainga cifuniro ca wocimwa.
4
Wocita ndi dzanja laulesi amasauka; Koma dzanja la akhama lilemeretsa.
5
Wokolola m'malimwe ndi mwana wanzeru; Koma wogona pakututa ndi mwana wocititsa manyazi.
6
Madalitso ali pamtu pa wolungama Koma m'kamwa mwa oipa mubisa ciwawa.
7
Amayesa wolungama wodala pamkumbukira; Koma dzina la oipa lidzabvunda.
8
Mwini mtima wanzeru amalandira malamulo; Koma citsiru colongolola cidzagwa.
9
Woyenda moongoka amayenda osatekeseka; Koma wokhotetsa njira zace adzadziwika.
10
Wotsinzinira acititsa cisoni; Koma wodzudzula momveka acita mtendere.
11
M'kamwa mwa wolungama ndi kasupe wa moyo; Koma m'kamwa mwa oipa mubisa ciwawa.
12
Udani upikisanitsa; Koma cikondi cikwirira zolakwa zonse.
13
Nzeru ipezedwa m'milomo ya wozindikira; Koma wopusa pamsana pace ntyole.
14
Anzeru akundika zomwe adziwa Koma m'kamwa mwa citsiru muononga tsopano lino.
15
Cuma ca wolemera ndi mudzi wace wolimba; Koma umphawi wao uononga osauka.
16
Nchito za wolungama zipatsa moyo; Koma phindu la oipa licimwitsa.
17
Wosunga mwambo ali m'njira ya moyo; Koma wosiya cidzudzulo asocera.
18
Wobisa udani ali ndi milomo yonama; Wonena ugogodi ndiye citsiru.
19
Pocuruka mau zolakwa sizisoweka; Koma wokhala cete acita mwanzeru.
20
Lilime la wolungama likunga siliva wosankhika; Koma mtima wa oipa uli wacabe.
21
Milomo ya wolungama imadyetsa ambiri; Koma zitsiru zimafa posowa nzeru.
22
Madalitso a Yehova alemeretsa, Saonjezerapo cisoni.
23
Masewero a citsiru ndiwo kucita zoipa; Koma masewero a wozindikira ndiwo nzeru.
24
Comwe woipa aciopa cidzamfikira; Koma comwe olungama acifuna cidzapatsidwa.
25
Monga kabvumvulu angopita, momwemo woipa kuti zi; Koma olungama ndiwo maziko osatha.
26
Ngati vinyo wowawa m'mano, ndi utsi m'maso, Momwemo wolesi kwa iwo amene amtuma.
27
Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku; Koma zaka za oipa zidzafinimpha,
28
Ciyembekezo ca olungama ndico cimwemwe; Koma cidikiro ca oipa cidzaonongeka.
29
Njira ya Yehova ndi linga kwa woongoka mtima; Koma akucita zoipa adzaonongeka.
30
Wolungama sadzacotsedwa konse: Koma oipa sadzakhalabe m'dziko.
31
M'kamwa mwa wolungama mulankhula nzeru; Koma lilime lokhota lidzadulidwa.
32
Milomo ya wolungama idziwa zokondweretsa; Koma m'kamwa mwa oipa munena zokhota,
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31