bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Proverbs 4
Proverbs 4
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 5 →
1
Ananu, mverani mwambo wa atate, Nimuchere makutu mukadziwe luntha;
2
Pakuti ndikuphunzitsani zabwino; Musasiye cilangizo canga.
3
Pakuti ndinali mwana kwa atate wanga, Wokondedwa ndi mai, ndine ndekha, sanabala wina.
4
Atate nandiphunzitsa, nati kwa ine, Mtima wako uumirire mau anga; Sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo.
5
Tenga nzeru, tenga luntha; Usaiwale, usapatuke pa mau a m'kamwa mwanga;
6
Usasiye nzeru, ndipo Idzakusunga; Uikonde, idzakucinjiriza.
7
Nzeru ipambana, tatenga nzeru; M'kutenga kwako konseko utenge luntha.
8
Uilemekeze, ndipo idzakukweza; Idzakutengera ulemu pamene uifungatira.
9
Idzaika cisada ca cisomo pamtu pako; Idzakupatsa korona wokongola.
10
Tamvera mwananga, nulandire mau anga; Ndipo zaka za moyo wako zidzacuruka.
11
Ndakuphunzitsa m'njira ya nzeru, Ndakuyendetsa m'mayendedwe olungama.
12
Mapazi ako sadzaombana ulikuyenda; Ukathamanga, sudzapunthwa.
13
Gwira mwambo, osauleka; Uusunge; pakuti ndiwo moyo wako.
14
Usalowe m'mayendedwe ocimwa, Usayende m'njira ya oipa.
15
Pewapo, osapitamo; Patukapo, nupitirire.
16
Pakuti akapanda kucita zoipa, samagona; Ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwacokera.
17
Pakuti amadya cakudya ca ucimo, Namwa vinyo wa cifwamba.
18
Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kuca, Kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe.
19
Njira ya oipa ikunga mdima; Sadziwa cimene ciwapunthwitsa,
20
Mwananga, tamvera mau anga; Cherera makutu ku zonena zanga.
21
Asacoke ku maso ako; Uwasunge m'kati mwa mtima wako.
22
Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza, Nalamitsa thupi lao lonse.
23
Cinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; Pakuti magwero a moyo aturukamo.
24
Tasiya m'kamwa mokhota, Uike patari milomo yopotoka.
25
Maso ako ayang'ane m'tsogolo, Zikope zako zipenye moongoka,
26
Sinkasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako; Njira zako zonse zikonzeke.
27
Usapatuke ku dzanja lamanja kapena kulamanzere; Suntha phazi lako kusiya zoipa.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31