bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Proverbs 14
Proverbs 14
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 15 →
1
Mkazi yense wanzeru amanga banja lace; Koma wopusa alipasula ndi manja ace.
2
Woyenda moongoka mtima aopa Yehova; Koma wokhota m'njira yace amnyoza,
3
M'kamwa mwa citsiru muli ntyole ya kudzikuza; Koma milomo ya anzeru Idzawasunga.
4
Popanda zoweta modyera muti see; Koma mphamvu ya ng'ombe icurukitsa phindu.
5
Mboni yokhulupirika sidzanama; Koma mboni yonyenga imalankhula zonama.
6
Wonyoza afunafuna nzeru osaipeza; Koma wozindikira saona bvuto m'kuphunzira.
7
Pita pamaso pa munthu wopusa, Sudzazindikira milomo yakudziwa.
8
Nzeru ya wocenjera ndiyo yakuti azindikire njira yace; Koma utsiru wa opusa ndiwo cinyengo.
9
Zitsiru zinyoza kuparamula; Koma mwa oongoka mtima muli ciyanjano.
10
Mtima udziwa kuwawa kwace kwace; Mlendo sadudukira ndi cimwemwe cace.
11
Nyumba ya oipa idzapasuka; Koma hema wa oongoka mtima adzakula.
12
Iripo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka; Koma matsiriziro ace ndi njira za imfa.
13
Ngakhale m'kuseka mtima uwawa; Ndipo matsiriziro a ciphwete ndi cisoni.
14
Wobwerera m'mbuyo m'mtima adzakhuta njira zace; Koma munthu wabwino adzakhuta za mwa iye yekha.
15
Wacibwana akhulupirira mau onse; Koma wocenjera asamalira mayendedwe ace.
16
Wanzeru amaopa nasiya zoipa; Koma wopusa amanyada osatekeseka.
17
Wokangaza kukwiya adzacita utsiru; Ndipo munthu wa ziwembu adzadedwa.
18
Acibwana amalandira colowa ca utsiru; Koma ocenjera amabvala nzeru ngati korona.
19
Oipa amagwadira abwino, Ndi ocimwa pa makomo a olungama.
20
Waumphawi adedwa ndi anzace omwe; Koma akukonda wolemera acuruka.
21
Wonyoza anzace acimwa; Koma wocitira osauka cifundo adala.
22
Kodi oganizira zoipa sasocera? Koma akuganizira zabwino adzalandira cifundo ndi ntheradi.
23
M'nchito zonse muli phindu; Koma kulankhula-lankhula kungopatsa umphawi.
24
Korona wa anzeru ndi cuma cao; Utsiru wa opusa ndiwo utsiru.
25
Mboni yoona imalanditsa miyoyo; Koma wolankhula zonama angonyenga.
26
Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba; Ndipo ana ace adzakhala ndi pothawirapo.
27
Kuopa Yehova ndiko kasupe wa moyo, Kupatutsa ku misampha ya imfa.
28
Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu; Koma popanda anthu kalonga aonongeka.
29
Wosakwiya msanga apambana kumvetsa; Koma wansontho akuza utsiru.
30
Mtima wabwino ndi moyo wa thupi; Koma nsanje ibvunditsa mafupa.
31
Wotsendereza aumphawi atonza Mlengi wace; Koma wocitira wosauka cifundo amlemekeza.
32
Wocimwa adzakankhidwa m'kuipa kwace; Koma wolungama akhulupirirabe pomwalira,
33
Nzeru ikhalabe m'mtima wa wozindikira, Nidziwika pakati pa opusa.
34
Cilungamo cikuza mtundu wa anthu; Koma cimo licititsa pfuko manyazi.
35
Mfumu ikomera mtima kapolo wocita mwanzeru; Koma idzakwiyira wocititsa manyazi.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31