bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Proverbs 11
Proverbs 11
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 12 →
1
Muyeso wonyenga unyansa Yehova; Koma mulingo wamphumphu umsekeretsa.
2
Pakudza kudzikuza padzanso manyazi; Koma nzeru iri ndi odzicepetsa,
3
Kuongoka mtima kwa olungama kuwatsogolera; Koma kukhota kwa aciwembu kudzawaononga.
4
Cuma sicithandiza tsiku la mkwiyo; Koma cilungamo cipulumutsa kuimfa.
5
Cilungamo ca wangwiro cimaongola njira yace; Koma woipa adzagwa ndi zoipa zace.
6
Cilungamo ca oongoka mtima cidzawapulumutsa; Koma aciwembu adzagwidwa ndi mphulupulu yao.
7
Pomwalira woipa cidikiro cace cionongeka; Ciyembekezo ca ucimo cionongeka.
8
Wolungama apulumuka kubvuto; Woipa nalowa m'malo mwace.
9
Wonyoza Mulungu aononga mnzace ndi m'kamwa mwace; Koma olungama adzapulumuka pakudziwa,
10
Olungama akapeza bwino, mudzi usekera; Nupfuula pakuonongeka oipa.
11
Madalitso a olungama akuza mudzi; Koma m'kamwa mwa oipa muupasula.
12
Wopeputsa mnzace asowa nzeru; Koma wozindikira amatonthola.
13
Kazitape woyendayenda amawanditsa zinsinsi; Koma wokhulupirika mtima abisa mau.
14
Popanda upo wanzeru anthu amagwa; Koma pocuruka aphungu pali cipulumutso.
15
Woperekera mlendo cikole adzaphwetekwapo; Koma wakuda cikole akhala ndi mtendere.
16
Mkazi wodekha agwiritsa ulemu; Aukali nagwiritsa cuma.
17
Wacifundo acitira moyo wace zokoma; Koma wankhanza abvuta nyama yace.
18
Woipa alandira malipiro onyenga; Koma wofesa cilungamo aonadi mphotho,
19
Wolimbikira cilungamo alandira moyo; Koma wolondola zoipa adzipha yekha,
20
Okhota mtima anyansa Yehova; Koma angwiro m'njira zao amsekeretsa.
21
Zoonadi, wocimwa sadzapulumuka cilango; Koma mbeu ya olungama idzalanditsidwa.
22
Monga cipini cagolidi m'mphuno ya nkhumba, Momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.
23
Cifuniro ca olungama cifikitsa zabwino zokha; Koma ciyembekezo ca oipa mkwiyo.
24
Alipo wogawira, nangolemerabe; Aliponso womana comwe ayenera kupatsa nangosauka.
25
Mtima wa mataya udzalemera; Wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.
26
Womana tirigu anthu amtemberera; Koma madalitso adzakhala pamtu pa wogulitsa.
27
Wopwaira ubwino afunitsa cikondwerero; Koma zoipa zidzamfikira wozilondola.
28
Wokhulupmra cuma cace adzagwa; Koma olungama adzaphuka ngati tsamba.
29
Wobvuta banja lace adzalowa m'zomsautsa; Wopusa adzatumikira wanzeru.
30
Cipatso ca wolungama ndi mtengo wa moyo; Ndipo wokola mtima ali wanzeru.
31
Taonani, wolungama adzalandira mphotho kunja kuno; Koposa kotani woipa ndi wocimwa?
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31