bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Proverbs 3
Proverbs 3
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 4 →
1
Mwananga, usaiwale malamulo anga, Mtima wako usunge malangizo anga;
2
Pakuti adzakuonjezera masiku ambiri, Ndi zaka za moyo ndi mtendere.
3
Cifundo ndi coonadi zisakusiye; Uzimange pakhosi pako; Uzilembe pamtima pako;
4
Motero udzapezakisomo ndi nzeru yabwino, Pamaso pa Mulungu ndi anthu.
5
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, Osacirikizika pa luntha lako;
6
Umlemekeze m'njira zako zonse, Ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
7
Usadziyese wekha wanzeru; Opa Yehova, nupatuke pazoipa;
8
Mitsempha yako idzalandirapo moyo, Ndi mafupa ako uwisi.
9
Lemekeza Yehova ndi cuma cako, Ndi zinthu zako zonse zoyambirira kuca;
10
Motero nkhokwe zako zidzangoti the, Mbiya zako zidzasefuka vinyo.
11
Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, Ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwace;
12
Pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; Monga atate mwana amene akondwera naye.
13
Wodala ndi wopeza nzeru, Ndi woona luntha;
14
Pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, Phindu lace liposa golidi woyengeka.
15
Mtengo wace uposa ngale; Ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye.
16
Masiku ambiri ali m'dzanja lamanja lace; Cuma ndi ulemu m'dzanja lace lamanzere.
17
Njira zace ziri zokondweretsa, Mayendedwe ace onse ndiwo mtendere.
18
Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; Wakulumirira ngwodala.
19
Yehova anakhazika dziko ndi nzeru; Naika zamwamba ndi luntha.
20
Zakuya zinang'ambika ndi kudziwakwace; Thambo ligwetsa mame.
21
Mwananga, zisacokere ku maso ako; Sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira;
22
Ndipo mtima wako udzatengapo moyo, Ndi khosi lako cisomo.
23
Pompo udzayenda m'njira yako osaopa, Osapunthwa phazi lako.
24
Ukagona, sudzacita mantha; Udzagona tulo tokondweretsa.
25
Usaope zoopsya zodzidzimutsa, Ngakhale zikadza zopasula oipa;
26
Pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako, Nadzasunga phazi lako lingakodwe.
27
Oyenera kulandira zabwino usawamane; Pokhoza dzanja lako kuwacitira zabwino.
28
Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso, Ndipo mawa ndidzakupatsa; Pokhala uli nako kanthu.
29
Usapangire mnzako ciwembu; Popeza akhala nawe pafupi osatekeseka.
30
Usakangane ndi munthu cabe, Ngati sanakucitira coipa,
31
Usacitire nsanje munthu waciwawa; Usasankhe njira yace iri yonse.
32
Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova; Koma cinsinsi cace ciri ndi oongoka.
33
Mulungu atemberera za m'nyumba ya woipa; Koma adalitsa mokhalamo olungama.
34
Anyozadi akunyoza, Koma apatsa akufatsa cisomo.
35
Anzeru adzalandira ulemu colowa cao; Koma opusa adzakweza manyazi.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31