bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Proverbs 18
Proverbs 18
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 19 →
1
Wopanduka afunafuna niro cace, Nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.
2
Wopusa sakondwera ndi kuzindikira; Koma kungobvumbulutsa za m'mtima mwace.
3
Pakudza wamphulupulu padzanso kunyoza; Manyazi natsagana ndi citonzo.
4
Mau a m'kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya; Kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wodzala.
5
Kukometsa mlandu wa wamphulupulu mwatsankhu sikuli kwabwino, Ngakhale kucitira cetera wolungama.
6
Milomo ya wopusa ifikitsa makangano; Ndipo m'kamwa mwace muputa kukwapulidwa.
7
M'kamwa mwa wopusa mumuononga, Milomo yace ikhala msampha wa moyo wace.
8
Mau a kazitape akunga zakudya zolongosoka, Zotsikira m'kati mwa mimba.
9
Wogwira nchito mwaulesi Ndiye mbale wace wa wosakaza.
10
Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; Wolungama athamangiramo napulumuka.
11
Cuma ca wolemera ndico mudzi wace wolimba; Alingalira kuti ndico khoma lalitari.
12
Mtima wa munthu unyada asanaonongeke; Koma cifatso citsogolera ulemu.
13
Wobwezera mau asanamvetse apusa, Nadzicititsa manyazi.
14
Mtima wa munthu umlimbitsa alikudwala; Koma ndani angatukule mtima wosweka?
15
Mtima wa wozindikira umaphunzira; Khutu la anzeru lifunitsa kudziwa.
16
Mtulo wa munthu umtsegulira njira, Numfikitsa pamaso pa akuru.
17
Woyamba kudzinenera ayang'anika wolungama; Koma mnzace afika namuululitsa zace zonse.
18
Ula uletsa makangano, Nulekanitsa amphamvu.
19
Kupembedza mbale utamcimwira nkobvuta, Kulanda mudzi wolimba nkosabvuta; Makangano akunga mipiringidzo ya linga.
20
Mimba ya munthu idzakhuta zipatso za m'kamwa mwace; Iye nadzakhuta phindu la milomo yace.
21
Lilime liri ndi mphamvu pa imfa ndi moyo; Wolikonda adzadya zipatso zace.
22
Wopeza mkazi apeza cinthu cabwino; Yehova amkomera mtima.
23
Wosauka amadandaulira; Koma wolemera ayankha mwaukali.
24
Woyanjana ndi ambiri angodziononga; Koma liripo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira.
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31