bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Proverbs 17
Proverbs 17
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 18 →
1
Nyenyeswa youma, pokhala mtendere, Iposa nyumba yodzala nyama yansembe, pali makangano.
2
Kapolo wocitamwanzeru Adzalamulira mwana wocititsa manyazi, Nadzagawana nao abale colowa.
3
Siliva ali ndi mbiya yosungunulira, golidi ali ndi ng'anjo; Koma Yehova ayesa mitima.
4
Wocimwa amasamalira milomo yolakwa; Wonama amvera lilime losakaza.
5
Wocitira ciphwete aumphawi atonza Mlengi; Wokondwera ndi tsoka sadzapulumuka cilango.
6
Zidzukulu ndizo korona wa okalamba; Ndipo ulemerero wa ana ndiwo atate ao.
7
Mlomo wangwiro suyenera citsiru; Ngakhale mlomo wonama suyenera kalonga ndi pang'ono ponse.
8
Wolandira cokometsera mlandu aciyesa ngale; Pali ponse popita iye acenjera.
9
Wobisa colakwa afunitsa cikondano; Koma wobwereza-bwereza mau afetsa ubwenzi.
10
Cidzudzulo cilowa m'kati mwa wozindikira, Kopambana ndi kukwapula wopusa kwambiri.
11
Woipa amafuna kupanduka kokha; Koma adzamtumizira mthenga wankhanza.
12
Kukomana ndi citsiru m'kupusa kwace Kuopsya koposa cirombo cocicotsera anace.
13
Wobwezera zabwino zoipa, Zoipa sizidzamcokera kwao.
14
Ciyambi ca ndeu cifanana ndi kutsegulira madzi; Tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.
15
Wokometsa mlandu wa wamphulupulu, ndi wotsutsa wolungama, Onse awiriwa amnyansa Yehova.
16
Kodi bwanji mtengo wogulira nzeru uli m'dzanja la citsiru, Popeza wopusa alibe mtima?
17
Bwenzi limakonda nthawi zonse; Ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.
18
Munthu wosowa nzeru apangana kulipirira wina, Napereka cikole pamaso pa mnzace.
19
Wokonda ndeu akonda kulakwa; Ndipo wotarikitsa khomo lace afunafuna kuonongeka.
20
Wokhota mtima sadzapeza bwino Ndipo mwini lilime lokhota adzagwa m'zoipa.
21
Wobala citsiru adzicititsa cisoni; Ndipo atate wa wopusa sakondwa.
22
Mtima wosekerera uciritsa bwino Koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa,
23
Munthu woipa alandira cokometsera mlandu coturutsa m'mfunga, Kuti apambukitse mayendedwe a ciweruzo.
24
Nzeru iri pamaso pa wozindikira; Koma maso a wopusa ali m'malekezero a dziko.
25
Mwana wopusa acititsa atate wace cisoni, Namvetsa zowawa amace wombala.
26
Kulipiritsa wolungama sikuli kwabwino, Ngakhale kukwapula akuru cifukwa aongoka mtima.
27
Wopanda cikamwakamwa apambana kudziwa; Ndipo wofatsa mtima ali wanzeru.
28
Ngakhalecitsirucikatontholaaciyesa canzeru; Posunama ali wocenjera.
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31