bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Proverbs 25
Proverbs 25
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 26 →
1
Iyinso ndiyo miyambo ya Solomo Imene anthu a Hezekiya mfumu ya Yuda anailemba.
2
Kubisa kanthu ndi ulemerero wa Mulungu; Koma ulemerero wa mafumu ndi kusanthula kanthu.
3
Pamlengalenga patarika, ndi padziko pakuya, Koma mitima ya mafumu singasanthulike.
4
Cotsera siliva mphala yace, Mmisiri wa ng'anjo aturutsamo mbale;
5
Cotsera woipa pamaso pa mfumu, Mpando wace udzakhazikika m'cilungamo.
6
Usadzitame pamaso pa mfumu, Ngakhale kuima m'malo mwa akuru;
7
Pakuti kunena kwa iwe, Takwera kuno, Kupambana ndi kuti utsitsidwe pamaso pa kalonga, Amene maso ako anamuona.
8
Usaturuke mwansontho kukalimbana, Ungalephere pa kutha kwace, Atakucititsa mnzako manyazi.
9
Nena mlandu wako ndi mnzako, Osaulula zinsinsi za mwini;
10
Kuti wakumva angakutonze, Mbiri yako yoipa ndi kusacoka.
11
Mau oyenera a pa nthawi yace Akunga zipatso zagolidi m'nsengwa zasiliva.
12
Monga phelele lagolidi ndi cipini cagolidi woyengeka, Momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.
13
Monga cisanu ca cipale cofewa pa nthawi ya masika, Momwemo mthenga wokhulupirika kwa amene anamtuma; Atsitsimutsa moyo wa ambuyace.
14
Monga mitambo ndi mphepo popanda mvula, Momwemo ndiye wodzikweza ndi zipatso zace monyenga.
15
Cipiriro cipembedza mkuru; Lilime lofatsa lityola pfupa,
16
Wapeza uci kodi? Idyapo wokwanira, Kuti ungakukole, nusanze.
17
Phazi lako lilowe m'nyumba ya mnzako kamodzi kamodzi; Kuti angatope nawe ndi kukuda.
18
Wocitira mnzace umboni wonama Ndiye cibonga, ndi lupanga, ndi mubvi wakuthwa.
19
Kukhulupirira munthu wa ciwembu tsiku latsoka Kunga dzino lotyoka ndi phazi loguluka.
20
Monga wobvula maraya tsiku lamphepo, Ngakhale kuthira vinyo wosasa m'soda, Momwemo woyimbira nyimbo munthu wacisoni.
21
Mdani wako akamva njala umdyetse, Akamva ludzu ummwetse madzi,
22
Pakuti udzaunjika makala amoto pamtu pace; Ndipo Yehova adzakupatsa mphotho,
23
Mphepo ya kumpoto ifikitsa mvula; Comweco lilime losinjirira likwiyitsa nkhope.
24
Kukhala pa ngondya ya tsindwi kufunika Kuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola.
25
Monga madzi ozizira kwa munthu wotopa, Momwemo mau abwino akucokera ku dziko lakutari.
26
Monga kasupe wopondedwa, ndi citsime cobvonongeka, Momwemo wolungama ngati akonjera woipa.
27
Kudya uci wambiri sikuli kwabwino; Comweco kufunafuna ulemu wako wako sikuli ulemu.
28
Wosalamulira mtima wace Akunga mudzi wopasuka wopanda linga,
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 26 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31