bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Proverbs 19
Proverbs 19
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 20 →
1
Wosauka woyenda mwangwiro Aposa wokhetsa milomo ndi wopusa.
2
Kukhumba kosadziwa sikuli kwabwino; Ndipo wofulumira ndi mapazi ace amacimwa.
3
Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yace; Mtima wace udandaula pa Yehova.
4
Cuma cionjezetsa mabwenzi ambiri; Koma mnzace wa waumphawi amleka.
5
Mboni yonama sidzakhala yosalangidwa; Wolankhula mabodza sadzapulumuka.
6
Ambiri adzapembedza waufulu; Ndipo yense ndi bwenzi la munthu wopatsa.
7
Abale onse a wosauka amuda; Nanga mabwenzi ace kodi satanimphirana naye? Awatsata ndi mau, koma kuli zi.
8
Wolandira nzeru akonda moyo wace; Wosunga luntha adzapeza zabwino.
9
Mboni yonama sidzapulumuka cilango; Wolankhula mabodza adzaonongeka.
10
Wopusa sayenera kukhala ndi zinthu zolongosoka; Nanga kapolo ayenera kulamulira akalonga kodi?
11
Kulingalira kwa munthu kucedwetsa mkwiyo; Ulemerero wace uli wakuti akhululukire colakwa.
12
Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango; Koma kukoma mtima kwace kunga mame pamsipu.
13
Mwana wopusa ndiye tsoka la atate wace; Ndipo makangano a mkazi ndiwo kudontha-donthabe.
14
Nyumba ndi cuma ndizo colowa ca atate; Koma mkazi wanzeru acokera kwa Yehova.
15
Ulesi ugonetsa tulo tofa nato; Ndipo moyo wamkhongono udzamva njala.
16
Wosunga lamulo asunga moyo wace; Wonyalanyaza mayendedwe ace adzafa.
17
Wocitira waumphawi cifundo abwereka Yehova; Adzambwezera cokoma caceco.
18
Menya mwanako, ciyembekezero ciripo, Osafunitsa kumuononga.
19
Munthu waukali alipire mwini; Pakuti ukampulumutsa udzateronso.
20
Tamvera uphungu, nulandire mwambo, Kuti ukhale wanzeru pa cimariziro cako,
21
Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu; Koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.
22
Cotikondetsa munthu ndico kukoma mtima kwace; Ndipo wosauka apambana munthu wonama.
23
Kuopa Yehova kupatsa moyo; Wokhala nako adzakhala wokhuta; Zoipa sizidzamgwera.
24
Wolesi alonga dzanja lace m'mbale, Osalibwezanso kukamwa kwace.
25
Menya wonyoza, ndipo acibwana adzaceniera; Nudzudzule wozindikira adzazindikira nzeru.
26
Wolanda za atate, ndi wopitikitsa amai, Ndiye mwana wocititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope.
27
Ukangofuna, mwananga, kusocera kusiya mau akudziwitsa, Leka kumva mwambo.
28
Mboni yopanda pace inyoza ciweruzo; M'kamwa mwa amphulupulu mumeza zoipa,
29
Akonzera onyoza ciweruzo, Ndi mikwingwirima pamsana pa opusa.
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31