bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Proverbs 16
Proverbs 16
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 17 →
1
Malongosoledwe a mtima nga munthu; Koma mayankhidwe a lilime acokera kwa Yehova.
2
Njira zonse za munthu ziyera pamaso pace; Koma Yehova ayesa mizimu.
3
Pereka zocita zako kwa Yehova, Ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.
4
Zonse Yehova anazipangaziri ndi zifukwa zao; Ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa,
5
Yense wonyada mtima anyansa Yehova; Zoonadi sadzapulumuka cilango.
6
Mphulupulu iomboledwa ndi cifundo ndi ntheradi; Apatuka pa zoipa poopa Yehova.
7
Njira za munthu zikakonda Yehova, Ayanjanitsana naye ngakhale adani ace.
8
Zapang'ono, pokhala cilungamo, Ziposa phindu lalikuru lopanda ciweruzo.
9
Mtima wa munthu ulingalira njira yace; Koma Yehova ayendetsa mapazi ace.
10
Mau a mlauli ali m'milomo ya mfumu; M'kamwa mwace simudzacita cetera poweruza.
11
Mwini muyeso ndi mulingo wolungama ndiye Yehova; Ndiyenso anapanga miyala yonse yoyesera ya m'thumba.
12
Kucita mphulupulu kunyansa mafumu; Pakuti mpando wao wakhazikika ndi cilungamo.
13
Milomo yolungama ikondweretsa mafumu; Wonena zoongoka amkonda.
14
Mkwiyo wa mfumu ndi mithenga ya imfa; Wanzeru adzaukhulula.
15
M'kuunika kwa nkhope ya mfumu muli moyo; Kukoma mtima kwace kunga mtambo wa mvula ya masika.
16
Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golidi, Kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?
17
Khwalala la oongoka mtima ndilo lakuti asiye zoipa; Wosunga njira yace acinjiriza moyo wace.
18
Kunyada kutsogolera kuonongeka Mtinia wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.
19
Kufatsa mtima ndi osauka Kuposa kugawana zofunkha ndi onyada.
20
Wolabadira mau adzapeza bwino; Ndipo wokhulupirira Yehova adala.
21
Wanzeru mtima adzachedwa wocenjera; Ndipo kukoma kwa milomo kuyenjezera kuphunzira.
22
Nzeru ndi kasupe wa moyo kwa mwini wace; Koma mwambo wa zitsiru ndi utsiru.
23
Mtima wa wanzeru ucenjeza m'kamwa mwace, Nuphunzitsanso milomo yace.
24
Mau okoma ndiwo cisa ca uci, Otsekemera m'moyo ndi olamitsa mafupa.
25
Iripo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka, Koma matsiriziro ace ndi njira za imfa.
26
Wanchito adzigwirira yekha nchito; Pakuti m'kamwa mwace mumfulumiza.
27
Munthu wopanda pace akonzeratu zoipa; Ndipo m'milomo mwace muli moto wopsereza.
28
Munthu wokhota amautsa makani; Kazitape afetsa ubwenzi.
29
Munthu waciwawa akopa mnzace, Namuyendetsa m'njira yosakhala bwino.
30
Wotsinzina ndiye aganizira zakhota; Wosunama afikitsa zoipa.
31
Imvi ndiyo korona wa ulemu, Idzapezedwa m'njira ya cilungamo.
32
Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; Wolamulira mtima wace naposa wolanda mudzi.
33
Maere aponyedwa pamfunga; Koma ndiye Yehova alongosola zonse.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31