bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Proverbs 12
Proverbs 12
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 13 →
1
Wokonda mwambo akonda kudziwa; Koma wakuda cidzudzulo apulukira.
2
Yehova akomera mtima munthu wabwino; Koma munthu wa ziwembu amtsutsa,
3
Munthu sadzakhazikika ndi udio, Muzu wa olungama sudzasunthidwa.
4
Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wace; Koma wocititsa manyazi akunga cobvunditsa mafupa a mwamunayo.
5
Maganizo a olungama ndi ciweruzo; Koma uphungu wa oipa unyenga.
6
Mau a oipa abisalira mwazi; Koma m'kamwa mwa olungama muwalanditsa.
7
Oipa amagwa kuli zi; Koma banja la olungama limaimabe.
8
Munthu amatamandidwa monga mwa nzeru yace; Koma wokhota mtima adzanyozedwa.
9
Wonyozedwa, amene ali ndi kapolo, Aposa wodzikuza, amene asowa zakudya.
10
Wolungama asamalira moyo wa coweta cace; Koma cifundo ca oipa ndi nkhanza.
11
Zakudyazikwanira wolima minda yace; Koma wotsata anthu opanda pace asowa nzeru.
12
Woipa akhumba cokodwa ndi amphulupulu; Koma muzu wa olungama umabala zipatso.
13
M'kulakwa kwa milomo muli msampha woipa; Koma wolungama amaturuka m'mabvuto.
14
Munthu amakhuta zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwace; Zocita za manja ace zidzabwezedwa kwa iye.
15
Njira ya citsiru nlolungama pamaso pace pace; Koma wanzeru amamvera uphungu.
16
Mkwiyo wa citsiru udziwika posacedwa; Koma wanzeru amabisa manyazi.
17
Wolankhula ntheradi aonetsa cilungamo; Koma mboni yonama imanyenga.
18
Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; Koma lilime la anzeru lilamitsa.
19
Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse; Koma lilime lonama likhala kamphindi.
20
Cinyengo ciri m'mitima ya oganizira zoipa; Koma aphungu a mtendere amakondwa.
21
Palibe bvuto lidzagwera wolungama; Koma amphulupulu adzadzazidwa ndi zoipa,
22
Milomo yonama inyansa Yehova; Koma ocita ntheradi amsekeretsa.
23
Munthu wanzeru abisa zomwe adziwa; Koma mtima wa opusa ulalikira utsiru.
24
Dzanja la akhama lidzalamulira; Koma wolesi adzakhala ngati kapolo,
25
Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu; Koma mau abwino aukondweretsa.
26
Wolungama atsogolera mnzace; Koma njira ya oipa iwasokeretsa.
27
Wolesi samaocha nyama yace anaigwira; Koma wolungama amalandira cuma copambana ca anthu.
28
M'khwalala la cilungamo muli moyo; M'njira ya mayendedwe ace mulibe imfa.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31