bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Proverbs 7
Proverbs 7
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 8 →
1
Mwananga, sunga mau anga, Ukundike malangizo anga;
2
Sunga malangizo anga, nukhale ndi moyo; Ndi malamulo anga ngati mwana wa diso lako.
3
Uwamange pa zala zako, Uwalembe pamtima pako;
4
Nena kwa nzeru, Ndiwe mlongwanga; Nuche luntha mbale wako.
5
Kuti zikucinjirizire kwa mkazi waciwerewere, Kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mau ace.
6
Pakuti pa zenera la nyumba yanga Ndinapenyera pa made ace; Ndinaona pakati pa acibwana,
7
Ndinazindikira pakati pa ang'ono Mnyamata wopanda nzeru,
8
Alikupita pakhwalala pafupi ndi mphambano ya pa mkaziyo, Ndi kuyenda pa njira ya ku nyumba yace;
9
Pa madzulo kuli sisiro, Pakati pa usiku pali mdima,
10
Ndipo taona, mkaziyo anamcingamira, Atabvala zadama wocenjera mtima,
11
Ali wolongolola ndi wosaweruzika, Mapazi ace samakhala m'nyumba mwace.
12
Mwina ali kumakwalala, mwina ali kumabwalo, Nabisalira pa mphambano zonse.
13
Ndipo anagwira mnyamatayo, nampsompsona; Nati kwa iye ndi nkhope yacipongwe,
14
Nsembe za mtendere ziri nane; Lero ndacita zowinda zanga.
15
Cifukwa cace ndaturuka kudzakucingamira, Kudzafunitsa nkhope yako, ndipo ndakupeza.
16
Ndayala zopfunda pakama panga, Nsaru zamangamanga za thonje la ku Aigupto,
17
Ndakapiza pamphasa panga mankhwala onunkhira A mvunja ndi cisiyo ndi mtanthanyerere.
18
Tiye tikondwere ndi cikondano mpaka mamawa; Tidzisangalatse ndi ciyanjano.
19
Pakuti mwamuna kulibe kwathu, Wapita ulendo wa kutari;
20
Watenga thumba la ndalama m'dzanja lace, Tsiku lowala mwezi adzabwera kwathu.
21
Amkakamiza ndi kukoka kwa mau ace, Ampatutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yace.
22
Mnyamatayo amtsata posacedwa, monga ng'ombe ipita kukaphedwa; Ndi monga unyolo umadza kulanga citsiru;
23
Mpaka mubvi ukapyoza mphafa yace; Amtsata monga mbalame yotamangira msampha; Osadziwa kuti adzaononga moyo wace.
24
Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, Labadirani mau a m'kamwa mwanga.
25
Mtima wako usapatukire ku njira ya mkaziyo, Usasocere m'mayendedwe ace.
26
Pakuti amagwetsa ambiri, atawalasa; Ndipo ophedwa ndi iye acurukadi.
27
Nyumba yace ndiyo njira ya kumanda, Yotsikira ku zipinda za imfa.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31