bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Proverbs 26
Proverbs 26
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 27 →
1
Monga cipale cofewa m'malimwe, ndi mvula m'masika, Momwemo ulemu suyenera citsiru.
2
Monga mpheta irikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka, Momwemo temberero la pacabe silifikira.
3
Cikoti ciyenera kavalo, ndi cam'kamwa ciyenera buru, Ndi ntyole iyenera pamsana pa zitsiru.
4
Usayankhe citsiru monga mwa utsiru wace, Kuti ungafanane naco iwe wekha.
5
Yankha citsiru monga mwa utsiru wace, Kuti asadziyese wanzeru.
6
Wotumiza mau ndi dzanja la citsiru Adula mapazi ace, namwa zompweteka.
7
Miyendo ya wopunduka iri yolobodoka, Momwemo mwambi m'kamwa mwa zitsiru.
8
Monga thumba la ngale m'mulu wa miyala, Momwemo wocitira citsiru ulemu.
9
Monga munga wolasa dzanja la woledzera, Momwemo mwambi m'kamwa mwa zitsiru.
10
Monga woponya mibvi ndi kulasa onse, Momwemo wolembera citsiru, ndi wolembera omwe alikupita panjira.
11
Monga garu abweranso ku masanzi ace, Momwemo citsiru cicitanso zopusa zace.
12
Kodi uona munthu wodziyesa wanzeru? Ngakhale citsiru cidzacenjera koma ameneyo ai.
13
Wolesi ati, Mkango uli panjira, Wobangulawo uli m'makwalala.
14
Monga citseko cikankhikira pa zitsulo za pamphuthu, Momwemo wolesi agubuduka pakama pace.
15
Wolesi alonga dzanja lace m'mbale; Kumtopetsa kulibweza kukamwa kwace.
16
Wolesi adziyesa wanzeru Koposa anthu asanu ndi awiri akuyankha mozindikira.
17
Wakungopita ndi kubvutika ndi ndeu yosakhala yace Akunga wogwira makutu a garu.
18
Monga woyaruka woponya nsakali, Mibvi, ndi imfa,
19
Momwemo wonyenga mnzace ndi kuti, Ndi kusewera kumeneku.
20
Posowa nkhuni moto ungozima; Ndi popanda kazitape makangano angoleka.
21
Monga makala ozizira pa makala akunyeka, ndi nkhuni pamoto; Momwemo munthu wamakangano autsa ndeu.
22
Mau a kazitape ndi zakudya zolongosoka Zitsikira m'kati mwa mimba.
23
Milomo yofunitsitsa ndi mtima woipa Ikunga mbale yadothi anaimata ndi mphala yasiliva.
24
Wakuda mnzace amanyenga ndi milomo yace; Koma akundika cinyengo m'kati mwace;
25
Pamene akometsa mau ace usamkhulupirire; Pakuti m'mtima mwace muli zonyansa zisanu ndi ziwiri.
26
Angakhale abisa udani wace pocenjera, Koma udio wace udzabvumbulutsidwa posonkhana anthu.
27
Wokumba dzenje adzagwamo, Wogubuduza mwala, udzabweranso pa iye mwini.
28
Lilime lonama lida omwewo linawasautsa; Ndipo m'kamwa mosyasyalika mungoononga.
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 27 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31