bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Proverbs 21
Proverbs 21
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 22 →
1
Mtima wa mfumu uli m'dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi; Aulozetsa komwe afuna.
2
Njira zonse za munthu zilungama pamaso pace; Koma Yehova ayesa mitima.
3
Kucita cilungamo ndi ciweruzo Kupambana ndi nsembe kumkonda Yehova.
4
Maso akunyada, ndi mtima wodzikuza, Ndi nyali ya oipa, ziri cimo.
5
Zoganizira za wakhama zicurukitsadi katundu; Koma yense wansontho angopeza umphawi.
6
Kupata cuma ndi lilime lonama ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa.
7
Ciwawa ca amphulupulu cidzawakokolola; Cifukwa akana kucita ciweruzo.
8
Wosenza cimo njira yace ikhotakhota; Koma nchito ya woyera mtima ilungama.
9
Kukhala pa ngondya ya tsindwi kufunika Kuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola.
10
Wamphulupulu mtima wace umkhumba zoipa; Sakomera mtima mnzace.
11
Polangidwa wonyoza, wacibwana alandira nzeru, Naphunzira pakuyang'ana pa wanzeru.
12
Wolungama aganizira za nyumba ya wamphulupulu, Kuti amphulupulu amagwetsedwa, naona zoipa.
13
Wotseka makutu ace polira waumphawi, Nayenso adzalira koma osamvedwa.
14
Mphatso ya m'tseri ipembedza mkwiyo, Ndi mtulo wa pamfunga ukali wolimba.
15
Kucita ciweruzo kukondweretsa wolungama; Koma kuwaononga akucita mphulupulu,
16
Munthu wosocera pa njira ya nzeru Adzakhala m'msonkhano wa akufa.
17
Wokonda zoseketsa adzasauka; Wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.
18
Wocimwa ndiye ciombolo ca wolungama; Ndipo waciwembu adzalowa m'malo mwa oongoka mtima.
19
Kukhala m'cipululu kufunika Kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wong'ung'udza.
20
Mokhala wanzeru muli katundu wofunika ndi mafuta; Koma wopusa angozimeza.
21
Wolondola cilungamo ndi cifundo Apeza moyo, ndi cilungamo, ndi ulemu.
22
Wanzeru akwera pa mudzi wa olimba, Nagwetsa mphamvu yace imene anaikhulupirira.
23
Wosunga m'kamwa mwace ndi lilime lace Asunga moyo wace kumabvuto.
24
Wonyada wodzikuza dzina lace ndiye wonyoza; Acita mwaukali modzitama.
25
Cifuniro ca wolesi cimupha; Cifukwa manja ace akana kugwira nchito.
26
Ena asirira modukidwa tsiku lonse; Koma wolungama amapatsa osamana.
27
Nsembe ya oipa inyansa; Makamaka pakudza nayo iwo mwaciwembu.
28
Mboni yonama idzafa; Koma mwamuna wakumvetsa adzanena mosakayika,
29
Munthu woipa aumitsa nkhope yace; Koma woongoka mtima akonza njira zace.
30
Kulibe nzeru ngakhale luntha Ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.
31
Kavalo amakonzedweratu cifukwa ca tsiku la nkhondo; Koma wopulumutsa ndiye Yehova.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31