bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 1
Matthew 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 2 →
1
Yesu Khristu, makolo ake anali Davide ndi Abrahamu. Motsatanatsatana maina a makolo ake onse ndi aŵa:
2
Abrahamu adabereka Isaki, Isaki adabereka Yakobe, Yakobe adabereka Yuda ndi abale ake.
3
Yuda adabereka Perezi ndi Zera, mwa Tamara; Perezi adabereka Hezironi, Hezironi adabereka Ramu.
4
Ramu adabereka Aminadabu, Aminadabu adabereka Nasoni, Nasoni adabereka Salimoni.
5
Salimoni adabereka Bowazi mwa Rahabu, Bowazi adabereka Obede mwa Rute, Obede adabereka Yese,
6
Yese adabereka mfumu Davide. Davide adabereka Solomoni, mwa amene poyamba adaali mkazi wa Uriya.
7
Solomoni adabereka Rehobowamu, Rehobowamu adabereka Abiya, Abiya adabereka Asa.
8
Asa adabereka Yehosafati, Yehosafati adabereka Yoramu, Yoramu adabereka Uziya.
9
Uziya adabereka Yotamu, Yotamu adabereka Ahazi, Ahazi adabereka Hezekiya.
10
Hezekiya adabereka Manase, Manase adabereka Amoni, Amoni adabereka Yosiya.
11
Yosiya adabereka Yekoniya ndi abale ake, pa nthaŵi imene Aisraele adaatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni.
12
Aisraele atatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni, Yekoniya adabereka Salatiele, Salatiele adabereka Zerubabele.
13
Zerubabele adabereka Abihudi, Abihudi adabereka Eliyakimu, Eliyakimu adabereka Azoro.
14
Azoro adabereka Zadoki, Zadoki adabereka Akimu, Akimu adabereka Eliudi.
15
Eliudi adabereka Eleazara, Eleazara adabereka Matani, Matani adabereka Yakobe.
16
Yakobe adabereka Yosefe, mwamuna wa Maria. Mariayu adabala Yesu, wotchedwa Khristu.
17
Choncho panali mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa Abrahamu mpaka pa mfumu Davide, mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa Davideyo mpaka pa nthaŵi imene Aisraele adaatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni, ndiponso mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa nthaŵi yotengedwa ukapolo kupita ku Babiloni mpaka pa nthaŵi ya Khristu, Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
18
Kubadwa kwa Yesu Khristu kudaatere: amai ake Maria adaafunsidwa mbeta ndi Yosefe; koma asanaloŵane, Maria adaapezeka kuti ali ndi pathupi mwa mphamvu za Mzimu Woyera.
19
Mwamuna wake Yosefe anali munthu wokonda chilungamo, komabe sadafune kumchititsa manyazi poyera. Nchifukwa chake adaganiza za kungothetsa mbeta ija osachitapo mlandu.
20
Akulingalira zimenezi, mngelo wa Ambuye adamuwonekera m'maloto, namuuza kuti, “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kumtenga Maria, mkazi wakoyu. Pathupi ali napopa padachitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
21
Adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu, chifukwa adzapulumutsa anthu ake ku machimo ao.”
22
Zonsezi zidaatero kuti zipherezere zimene Ambuye adaalankhulitsa mneneri kuti,
23
“Namwali wina wosadziŵa mwamuna adzatenga pathupi nkubala mwana wamwamuna. Mwanayo adzatchedwa dzina loti Imanuele,” ndiye kuti “Mulungu ali nafe.”
24
Tsono Yosefe atadzuka, adachita monga momwe mngelo wa Ambuye uja adaamuuzira. Adamtenga Maria, mkazi wake uja,
25
koma sadamdziŵe mpaka adabala mwana wamwamuna. Pambuyo pake Yosefe adatcha mwanayo dzina loti Yesu.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28