bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 14
Matthew 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 15 →
1
Pa nthaŵi imeneyo Herode, mfumu ya ku Galileya, adaamva zimene anthu ankanena za Yesu.
2
Tsono adauza nduna zake kuti, “Ameneyu ndi Yohane Mbatizi uja, adauka kwa akufa, nkuwona akuchita zamphamvu zonsezi.”
3
Pajatu Herode kale adaatuma asilikali ake kuti akagwire Yohane, akammange ndi kumponya m'ndende. Adaachita zimenezi chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo, mbale wake.
4
Pakuti Yohane adaauza Herode kuti, “Nkulakwira Malamulo kumukwatira mkaziyo.”
5
Kwenikweni Herode ankafuna kupha Yohane, koma ankaopa anthu, chifukwa iwo ankati ndi mneneri.
6
Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiasi adaavina pamaso pa anthu oitanidwa ku phwando, mwakuti adaakondwetsa Herode kwambiri.
7
Motero Herode adaalonjeza molumbira kuti, “Ndithudi, ndidzakupatsa chilichonse chimene ungapemphe.”
8
Tsono mai wake atamuuza choti apemphe, mwana wamkazi uja adati, “Mundipatse pompano mutu wa Yohane Mbatizi m'mbale.”
9
Pamenepo mfumu Herode adamva chisoni. Koma chifukwa cha malumbiro ake ndiponso chifukwa cha anthu oitanidwa ku phwando aja, adalamula kuti ampatse mutu adaapemphawo.
10
Tsono adatuma munthu kuti akamdule mutu Yohaneyo m'ndende.
11
Mutuwo adautengera m'mbale nakaupereka kwa mtsikana uja, mtsikanayo nkukaupereka kwa mai wake.
12
Pambuyo pake ophunzira a Yohane adabwera nadzatenga mtembo wake nkukauika m'manda. Kenaka adapita kukauza Yesu.
13
Yesu atazimva zimenezi, adachokako kumeneko m'chombo, kuti apite kwayekha kwazii. Koma anthu atamva, adayenda pa mtunda namlondola kuchokera ku mizinda yao.
14
Yesu adatuluka m'chombomo, ndipo pamene adaŵaona anthu ambirimbiriwo, adaŵamvera chifundo, nayamba kuchiritsa amene ankadwala.
15
Nthaŵi yamadzulo ophunzira ake adadzamuuza kuti, “Kunotu nkuthengo, ndipo ano ndi madzulo. Auzeni anthuŵa azinyamuka, apite ku midzi kuti azikagula chakudya.”
16
Koma Yesu adaŵauza kuti, “Palibe chifukwa choti achokere. Inuyo apatseni chakudya.”
17
Iwo adati, “Pano tili ndi buledi msanu yekha ndi nsomba ziŵiri, basi.”
18
Yesu adati, “Bwera nazoni kuno.”
19
Atatero, adalamula kuti anthu aja akhale pansi pa udzu. Tsono adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziŵiri zija, nayang'ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake, ophunzira aja nkukagaŵira anthuwo.
20
Anthu onsewo adadya mpaka kukhuta. Pambuyo pake ophunzira aja adatola zotsala nkudzaza madengu khumi ndi aŵiri.
21
Koma tsono anthu amene adaadyawo analipo ngati zikwi zisanu amuna okha, osaŵerenga akazi ndi ana.
22
Madzulo omwewo Yesu adalamula ophunzira ake kuti aloŵe m'chombo, atsogole kupita ku tsidya, pamene Iye akuuza anthu kuti azipita kwao.
23
Tsono atatsazikana nawo anthu aja, Iye adakwera ku phiri yekha kukapemphera. M'mene kunkayamba kuda, nkuti ali komweko yekhayekha.
24
Pamenepo nkuti chombo chija chili kutalitali ndi mtunda, chikuvutika ndi mafunde, chifukwa chinali chitayang'anana ndi mphepo.
25
M'mamaŵa kukali mbuu, Yesu adadza kwa iwo Iye akuyenda pa madzi.
26
Pamene ophunzira aja adamuwona akuyenda pa madzi, adaopsedwa nati, “Ndi mzukwa!” Ndipo adayamba kukuwa chifukwa cha mantha.
27
Koma nthaŵi yomweyo Yesu adaŵauza kuti, “Khazikani mtima pansi, ndine; musaope.”
28
Apo Petro adati, “Ambuye, ngati ndinudi, tandiwuzani kuti ndibwere kwa Inu pamadzipo.”
29
Yesu adati, “Chabwino, bwera.” Tsono Petro adatuluka m'chombo nayamba kuyenda pa madzi kupita kwa Yesu.
30
Koma ataona m'mene ikuwombera mphepo, adachita mantha, nkuyamba kumira. Tsono adafuula kuti, “Ambuye, pulumutseni!”
31
Pompo Yesu adatambalitsa dzanja nkumugwira nati, “Iwe wa chikhulupiriro chochepawe, unakayikiranji?”
32
Pambuyo pake aŵiriwo adaloŵa m'chombo muja, mphepo nkuleka.
33
Apo amene anali m'chombo aja adamgwadira Yesu nati, “Ndithudi, ndinu Mwana wa Mulungu.”
34
Tsono onse adaoloka nyanja nakafika ku Genesarete.
35
Anthu akumeneko adamzindikira Yesu, nakadziŵitsa anzao a ku dera lonse lozungulira pamenepo. Motero adadza kwa Yesu ndi anthu onse odwala.
36
Adampempha kuti aŵalole odwalawo kungokhudza ngakhale mphonje ya chovala chake. Mwakuti onse amene ankaikhudza, ankachira.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28