bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 11
Matthew 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 12 →
1
Yesu atatsiriza kulangiza ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, adachoka kumeneko nkumakaphunzitsa ndi kulalika m'mizinda yao.
2
Pamene Yohane Mbatizi anali m'ndende, adaamva zimene Khristu uja ankachita. Choncho adatuma ophunzira ake ena kwa Iye kukamufunsa kuti,
3
“Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?”
4
Yesu adati, “Pitani, kamuuzeni Yohane zimene mukuzimva ndi kuziwona.
5
Akhungu akupenya ndipo opunduka miyendo akuyenda; akhate akuchira ndipo agonthi akumva; akufa akuukitsidwa ndipo amphaŵi akumva Uthenga Wabwino.
6
Ngwodala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.”
7
Pamene amithenga a Yohane aja ankachoka, Yesu adayamba kufunsa makamu a anthu aja za Yohane kuti, “Kodi m'mene mudaapita ku chipululu, mudaati mukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?
8
Nanga mudaati mukaona chiyani? Munthu wovala zofeŵa kodi? Iyai, anthu ovala zofeŵa amakhala m'nyumba za mafumu.
9
Tanenanitu, mudaati mukaona chiyani? Mneneri kodi? Zoonadi, ndipo ndikunenetsa kuti mudakaona woposa mneneri amene.
10
Ameneyu ndiye uja Malembo akunena zakeyu kuti, “ ‘Nayitu nthumwi yanga, ndikuituma m'tsogolo mwako, kuti ikakonzeretu njira yodzadzeramo iwe.’
11
Ndithu ndikunenetsa kuti mwa anthu onse amene adabadwa pansi pano, palibe ndi mmodzi yemwe woposa Yohane Mbatizi. Komabe ngakhale amene ali wamng'onong'ono mu Ufumu wakumwamba amampambana.
12
Kuyambira pa nthaŵi ya Yohane Mbatizi mpaka tsopano anthu akhala akulimbana ndi Ufumu wa Kumwamba, ndipo ochita chamuna ndiwo amene akuulanda.
13
Aneneri onse ndiponso Malamulo a Mose ankaneneratu za Ufumu umenewu mpaka nthaŵi ya Yohane Mbatizi.
14
Ndipo ngati mukufunadi kukhulupirira zimenezi, Yohaneyo ndiye Eliya uja ankati adzabwerayu.
15
Amene ali ndi makutu, amve!
16
“Kaya anthu amakonoŵa ndingaŵafanizire ndi chiyani? Ali ngati ana okangana pa msika, ena akufunsa anzao kuti,
17
“ ‘Tidaakuimbirani ng'oma yaukwati, bwanji inu osavina? Tidaabuma maliro, bwanji inu osalira?’
18
Paja Yohane Mbatizi atabwera, ankasala zakudya ndi zakumwa, anthu nkumati, ‘Adagwidwa ndi mzimu woipa.’
19
Mwana wa Munthu adabwera nkumadya ndi kumwa ndithu, anthu amvekere, ‘Tamuwonani, munthuyu ndi wadyera, chidakwa, ndiponso bwenzi la anthu amsonkho ndi anthu osasamala Malamulo.’ Komabe chilungamo cha nzeru za Mulungu chimatsimikizika ndi zochita zake.”
20
Pambuyo pake Yesu adayamba kudzudzula midzi imene Iye adaaichitira zamphamvu zochuluka. Adaidzudzula chifukwa anthu ake anali osatembenuka mtima.
21
Adati, “Uli ndi tsoka iwe Korazini! Uli ndi tsoka iwe Betsaida! Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa inu, achikhala zidaachitikira ku Tiro ndi ku Sidoni, bwenzi anthu ake atavala kale ziguduli nkudzithira phulusa, kuwonetsa kuti atembenukadi mtima.
22
Koma ndikunenetsa kuti pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Tiro ndi Sidoni, koposa polanga inu.
23
Ndipo iwe Kapernao, kodi ukuyesa kuti adzakukweza mpaka Kumwamba? Iyai, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa. Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa iwe, achikhala zidaachitikira m'Sodomu, bwenzi mzindawo ukadalipo mpaka lero.
24
Koma ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo Mulungu adzachitako chifundo polanga Sodomu koposa polanga iwe.”
25
Pa nthaŵi imeneyo Yesu adati, “Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaululira anthu osaphunzira, nkubisira anthu anzeru ndi ophunzira.
26
Chabwino Atate, pakuti mudafuna kutero mwa kukoma mtima kwanu.
27
“Atate adaika zonse m'manja mwanga. Palibe wina wodziŵa Mwana kupatula Atate okha. Palibenso wina wodziŵa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuululira.
28
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.
29
Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu.
30
Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28