bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 27
Matthew 27
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 28 →
1
M'maŵa kutacha, akulu onse a ansembe ndi akulu a Ayuda adapanga upo kuti aphe Yesu.
2
Adammanga, napita naye kwa Pilato, bwanamkubwa.
3
Pamene Yudasi, wopereka Yesu kwa adani ake uja, adaona kuti Yesu mlandu wamuipira, nthumanzi idamugwira. Tsono adakaŵabwezera akulu a ansembe ndi akulu a Ayudawo ndalama makumi atatu zasiliva zija.
4
Adati, “Ndidachimwa pakupereka munthu wosalakwa kuti aphedwe.” Koma iwo adati, “Ife tilibe nazo kanthu. Izo nzako.”
5
Yudasi adakaziponya ndalamazo m'Nyumba ya Mulungu nachokapo, kenaka nkukadzikhweza.
6
Akulu a ansembe aja adatola ndalamazo nati, “Malamulo athu satilola kuika ndalamazi m'bokosi la chuma cha m'Nyumba ya Mulungu, popeza kuti ndi za magazi.”
7
Choncho adapangana kuti ndalamazo agulire munda wa mmisiri wa mbiya, kuti ukhale manda a alendo.
8
Nchifukwa chake mpaka lero mundawo umatchedwa “Munda wa Magazi.”
9
Motero zidapherezera zimene mneneri Yeremiya adaanena kuti, “Adatenga ndalama zija makumi atatu, mtengo wake umene Aisraele adaagamula,
10
nagulira munda wa mmisiri wa mbiya, monga momwe Ambuye adaandilamulira.”
11
Tsono Yesu adaimirira pamaso pa bwanamkubwa. Iyeyo adamufunsa kuti, “Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu adati, “Mwanena nokha.”
12
Koma pamene akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda aja ankamuneneza, Yesu sadayankhepo kanthu.
13
Apo Pilato adamufunsa kuti, “Kodi sukumva zonse akukunenezazi?”
14
Koma Yesu sadamuyankhe kanthu, kotero kuti bwanamkubwa uja adadabwa kwambiri.
15
Pa nthaŵi ya chikondwerero cha Paska, bwanamkubwa ankaŵamasulira anthu mkaidi mmodzi, yemwe iwo ankafuna.
16
Pa nthaŵi imeneyo panali mkaidi wina wodziŵika, dzina lake Barabasi.
17
Tsono anthu atasonkhana, Pilato adaŵafunsa kuti, “Mukufuna kuti ndikumasulireni uti, Barabasi kapena Yesu, wotchedwa Khristu?”
18
Adaatero chifukwa adaadziŵa kuti Yesuyo anthuwo angodzampereka chifukwa cha kaduka chabe.
19
Pilato ali pa mpando woweruzira milandu, mkazi wake adamtumizira mau. Adati, “Musaloŵerepo pa nkhani ya munthu wolungamayo. Inetu maloto andivuta kwambiri usiku chifukwa cha Iyeyo.”
20
Akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda adayamba kukakamiza anthu kupempha Pilato kuti amasule Barabasi, ndipo kuti Yesu aphedwe.
21
Tsono bwanamkubwa uja adaŵafunsa kuti, “Mukufuna kuti ndikumasulireni uti mwa aŵiriŵa?” Anthu aja adati, “Barabasi.”
22
Pilato adaŵafunsa kuti, “Nanga tsono ndichite naye chiyani Yesu, wotchedwa Khristuyu?” Anthu onse aja adati, “Apachikidwe pa mtanda!”
23
Pilato adaŵafunsanso kuti, “Adalakwanji?” Koma anthu aja adafuula koposa kuti, “Apachikidwe pa mtanda!”
24
Pilato adaona kuti sakuphulapo kanthu, ndipo kuti anthu ali pafupi kuchita chipwirikiti. Choncho adaitanitsa madzi, nkusamba m'manja pamaso pa anthu onse, nanena kuti, “Ine ndiye ndilibe kanthu pa imfa ya munthuyu. Izo nzanu.”
25
Anthu onse aja adati, “Imfayo mlandu wake ugwere ife ndi ana athu.”
26
Apo Pilato adaŵamasulira Barabasi, nalamula kuti Yesu akwapulidwe. Pambuyo pake adampereka kuti akampachike pa mtanda.
27
Pamenepo asilikali a bwanamkubwa adatenga Yesu nakaloŵa naye kunyumba kwa bwanamkubwa. Adasonkhanitsa gulu lonse la asilikali anzao nazinga Yesu.
28
Adamuvula zovala zake, namuveka chovala chofiira.
29
Adaluka nsangamutu yaminga naiika pamutu pake, ndipo adamgwiritsa ndodo m'dzanja lake lamanja. Kenaka adayamba kumgwadira, namaseŵera naye mwachipongwe nkumanena kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda.”
30
Adamthira malovu, natenga ndodo ija nkumamumenya nayo m'mutu.
31
Ataseŵera naye mwachipongwe choncho, adamuvula chovala chija namuvekanso zovala zake. Kenaka adamtenga, nkupita naye kuti akampachike pa mtanda.
32
Pamene ankatuluka mumzindamo, adakumana ndi munthu wina, dzina lake Simoni, wa ku Kirene. Tsono asilikali aja adamkakamiza kuti asenze mtanda wa Yesu.
33
Ndipo adafika ku malo otchedwa Gologota, (ndiye kuti “Malo a Chibade cha Mutu.”)
34
Kumeneko adapatsa Yesu vinyo wosanganiza ndi ndulu kuti amwe. Koma atalaŵa, adakana kumwa.
35
Atampachika pa mtanda, adagaŵana zovala zake pakuchita maere.
36
Kenaka adakhala pansi namamlonda.
37
Pamwamba pa mutu wake adaalembapo mau osonyeza mlandu womuphera, akuti, “Uyu ndi Yesu, Mfumu ya Ayuda.”
38
Adapachikanso pa mitanda zigaŵenga ziŵiri, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere.
39
Anthu amene ankadutsa pamenepo, ankamunyodola nkumapukusa mitu.
40
Ankanena kuti, “Iwe, suja unkati, ‘Ndidzapasula Nyumba ya Mulungu nkuimanganso pa masiku atatu?’ Ngati ndiwedi Mwana wa Mulungu tadzipulumutsatu nkutsika pamtandapo.”
41
Nawonso akulu a ansembe pamodzi ndi aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda ankamuseka. Ankati,
42
“Adapulumutsa anthu ena, koma akulephera kudzipulumutsa Iye mwini. Si Mfumu ya Aisraele nanga? Atsiketu tsopano pamtandapo kuti timkhulupirire.
43
Ankadalira Mulungu; ampulumutsetu tsopano Mulunguyo, ngati amamkondadi; paja ankati, Ndine Mwana wa Mulungu!”
44
Zigaŵenga zimene adaazipachika pamodzi ndi Yesu zija, nazonso zinkamunyoza chimodzimodzi.
45
Kuyambira pa 12 koloko masana mpaka pa 3 koloko, padaagwa mdima pa dziko lonse.
46
Tsono nthaŵi ili ngati 3 koloko, Yesu adafuula kwakukulu kuti, “Eli, Eli, lama sabakatani?” Ndiye kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?”
47
Atamva mauwo, ena amene adaaimirira pamenepo adati, “Munthuyu akuitana Eliya.”
48
Motero wina adathamanga nakatenga chinkhupule. Adachiviika m'vinyo wosasa, nkuchitsomeka ku bango nampatsira, kuti amwe.
49
Koma ena adati, “Taima, tiwone ngati Eliya abweredi kudzampulumutsa.”
50
Koma Yesu adafuulanso kwakukulu, napereka mzimu wake.
51
Pompo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Kudachita chivomezi, ndipo matanthwe adang'ambika.
52
Manda adatsekuka ndipo anthu a Mulungu ambiri amene anali atamwalira kale, adauka kwa akufa.
53
Adatuluka m'manda, ndipo Yesu atauka kwa akufa, iwo adaloŵa mu Yerusalemu, Mzinda Wopatulika, anthu ambiri nkumaŵaona.
54
Mkulu wa asilikali ndiponso amene anali naye polonda Yesu, ataona chivomezi chija ndi zina zonse zimene zidaachitika, adachita mantha kwambiri nati, “Ndithudi, munthuyu adaalidi Mwana wa Mulungu.”
55
Patali poteropo padaali azimai ambiri akungoyang'anitsitsa. Iwoŵa ndi amene adaatsatira Yesu kuchokera ku Galileya ndi kumamtumikira.
56
Pakati pao panali Maria wa ku Magadala, Maria mai wa Yakobe ndi Yosefe, ndiponso mai wa ana a Zebedeo.
57
Chisisira chitagwa, kudafika munthu wina wolemera, wochokera ku Arimatea, dzina lake Yosefe. Nayenso anali wophunzira wa Yesu.
58
Iyeyu adakapempha mtembo wa Yesu kwa Pilato. Pilato adalamula kuti ampatse mtembowo.
59
Tsono Yosefe adautenga, naukulunga m'nsalu yoyera yabafuta.
60
Adakauika m'manda ake atsopano ochita chosema m'thanthwe. Tsono adagubuduzira chimwala pa khomo kuti atseke pamandapo, nachoka.
61
Maria wa ku Magadala ndi Maria wina uja anali pomwepo atakhala pansi kuyang'anana ndi mandawo.
62
M'maŵa mwake, litapita tsiku lokonzekera Sabata, akulu a ansembe pamodzi ndi Afarisi adasonkhana napita kwa Pilato.
63
Adamuuza kuti, “Bwana, tikukumbukira kuti munthu wonyenga uja akali moyo ankati, ‘Patapita masiku atatu, ndidzaukanso.’
64
Tsono mulamule kuti azilondapo pamanda pake mpaka mkucha. Tikuwopa kuti ophunzira ake angadzabwere nkudzaba mtembo wake, kenaka namadzauza anthu kuti ‘Iye uja wauka kwa akufa.’ Apo kunyenga kotsirizaku kudzakhala koipa zedi kupambana koyamba kuja.”
65
Pilato adaŵauza kuti, “Paja alonda muli nawo. Pitani, kalondeni pamandapo monga mukudziŵira.”
66
Iwo adapitadi, nakatseka manda kolimba posindikiza chizindikiro pa chimwala chotsekeracho. Kenaka adasiya asilikali akulonda pomwepo.
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 28 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28