bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 17
Matthew 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 18 →
1
Patapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro, Yakobe ndi Yohane, mbale wa Yakobeyo, nakwera nawo ku phiri lalitali, kwaokha.
2
Tsono maonekedwe a Yesu adasinthika iwo akuwona. Nkhope yake idaŵala ngati dzuŵa, ndipo zovala zake zidachita kuti mbee kuyera.
3
Nthaŵi yomweyo ophunzira aja adaona Mose ndi Eliya akulankhula naye.
4
Petro adauza Yesu kuti, “Ambuye, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Ngati mukufuna, ndimanga misasa itatu pano, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.”
5
Akulankhula choncho, kudadza mtambo woŵala nuŵaphimba. Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, ndipo ndimakondwera naye kwambiri. Muzimumvera.”
6
Ophunzira aja atamva zimenezi, adachita mantha kwambiri nadzigwetsa chafufumimba.
7
Koma Yesu adabwera, naŵakhudza nkunena kuti, “Dzukani, musachite mantha.”
8
Iwo aja poŵeramuka, adangoona kuti palibe munthu winanso, koma Yesu yekha.
9
Pamene ankatsika phiri lija, Yesu adaŵalamula kuti, “Zimene mwaona m'masomphenyazi musakauze wina aliyense mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa.”
10
Ophunzira aja adamufunsa kuti, “Nanga bwanji aphunzitsi a Malamulo amati Eliya adzayenera kuyamba wabwera?”
11
Yesu adati, “Inde Eliya ayambadi wabwera nkudzakonzanso zonse.
12
Koma ndikunenetsa kuti Eliya adabwera kale, ndipo anthu sadamzindikire, koma adamchita zonse zimene iwo ankafuna. Chonchonso Mwana wa Munthu adzazunzidwa ndi anthuwo.”
13
Pamenepo ophunzira aja adazindikira kuti ankaŵauza za Yohane Mbatizi.
14
Pamene iwo adafikanso kumene kunali khamu la anthu kuja, munthu wina adadzagwadira Yesu.
15
Adati, “Ambuye mchitireni chifundo mwana wanga. Ali ndi khunyu ndipo amavutika koopsa. Kaŵirikaŵiri amagwa pa moto mwinanso m'madzi.
16
Ndinabwera naye kwa ophunzira anuŵa, koma alephera kumchiritsa.”
17
Yesu adati, “Ha! Anthu a m'badwo wopanda chikhulupiriro ndi wopotoka maganizo! Ndiyenera kukhala nanube mpaka liti? Ndiyenera kukupirirani mpaka liti? Tabwera nayeni kuno mwanayo.”
18
Atatero, Yesu adazazira mzimu woipawo, ndipo udatuluka mwa mnyamatayo. Pompo iye adachira.
19
Pambuyo pake ophunzira aja adadza kwa Yesu paseri namufunsa kuti, “Ifeyo ndiye tinalephera bwanji kuutulutsa mzimu woipa uja?”
20
Yesu adaŵayankha kuti, “Chifukwa chake nchakuti chikhulupiriro chanu nchochepa. Ndithu ndikunenetsa kuti mutakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa ngati kambeu ka mpiru, mudzauza phiri ili kuti, ‘Choka apa, pita uko,’ ilo nkuchokadi. Mwakuti palibe kanthu kamene kadzakukanikeni.” [
21
“Koma mzimu wa mtundu umenewu, pokhapokha mutayamba mwapemphera ndi kusala zakudya mpamene mungautulutse.”]
22
Tsiku lina ophunzira atasonkhana onse ku Galileya, Yesu adaŵauza kuti, “Mwana wa Munthu akudzaperekedwa kwa anthu.
23
Iwo adzamupha, koma mkucha wake Iye adzauka.” Ophunzirawo atamva zimenezi, adagwidwa ndi chisoni chachikulu.
24
Pamene Yesu ndi ophunzira ake adafika ku Kapernao, okhometsa msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu adadzafunsa Petro kuti, “Kodi aphunzitsi anuŵa sakhoma msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu?”
25
Iye adati, “Amakhoma.” Tsono Petro ataloŵa m'nyumba, asananene chilichonse, Yesu adamufunsa kuti, “Iwe Simoni, ukuganiza bwanji? Kodi mafumu apansipano amalandira msonkho kwa yani? Kwa anthu a mtundu wao, kapena kwa alendo?”
26
Petro adati, “Kwa alendo.” Apo Yesu adamuuza kuti, “Tsono ndiye kutitu anthu a mtundu wao sayenera kukhoma.
27
Koma kuwopa kuŵakhumudwitsa a ku Nyumba ya Mulunguŵa, kaŵedze nsomba ku nyanja. Nsomba imene ukayambire kuŵedza, ukaikanule kukamwa, ndipo ukapezamo ndalama. Ukatenge ndalamayo nkukakhomera msonkho wanga ndi wako womwe.”
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28