bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 12
Matthew 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 13 →
1
Pa tsiku lina la Sabata Yesu ankadutsa m'minda ya tirigu. Ophunzira ake anali ndi njala, ndipo adayamba kuthyolako ngala za tirigu nkumadya.
2
Pamene Afarisi adaona zimenezi, adauza Yesu kuti, “Taonani, ophunzira anu akuchita zimene siziloledwa pa tsiku la Sabata.”
3
Iye adati, “Kani simudaŵerenge zimene adaachita Davide, pamene iye ndi anzake adaazingwa nayo njala?
4
Suja adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nkukadya buledi woperekedwa kwa Mulungu? Chonsecho buledi ameneyo kunali kosaloledwa kuti iyeyo kapena anzakewo nkumudya, koma ansembe okha.
5
Kaya simudaŵerengenso m'Malamulowo kuti m'Nyumba ya Mulungu, pa tsiku la Sabata, ansembe amaphwanya lamulo lokhudza tsiku la Sabata, komabe saŵayesa olakwa?
6
Ndipotu ndikunenetsa kuti pali wina pano woposa Nyumba ya Mulunguyo.
7
Mukadadziŵa tanthauzo la mau a Mulungu aja akuti, ‘Ndimafuna chifundo, osati nsembe ai,’ sibwenzi mutaweruza kuti ndi olakwa anthu amene sadalakwe konse.
8
Pajatu Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro wonse pa zokhudza tsiku la Sabata.”
9
Yesu adachoka kumeneko nakaloŵa m'Nyumba yamapemphero.
10
M'menemo munali munthu wopuwala dzanja. Tsono anthu ena amene ankafuna chifukwa choti akamnenezere Yesuyo, adamufunsa kuti, “Kodi Malamulo amalola kuchiritsa munthu pa tsiku la Sabata?”
11
Yesu adaŵayankha kuti, “Ndani mwa inu atakhala ndi nkhosa imodzi, nkhosayo nkugwa m'dzenje pa tsiku la Sabata, angapande kuigwira nkuitulutsa?
12
Nanji munthu, amene amaposa nkhosa kutalitali! Ndiye kutitu Malamulo amalola kuchita zabwino pa tsiku la Sabata.”
13
Atatero, adalamula munthu uja kuti, “Tambalitsa dzanja lako.” Iye adalitambalitsa, ndipo dzanja lakelo lidakhalanso bwino ngati linzake.
14
Pamenepo Afarisi aja adatuluka nakachita upo kuti apangane njira yophera Yesu.
15
Yesu atamva za upowo, adachokako kumeneko. Anthu ambiri adamtsatira, ndipo Iye adaŵachiritsa onse amene ankadwala.
16
Koma adaŵalamula kuti asakamuulule.
17
Adaachita zimenezi kuti zipherezere zimene Mulungu adaalankhulitsa mneneri Yesaya kuti,
18
“Nayu mtumiki wanga amene ndamsankha. Ndimamkonda, ndipo mtima wanga umasangalala naye kwambiri. Ndidzaika Mzimu wanga mwa iyeyo, ndipo adzalalika za chilungamo kwa anthu a mitundu ina.
19
Iye sadzachita makani, kapena kufuula. Palibe munthu wodzamva mau ake m'miseu ya m'mizinda.
20
Iye sadzatsiriza bango lothyoka, nyale yofuka sadzaizimitsa, mpaka atapambanitsa chilungamo.
21
Ndipo anthu akunja adzamdalira.”
22
Pambuyo pake anthu adadza kwa Yesu ndi munthu wakhungu, wosatha kulankhula, ndi woloŵedwa mizimu yoipa. Tsono Yesu adamchiritsa, kotero kuti adayamba kulankhula ndi kupenya.
23
Anthu onse adazizwa kwambiri nkumanena kuti, “Kodi ameneyu sangakhale Mwana uja wa Davide?”
24
Koma Afarisi atamva zimenezi adati, “Iyai, mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipa sizichokeratu kwina, koma kwa Belezebulu, mkulu wa mizimu yoipayo.”
25
Yesu adaadziŵa zimenezi, motero adaŵauza kuti, “Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo kutha kwake nkomweko. Ndipo anthu a m'mudzi uliwonse kapena a m'banja lililonse akayamba kuukirana, mudzi wotere kapena banja lotere silingalimbe ai.
26
Ngati a mu ufumu wa Satana atulutsana okhaokha, ndiye kuti agaŵikana. Nanga Satanayo ufumu wake ungalimbe bwanji?
27
Inu mukuti Ineyo ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Belezebulu, nanga ophunzira anu amaitulutsa ndi mphamvu za yani? Nchifukwa chake ophunzira anu omwewo ndi amene adzakuweruzeni kuti ndinu olakwa.
28
Koma ngati Ine ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Mzimu wa Mulungu, ndiye kuti Mulungu wayamba kukhazikitsa ufumu wake pakati panu.
29
“Palibe munthu amene angathe kuloŵa m'nyumba ya munthu wamphamvu nkufunkha chuma chake, atapanda kuyamba wamumanga munthu wamphamvuyo. Atatero ndiye angafunkhe zam'nyumbamo.
30
“Munthu wosavomerezana ndi Ine, ndiye kuti ndi wotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ndiye kuti ameneyo ndi womwaza.
31
Nchifukwa chake ndikunenetsa kuti Mulungu adzakhululukira anthu tchimo lililonse, ngakhale mau achipongwe omunyoza Iyeyo. Koma munthu wochita chipongwe Mzimu Woyera, Mulungu sadzamkhululukira.
32
Chimodzimodzinso aliyense wonenera zoipa Mwana wa Munthu, Mulungu adzamkhululukira. Koma aliyense wonenera zoipa Mzimu Woyera, Mulungu sadzamkhululukira konse nthaŵi ino, ngakhalenso nthaŵi ilikudza.”
33
“Mukanena kuti, ‘Mtengo uwu ngwabwino,’ ndiye kuti zipatso zakenso nzabwino. Koma mukanena kuti, ‘Mtengo uwu ngwoipa,’ ndiye kuti zipatso zakenso nzoipa. Pajatu mtengo umadziŵika ndi zipatso zake.
34
Ana a njoka inu, mungathe bwanji kulankhula zabwino pamene muli oipa? Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.
35
Munthu wabwino amatulutsa zabwino m'chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m'chuma choipa cha mumtima mwake.
36
Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula.
37
Mwakuti chifukwa cha mau ako omwe mlandu udzakukomera kapena kukuipira.”
38
Pamenepo aphunzitsi ena a Malamulo ndi Afarisi ena adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tifuna kuti mutiwonetse chizindikiro chozizwitsa.”
39
Koma Yesu adati, “Anthu a mbadwo uno ndi oipa ndi osakhulupirika, amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa. Komabe sadzachiwona chizindikirocho, kupatula cha mneneri Yona chija.
40
Monga Yona uja anali m'mimba mwa chinsomba chija masiku atatu, usana ndi usiku, chomwechonso Mwana wa Munthu adzakhala m'kati mwa nthaka masiku atatu, usana ndi usiku.
41
Pa tsiku la chiweruzo anthu a ku Ninive adzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nadzaŵatsutsa. Paja iwowo adaatembenuka mtima, atamva malaliko a Yona. Ndipotu pano pali woposa Yona amene.
42
Pa tsiku la chiweruzo mfumukazi yakumwera ija idzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno nidzaŵatsutsa. Paja iyo idaachita kuchokera ku mathero a dziko lapansi kudzamva zolankhula zanzeru za mfumu Solomoni. Ndipotu pano pali woposa Solomoni amene.”
43
“Mzimu woipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo opanda madzi, kufunafuna malo opumulirako, koma osaŵapeza.
44
Ndiye umati, ‘Ndibwerera kunyumba kwanga komwe ndidatuluka kuja.’ Tsono ukafika, umapeza m'nyumba muja muli zii, mosesasesa ndi mokonza bwino.
45
Pamenepo umakatenga mizimu ina isanu ndi iŵiri yoipa koposa uwowo, kenaka yonseyo imaloŵa nkukhazikika momwemo. Choncho mkhalidwe wotsiriza wa munthu uja umaipa koposa mkhalidwe wake woyamba. Zidzateronso ndi anthu ochimwa amakono.”
46
Pamene Yesu ankalankhula ndi anthu ambirimbiri aja, nthaŵi yomweyo amai ake ndi abale ake adafika, naima panja. Ankafuna mpata woti alankhule naye.
47
Tsono munthu wina adauza Yesu kuti, “Amai anu ndi abale anu ali panjapa, akufuna kulankhula nanu.”
48
Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ine amai anga ndani? Ndipo abale anga ndani?”
49
Atatero, adaloza ophunzira ake nati, “Inetu amai anga ndi abale anga ndi aŵa.
50
Pakuti aliyense wochita zimene Atate anga akumwamba akufuna, ameneyo ndiye mbale wanga ndi mlongo wanga ndi amai anga.”
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28