bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 15
Matthew 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 16 →
1
Tsiku lina Afarisi ena ndi aphunzitsi ena a Malamulo adadza kwa Yesu kuchokera ku Yerusalemu. Adamufunsa kuti,
2
“Chifukwa chiyani ophunzira anu sasunga mwambo wa makolo? Sasamba m'manja moyenera akamadya chakudya.”
3
Yesu adaŵayankha kuti, “Nanga bwanji inuyo, chifukwa choumirira miyambo yanu, mumaphwanya lamulo la Mulungu?
4
Paja Mulungu adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’
5
Koma inu mumati, ‘Munthu akauza atate ake kapena amai ake kuti, “Zimene ndikadakuthandiza nazoni, ndazipereka kwa Mulungu,” ameneyo sasoŵanso kulemekeza atate ake.’
6
Pakutero, chifukwa cha mwambo wanuwo, mau a Mulungu inu mumaŵasandutsa achabechabe.
7
Inu anthu achiphamaso, ndithu mneneri Yesaya adaanenadi zoona muja adaati,
8
“ ‘Anthu aŵa amangondilemekeza ndi pakamwa chabe, koma mtima wao uli kutali ndi Ine.
9
Amandipembedza inde, koma kupembedza kwaoko nkopanda phindu, chifukwa zimene amaphunzitsa ngati zophunzitsa zenizeni ndi malamulo a anthu chabe.’ ”
10
Pambuyo pake Yesu adaitana anthu aja kuti adze pafupi, ndipo adaŵauza kuti, “Mverani ndipo mumvetse bwino.
11
Si chinthu choloŵa m'kamwa mwa munthu chimene chimamuipitsa ai, koma chotuluka m'kamwa mwake ndiye chimene chimamuipitsa.”
12
Pamenepo ophunzira ake adadzamufunsa kuti, “Kodi mukudziŵa kuti Afarisi aja akhumudwa atamva zija mwanenazi?”
13
Yesu adati, “Chomera chilichonse chimene sichidabzalidwe ndi Atate anga akumwamba, chidzazulidwa.
14
Alekeni, ndi atsogoleri akhungu ameneŵa. Tsono ngati wakhungu atsogolera wakhungu mnzake, onse aŵiri adzagwa m'dzenje.”
15
Apo Petro adampempha kuti, “Timasulirenitu fanizoli.”
16
Yesu adati, “Kani ngakhale inunso simumvetsa?
17
Kodi inu simuzindikira kuti zonse zoloŵa m'kamwa mwa munthu zimaloŵa m'mimba mwake, pambuyo pake nkukatayidwa kuthengo?
18
Koma zotuluka m'kamwa mwa munthu zimachokera mu mtima, ndipo zimenezi ndizo zimamuipitsa.
19
Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za kuphana, za chigololo, za chiwerewere, za kuba, maumboni onama, ndiponso zachipongwe.
20
Zimenezi ndizo zimaipitsa munthu. Koma kudya chakudya osasamba m'manja, sikungaipitse munthu.”
21
Yesu adachoka kumeneko, napita ku madera a ku Tiro ndi Sidoni.
22
Mai wina wachikanani, wa ku madera amenewo, adadza kwa Yesu. Adafuula kuti, “Mundichitire chifundo, Inu Ambuye, Mwana wa Davide. Mwana wanga wamkazi ngwogwidwa koopsa ndi mzimu woipa.”
23
Koma Yesu sadamuyankhe mau ndi amodzi omwe. Ophunzira ake adadza nampempha kuti, “Muuzeni azipita, onani akubwera natisokosera.”
24
Yesu adati, “Inetu Mulungu adandituma kwa amene ali ngati nkhosa zotayika pa mtundu wa Aisraele.”
25
Mai uja adadzamgwadira nati, “Ambuye, ndithu thandizeni.”
26
Yesu adamuuza kuti, “Sibwino kutenga chakudya cha ana nkuponyera agalu.”
27
Maiyo adati, “Nzoonadi, Ambuye, koma suja ngakhale agalu omwe amadyako nyenyeswa zimene zimagwa pansi kuchokera pa tebulo la mbuye ao?”
28
Apo Yesu adati, “Inu mai, chikhulupiriro chanu nchachikulu. Zichitikedi zimene mukufuna.” Pompo mwana wake wamkazi uja adachira.
29
Pambuyo pake Yesu adachoka kumeneko, nayenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya. Kenaka adakwera m'phiri nakakhala pansi kumeneko.
30
Anthu ambirimbiri adadza kwa Iye ndi anthu opunduka miyendo, akhungu, olumala, osalankhula, ndiponso ndi odwala ena ambiri. Adaŵakhazika pafupi ndi Yesu, Iye nkuŵachiritsa.
31
Tsono anthu onse adadabwa poona kuti osalankhula aja akulankhula, olumala aja achira, opunduka miyendo aja akuyenda, ndipo akhungu aja akupenya. Choncho adatamanda Mulungu wa Israele.
32
Yesu adaitana ophunzira ake, naŵauza kuti, “Ndikuŵamvera chifundo anthuŵa, chifukwa akhala nane masiku atatu tsopano, ndipo alibe chakudya. Sindifuna kuŵabweza kwao ali ndi njala chonchi, kuwopa kuti angalefuke pa njira.”
33
Ophunzirawo adamufunsa kuti, “Anthu ochuluka chotereŵa tingaŵapezere kuti chakudya chokwanira, kuthengo ngati kuno?”
34
Yesu adaŵafunsa kuti, “Kaya buledi muli naye mngati?” Iwo aja adati, “Msanu ndi muŵiri, ndiponso tinsomba toŵerengeka.”
35
Apo Yesu adalamula anthu aja kuti akhale pansi.
36
Kenaka adatenga buledi msanu ndi muŵiri uja, ndi nsomba zija, adathokoza Mulungu, nazinyemanyema nkuzipereka kwa ophunzira ake, iwowo nakazigaŵira anthu aja.
37
Anthu onsewo adadya mpaka kukhuta. Adatola zotsala, nkudzaza madengu asanu ndi aŵiri.
38
Koma tsono anthu amene adaadyawo, analipo zikwi zinai amuna okha, osaŵerenga akazi ndi ana.
39
Pambuyo pake Yesu adatsazikana nawo anthu aja, kenaka Iye adaloŵa m'chombo napita ku dera la Magadani.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28