bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 22
Matthew 22
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 23 →
1
Yesu adalankhulanso ndi anthu aja m'mafanizo. Adati,
2
“Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Mfumu ina idaakonzera mwana wake phwando laukwati.
3
Idatuma antchito ake kuti akaŵauze anthu amene adaaitanidwa kuphwandoko kuti azibwera, anthuwo nkukana.
4
Idatumanso antchito ena nkunena kuti, ‘Kaŵauzeni oitanidwa aja kuti chakudya chakonzeka. Ndapha ng'ombe ndi nyama zina zonenepa. Zonse zakonzeka, bwerani ku phwando laukwati.’
5
Koma oitanidwawo sadalabadireko, adangopita ku zao: wina kumunda kwake, wina ku ntchito yake yamalonda.
6
Enawo adagwira antchito a mfumu aja naŵazunza, nkuŵapha.
7
“Pamenepo mfumu idapsa mtima kwambiri, mwakuti idatuma ankhondo ake kuti akaononge opha anzao aja, ndi kutentha mudzi wao.
8
Pambuyo pake idauza antchito ake kuti, ‘Phwando laukwati ndiye lakonzekatu, koma oitanidwa aja anali osayenera.
9
Pitani tsono ku mphambano za miseu, mukaitane aliyense amene mukampeze, kuti abwere kuno ku phwando laukwati.’
10
Apo antchitowo adapitadi ku miseu nakasonkhanitsa onse amene adaŵapeza, abwino ndi oipa omwe, mwakuti nyumba yaphwando idadzaza ndi anthu.
11
“Pamene mfumu ija idaloŵa m'nyumbamo kukaona anthu odzadya phwando aja, idapezamo wina amene sadavale chovala chaukwati.
12
Tsono idamufunsa kuti ‘Kodi iwe, waloŵa bwanji muno opanda chovala chaukwati?’ Iye uja adangoti chete.
13
Apo mfumuyo idauza anyamata ake kuti, ‘Mmangeni manja ndi miyendo, mukamponye kunja ku mdima. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.’ ”
14
Tsono Yesu adati, “Inde oitanidwa ngambiri, komatu osankhidwa ngoŵerengeka.”
15
Nthaŵi ina Afarisi adakapangana zodzatapa Yesu m'kamwa.
16
Adatuma ophunzira ao ena pamodzi ndi ena a m'chipani cha Herode kwa Yesu. Iwoŵa adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti Inu mumanena zoona, mumaphunzitsa malamulo a Mulungu moona, ndipo simuwopa munthu aliyense. Paja Inu simuyang'anira kuti uyu ndani.
17
Ndiye timati mutiwuze zimene mukuganiza. Kodi Malamulo a Mulungu amatilola kuti tizikhoma msonkho kwa Mfumu ya ku Roma, kapena ai?”
18
Koma Yesu podziŵa maganizo ao oipa, adati, “Bwanji kodi mukundiyesa dala, anthu achiphamasonu?
19
Tandiwonetsani ndalama yamsonkho.” Iwo adampatsadi ndalamayo.
20
Pamenepo Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi nkhopeyi ndi ya yani, ndipo dzinali ndi la yani?”
21
Iwo aja adati, “Zonse ndi za Mfumu ya ku Roma.” Apo Yesu adaŵauza kuti, “Tsono perekani kwa Mfumu zake za Mfumuyo, ndiponso kwa Mulungu zake za Mulungu.”
22
Atamva zimenezi, anthuwo adathedwa nzeru, motero adamsiya nachokapo.
23
Tsiku lomwelo Asaduki ena adadza kwa Yesu. (Paja iwo amati akufa sadzauka.) Adamufunsa kuti,
24
“Aphunzitsi, Mose adati, ‘Ngati munthu amwalira opanda ana, mbale wake wa womwalirayo aloŵe chokolo, kuti amuberekere ana mbale wake uja.’
25
Tsono kwathu kudaali anthu asanu ndi aŵiri pachibale pao. Woyamba adaakwatira mkazi, nkumwalira. Tsono popeza kuti analibe mwana, adasiyira mbale wake mkazi wake uja.
26
Chimodzimodzinso wachiŵiri ndi wachitatu, mpaka wachisanu ndi chiŵiri.
27
Potsiriza pake mai uja nayenso adamwalira.
28
Nanga tsono pa tsiku lodzauka akufa, mwini mkaziyo adzakhala utiwuti pakati pa abale asanu ndi aŵiri aja, popeza kuti onsewo adaamkwatirapo?”
29
Yesu adaŵayankha kuti, “Mukulakwa chifukwa simudziŵa Malembo, ngakhalenso mphamvu za Mulungu.
30
Pajatu pouka akufa, palibenso za kukwatira kapena kukwatiwa ai. Onse ali ngati angelo Kumwamba.
31
Tsono zakuti anthu adzauka kwa akufa, kodi simudaŵerenge zimene Mulungu adakuuzani zija kuti,
32
‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, ndine Mulungu wa Isaki, ndine Mulungu wa Yakobe?’ Ndiye kutitu sali Mulungu wa anthu akufa ai, koma wa anthu amoyo.”
33
Pamene anthu ochuluka aja amene anali pamenepo adamva zimenezi, adadabwa kwambiri ndi zophunzitsa zake.
34
Afarisi atamva kuti Yesu adatsutsa Asaduki, adasonkhana.
35
Tsono mmodzi mwa iwo, katswiri wa Malamulo, adafunsa Yesu funso kuti amutape m'kamwa.
36
Adati, “Aphunzitsi, kodi mwa malamulo onse a Mulungu, lalikulu ndi liti?”
37
Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.
38
Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu.
39
Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.
40
Malamulo onse a Mose ndiponso zonse zimene aneneri adaphunzitsa zagona pa malamulo aŵiriŵa.”
41
Afarisi atasonkhana pamodzi, Yesu adaŵafunsa funso.
42
Adati, “Mumaganiza chiyani za Mpulumutsi wolonjezedwa uja? Mumati ndi mwana wa yani?” Iwo aja adati, “Ndi mwana wa Davide.”
43
Iye adaŵafunsa kuti, “Tsono bwanji nanga Davideyo ndi nzeru zochokera kwa Mzimu Woyera, akutchula Mpulumutsi wolonjezedwa uja kuti Mbuye wake? Paja adati,
44
“ ‘Chauta adauza Mbuye wanga kuti, Khala ku dzanja langa lamanja, mpaka nditasandutsa adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.’
45
“Ngati Davide akutchula Mpulumutsi wolonjezedwa uja kuti Mbuye wake, angakhale mwana wakenso bwanji?”
46
Panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kumuyankha ngakhale mau amodzi. Tsono kuyambira tsiku limenelo panalibenso munthu amene adalimba mtima kuti amufunse mafunso.
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28