bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 2
Matthew 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 3 →
1
Yesu adabadwira m'mudzi wa Betelehemu, m'dziko la Yudeya, pa nthaŵi imene Herode anali mfumu ya dzikolo. Ndiye kudaabwera akatswiri ena a nyenyezi ku Yerusalemu kuchokera kuvuma.
2
Iwowo ankafunsa kuti, “Ali kuti mwana amene adabadwa kuti adzakhale Mfumu ya Ayuda? Ife tidaona nyenyezi yake ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza.”
3
Mfumu Herode atamva zimenezi, adavutika kwambiri ndipo anthu ena onse a m'Yerusalemu nawonso adavutika nazo.
4
Tsono Herodeyo adasonkhanitsa akulu onse a ansembe ndi aphunzitsi onse a Malamulo a Mose, naŵafunsa kuti, “Kodi paja adati Mpulumutsi wolonjezedwa ndi Mulungu uja adzabadwira kuti?”
5
Iwo adati, “M'mudzi wa Betelehemu ku Yudeya. Pajatu mneneri adalemba kuti,
6
“ ‘Iwe Betelehemu wa m'dziko la Yuda, sindiwe wamng'ono konse pakati pa akulu olamulira Yuda. Pakuti kwa iwe kudzachokera mtsogoleri pamene adzalamulira anthu anga Aisraele.’ ”
7
Pamenepo Herode adaŵaitanira paseri akatswiri a nyenyezi aja, naŵafunsitsa za nthaŵi yeniyeni imene adaaiwonera nyenyeziyo.
8
Kenaka adaŵatumiza ku Betelehemu nkuŵauza kuti, “Pitani, kafunsitseni za mwanayo. Mukakampeza, mudzandidziŵitse, kuti inenso ndidzapite kukampembedza.”
9
Anthu aja atamva mau a mfumu, adanyamuka. Nyenyezi imene adaaiwona kuvuma ija idaŵatsogolera mpaka idakafika nkukaima pamwamba pa malo amene panali mwanayo.
10
Ataiwona nyenyeziyo, adasangalala kwabasi.
11
Adaloŵa m'nyumba, naona mwanayo ali ndi Maria mai wake, ndipo adagwada nampembedza. Kenaka adamasula chuma chao, nampatsa mitulo ya golide, lubani ndi mafuta onunkhira a mure.
12
Mulungu adaŵachenjeza m'maloto kuti asadzerekonso kwa Herode kuja. Motero adadzera njira ina pobwerera kwao.
13
Atapita akatswiri a nyenyezi aja, mngelo wa Ambuye adaonekera Yosefe m'maloto. Adamuuza kuti, “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mai wake, uthaŵire ku Ejipito. Ukakhale kumeneko mpaka ndidzakuuze, popeza kuti Herode azidzafunafuna mwanayu kuti amuphe.”
14
Apo Yosefe adadzuka usiku womwewo, nkutenga mwanayo ndi mai wake kupita ku Ejipito.
15
Adakhala kumeneko mpaka Herode atamwalira, kuti zipherezere zimene Ambuye adaalankhulitsa mneneri kuti, “Ndidaitana Mwana wanga kuti atuluke ku Ejipito.”
16
Herode atazindikira kuti akatswiri a nyenyezi aja adampusitsa, adatuma anthu ku Betelehemu ndi ku midzi yonse yozungulira, kuti akaphe ana aamuna onse a zaka ziŵiri kapena kucheperapo. Zaka zimenezi adaaŵerengera potsata m'mene adaamvera kwa akatswiri aja za nthaŵi imene iwowo adaaiwonera nyenyeziyo.
17
Pamenepo zidachitikadi zimene mneneri Yeremiya adaanena kuti,
18
“Mau akumveka ku Rama, kulira ndi kubuma kwambiri: Rakele akulira ana ake. Akukana kumtonthoza, chifukwa ana ake asoŵa.”
19
Herode atamwalira, mngelo wa Ambuye adaonekera Yosefe m'maloto ku Ejipito.
20
Adamuuza kuti, “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mai wake, ubwerere ku Israele. Aja ankafuna kumupha mwanayu adafa.”
21
Apo Yosefe adanyamuka, nkutenga mwana uja ndi mai wake, kubwerera ku Israele.
22
Koma atamva kuti Arkelao ndiye mfumu ya ku Yudeya m'malo mwa bambo wake Herode, adaopa kupita kumeneko. Tsono atalandira chenjezo kwa Mulungu m'maloto, adapita ku dera la Galileya.
23
Kumeneko adakakhala ku mudzi wina dzina lake Nazarete, kuti zipherezere zimene aneneri adaanena kuti, “Adzatchedwa Mnazarete.”
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28