bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 20
Matthew 20
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 21 →
1
“Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Munthu wina adaalaŵirira m'mamaŵa kukalemba anthu okagwira ntchito m'munda wake wamphesa.
2
Adaapangana nawo kuti adzaŵalipira ndalama imodzi yasiliva pa tsiku, naŵatuma kumunda kwake.
3
Pa nthaŵi ya 9 koloko adapitanso, nakapeza ena atangokhala khale pa msika, osagwira ntchito.
4
Adaŵauza kuti, ‘Inunso pitani ku munda wanga wamphesa, ndidzakulipirani moyenerera.’
5
Iwowo adapitadi. Munthu uja adapitanso pa 12 koloko masana ndi pa 3 koloko, nakachita chimodzimodzi.
6
Pafupi 5 koloko madzulo adapitanso nakapeza enanso akungokhala. Adaŵafunsa kuti, ‘Bwanji mwangokhala khale pano tsiku lonse osagwira ntchito?’
7
Iwowo adayankha kuti, ‘Chifukwa palibe amene watilemba.’ Iye uja adaŵauza kuti, ‘Inunso pitani ku munda wanga wamphesa.’
8
“Dzuŵa likuloŵa, mwinimunda uja adauza kapitao wake kuti, ‘Kaŵaitane antchito aja, uŵalipire. Uyambire amene alembedwa potsirizawo, utsirizire oyamba aja.’
9
Pamene adabwera olembedwa pa 5 koloko yamadzulo aja, aliyense adalandira ndalama imodzi.
10
Tsono pamene olembedwa poyamba aja adabwera, ankaganiza kuti alandira pakulu. Koma nawonso adangolandira aliyense ndalama imodzi.
11
Ndiye iwowo polandira, adayamba kuŵiringula,
12
adati, ‘Aa! Anzathu otsiriziraŵa angogwira ntchito kanthaŵi pang'ono, bwanji mwaŵapatsa malipiro olingana ndi athu, pamene ifeyo tathyoka nayo ntchito tsiku lathunthu, ndi chidzuŵa chonse chija?’
13
Koma mwinimunda uja adayankha mmodzi mwa iwo kuti, ‘Iwe, inetu sindidakubere ai. Kodi suja tinapangana ndalama yasiliva imodzi?
14
Tenga malipiro ako, uzipita. Mwiniwakene ndafuna kuti ndipatse wolembedwa potsirizayu molingana ndi iwe.
15
Kodi zinthu zanga ndisachite nazo monga ndifunira? Kapenatu ukuipidwa nawo ufulu wanga eti?’ ”
16
Tsono Yesu adati, “Choncho amene ali oyambirira adzakhala otsirizira. Ndipo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira.”
17
Pamene Yesu ankapita ku Yerusalemu, adaŵatengera pambali ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja. Pa njira adaŵauza kuti,
18
“Tilitu pa ulendo wopita ku Yerusalemu. Kumeneko Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Iwo akamuweruza ndi kugamula kuti aphedwe,
19
ndipo akampereka kwa anthu akunja. Amenewo akamchita chipongwe, akamkwapula, nkumupachika pa mtanda; koma mkucha wake Iye adzauka kwa akufa.”
20
Pambuyo pake mkazi wa Zebedeo adadza ndi ana ake kwa Yesu, namgwadira kuti ampemphe kanthu.
21
Yesu adamufunsa kuti, “Amai, kodi muli ndi mau?” Iye adayankha kuti, “Ndimati mulonjeze kuti mu Ufumu wanu ana anga aŵiriŵa adzakhale wina ku dzanja lanu lamanja, wina ku dzanja lanu lamanzere.”
22
Koma Yesu adayankha kuti, “Simukudziŵa zimene mukupempha. Kodi inu mungathe kumwa nao chikho chamasautso chimene ndikudzamwera Ine?” Iwo aja adayankha kuti, “Inde, tingathe.”
23
Apo Yesu adati, “Chabwino, mudzamwa nao chikho changacho. Koma Ineyo si udindo wanga kusankha munthu kuti akhale ku dzanja langa lamanja, kapena ku dzanja langa lamanzere. Atate ndiwo adzapereke malo ameneŵa kwa amene Atatewo adaŵakonzera.”
24
Pamene khumi ena aja adamva zimenezi, adapsera mtima abale aŵiri aja.
25
Koma Yesu adaŵaitana ophunzira akewo naŵauza kuti, “Mukudziŵa kuti olamulira amadyera anthu ao masuku pa mutu. Akuluakulu aonso amaonetsadi mphamvu zao pa anthu ao.
26
Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, akhale mtumiki wanu.
27
Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, akhale kapolo wanu.
28
Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”
29
Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankatuluka mu mzinda wa Yeriko, anthu ambirimbiri ankamutsatira.
30
Panali anthu aŵiri akhungu amene adaakhala pansi pamphepete pa mseu. Iwo aja atamva kuti Yesu akupita mumseumo, adayamba kufuula kuti, “Inu Ambuye, Mwana wa Davide, mutichitire chifundo.”
31
Anthu aja adaŵazazira akhunguwo kuti akhale chete. Koma iwo nkumafuulirafuulira kuti, “Inu Ambuye, Mwana wa Davide, mutichitire chifundo.”
32
Yesu adaima, naŵaitana, nkuŵafunsa kuti, “Kodi mukufuna kuti ndikuchitireni chiyani?”
33
Iwo aja adati, “Ambuye, tikufuna kuti tizipenya.”
34
Yesu adaŵamvera chifundo nakhudza maso ao. Pompo iwo adayamba kupenya, kenaka nkumamutsata.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
Recommended Reading
Commentary
Matthew Commentaries
→
Devotional
Matthew Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→