bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 26
Matthew 26
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 27 →
1
Yesu atatsiriza kulankhula nkhani zonsezi, adauza ophunzira ake kuti,
2
“Pajatu chikondwerero cha Paska chiyambika patangopita masiku aŵiri, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kuti akapachikidwe pa mtanda.”
3
Nthaŵi imeneyo akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda adasonkhana m'nyumba ya mkulu wa ansembe onse, dzina lake Kayafa.
4
Ankakambirana za njira yoti agwirire Yesu mochenjera, nkumupha.
5
Koma ankati, “Zimenezi tisadzachite pa nthaŵi ya chikondwerero ai, pangadzachitike chipolowe pakati pa anthu.”
6
Tsiku lina Yesu anali ku Betaniya, m'nyumba ya Simoni wotchedwa Wakhate.
7
Pamene ankadya, kudafika mai wina atatenga nsupa yagalasi ya mafuta onunkhira amtengowapatali. Adayamba kuthira mafutawo pamutu pa Yesu.
8
Koma pamene ophunzira ake adaona zimenezi, adaipidwa nazo nkumauzana kuti, “Chifukwa chiyani kusakaza zinthu chotere?
9
Ndithu mafuta ameneŵa akadatha kuŵagulitsa pa mtengo waukulu zedi, kenaka ndalama zake nkukapatsa anthu osauka.”
10
Yesu podziŵa zimene iwo aja ankalankhula, adaŵafunsa kuti, “Mukumuvutiranji maiyu? Zimenetu wandichitira iyeyuzi nzabwino kwambiri.
11
Anthu osauka muli nawo nthaŵi zonse, koma Ine simudzakhala nane nthaŵi zonse.
12
Iyeyu wathira mafuta ameneŵa pa thupi langa kuti alidzozeretu lisanaikidwe m'manda.
13
Ndithu ndikunenetsa kuti kulikonse kumene anthu azikalalika Uthenga Wabwinowu pa dziko lonse lapansi, azikafotokozanso zimene maiyu wachita, kuti anthu azidzamkumbukira.”
14
Pambuyo pake Yudasi Iskariote, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja, adapita kwa akulu a ansembe.
15
Adakaŵafunsa kuti, “Kodi mudzandipatsa chiyani ndikadzampereka Yesuyu kwa inu?” Iwo adamupatsa ndalama zasiliva makumi atatu.
16
Tsono kuyambira pomwepo iye adayamba kufunafuna mpata womuperekera kwa iwo.
17
Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, ophunzira aja adadza nafunsa Yesu kuti, “Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Paska?”
18
Iye adaŵauza kuti, “Pitani m'mudzimu kwa munthu wina wake. Mukanene kuti, ‘Aphunzitsi akuti nthaŵi yao ili pafupi, akudzadyera kwanu kuno phwando la Paska pamodzi ndi ophunzira ao.’ ”
19
Ophunzira aja adapita nakachita zomwe Yesu adaaŵauza, nakakonzadi za phwando la Paska.
20
Kutada, Yesu ndi ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja adakhala pamodzi nkumadya.
21
Iwowo alikudya, Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti wina mwa inu andipereka kwa adani anga.”
22
Ophunzirawo adamva chisoni kwambiri, nayamba mmodzimmodzi kumufunsa kuti, “Monga nkukhala ine, Ambuye?”
23
Yesu adaŵayankha kuti, “Yemwe wasunsa mkate m'mbalemu pamodzi ndi Ine, ameneyo ndiye andipereke.
24
Mwana wa Munthu akukaphedwadi, monga momwe Malembo akunenera za Iye. Komabe ali ndi tsoka munthu amene akukapereka Mwana wa Munthuyo. Kukadakhala bwino koposa kwa munthu ameneyo, akadapanda kubadwa.”
25
Yudasi, amene pambuyo pake adapereka Yesu, adafunsa kuti, “Monga nkukhala ine, Aphunzitsi?” Yesu adamuyankha kuti, “Wanena wekha.”
26
Iwo alikudya choncho, Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagaŵira ophunzira aja, ndipo adati, “Kwayani, idyani, ili ndi thupi langa.”
27
Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu nkuchipereka kwa ophunzirawo. Adaŵauza kuti, “Imwani nonsenu.
28
Pakuti aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.
29
Kunena zoona, kuyambira tsopano sindidzamwanso chakumwa cha mtengo wamphesachi, mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano pamodzi nanu mu Ufumu wa Atate anga.”
30
Tsono ataimba nyimbo yotamanda Mulungu, onse adatuluka nkumapita ku Phiri la Olivi.
31
Pambuyo pake Yesu adaŵauza kuti, “Nonsenu mukhumudwa nane nkundisiya usiku uno. Paja Malembo akuti, ‘Ndidzapha mbusa, ndipo nkhosa za msambiwo zidzangoti balala.’
32
Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola ndine kupita ku Galileya.”
33
Petro adati, “Ngakhale onse akhumudwe nkukusiyani, ine ndekha ai.”
34
Yesu adamuuza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti usiku womwe uno, tambala asanalire, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziŵa.”
35
Koma Petro adamuuza kuti, “Ngakhale atati andiphere nanu kumodzi, ine sindingakukaneni konse kuti sindikudziŵani.” Ophunzira ena onse aja nawonso adanena chimodzimodzi.
36
Yesu adapita ndi ophunzira ake aja ku malo ena otchedwa Getsemani. Tsono adauza ophunzirawo kuti, “Inu bakhalani pano, Ine ndikupita uko kukapemphera.”
37
Adatengako Petro ndi ana aŵiri aja a Zebedeo. Yesu adayamba kugwidwa ndi chisoni ndi kuvutika mu mtima.
38
Adaŵauza kuti, “Mumtima mwanga muli chisoni chachikulu chofa nacho. Inu khalani pompano, komatu mukhale maso pamodzi nane.”
39
Adapita patsogolo pang'ono, nadzigwetsa choŵeramitsa nkhope pansi nkuyamba kupemphera. Adati, “Atate, ngati nkotheka, chindichokere chikho chamasautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”
40
Atatero adabwerera kwa ophunzira aja, naŵapeza ali m'tulo. Tsono adafunsa Petro kuti, “Mongadi nonsenu mwalephera kukhala maso pamodzi nane ngakhale pa kanthaŵi kochepa?
41
Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.”
42
Adachokanso kachiŵiri nakapemphera kuti, “Atate, ngati chikho chamasautsochi sichingandichoke, mpaka nditamwa ndithu, chabwino, zimene mukufuna zichitike.”
43
Pamene adabwerakonso, adaŵapeza ali m'tulo, chifukwa zikope zao zinkalemera.
44
Yesu adaŵasiyanso, napita kukapemphera kachitatu, akunena mau amodzimodzi omwe aja.
45
Pambuyo pake adabwera kwa ophunzira ake nati, “Kodi monga mukugonabe ndi kupumula? Ndipotu nthaŵi ija yafika, Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa anthu ochimwa.
46
Dzukani, tiyeni tizipita. Suuyu wodzandipereka uja, wafika.”
47
Yesu akulankhula choncho, wafika Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Adaabwera ndi khamu la anthu atatenga malupanga ndi zibonga. Anthuwo adaaŵatuma ndi akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda.
48
Wodzampereka uja anali ataŵauza chizindikiro kuti, “Yemwe ndikamumpsompsoneyo, ndi ameneyo, mukamugwire.”
49
Tsono Yudasi adadzangofikira pa Yesu, nkunena kuti, “Moni Aphunzitsi!” Atatero adamumpsompsona.
50
Yesu adamuuza kuti, “Bwenzi langa, chita zimene wadzera.” Apo anthu aja adabwera namugwira Yesu.
51
Koma wina mwa amene anali limodzi ndi Yesu, adasolola lupanga lake, natema wantchito wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu.
52
Apo Yesu adamuuza kuti, “Bwezera lupangalo m'chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzaphedwa ndi lupanga.
53
Kodi ukuyesa kuti Ine sindingapemphe Atate, Iwo nthaŵi yomweyo nkunditumizira magulu ankhondo a angelo oposa khumi ndi aŵiri?
54
Koma ndikadatero, nanga zikadachitika bwanji zimene Malembo adaneneratu kuti ziyenera kuchitika?”
55
Pamenepo Yesu adaŵafunsa anthu aja kuti, “Bwanji mwachita kudzandigwira muli ndi malupanga ndi zibonga, ngati kuti ndine chigaŵenga? Tsiku ndi tsiku ndinkakhala pansi m'Nyumba ya Mulungu ndikuphunzitsa, inuyo osandigwira.
56
Koma zonsezi zachitika kuti ziwonekedi zimene aneneri adalemba.” Pamenepo ophunzira ake onse aja adathaŵa, kumusiya yekha.
57
Tsono anthu amene adagwira Yesu aja adapita naye kunyumba kwa Kayafa, mkulu wa ansembe onse. Kumeneko kudaasonkhana aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda.
58
Koma Petro ankamutsatira chapatali, mpaka ku bwalo la nyumba ya mkulu wa ansembe uja. Adaloŵa m'kati, nakhala pansi pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu kuti aone m'mene zithere.
59
Akulu a ansembe aja ndi onse a m'Bwalo Lalikulu la Ayuda ankafunafuna umboni wonama woneneza Yesu kuti amuphe.
60
Koma sadaupeze ngakhale padaabwera mboni zambiri zabodza. Potsiriza padabwera anthu aŵiri.
61
Adati, “Munthu uyu ankati, ‘Ine ndingathe kupasula Nyumba ya Mulungu nkuimanganso pa masiku atatu.’ ”
62
Tsono mkulu wa ansembe onse adaimirira nafunsa Yesu kuti, “Kodi ulibe poyankha? Nzotani zimene anthuŵa akukunenezazi?”
63
Koma Yesu adangokhala chete. Pamenepo mkulu wa ansembe uja adauza Yesu kuti, “Ndikukulamula m'dzina la Mulungu wamoyo kuti utiwuze molumbira ngati ndiwedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu.”
64
Yesu adamuyankha kuti, “Mwanena nokha. Komanso ndikukuuzani kuti kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa Munthu atakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvuzonse. Mudzamuwona akubwera pa mitambo.”
65
Apo mkulu wa ansembe uja adang'amba zovala zake nati, “Kunyoza Mulungu koopsatu kumeneku! Kodi pamenepa nkufunanso mboni zina ngati? Mwadzimvera nokha kunyoza Mulungu koopsaku.
66
Ndiye inu mukuganiza bwanji?” Iwo aja adayankha kuti, “Ayenera kuphedwa.”
67
Pomwepo iwo adayamba kumthira malovu kumaso nkumamumenya, ena kumamuwomba makofi,
68
nkumanena kuti, “Iwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, nanga sindiwe mneneri? Lota, wakumenya ndani?”
69
Petro adaakhala kunja m'bwalo la nyumba ija. Mtsikana wina wantchito adabwera namuuza kuti, “Inunsotu munali ndi Yesu wa ku Nazareteyu.”
70
Koma iye adakana pamaso pa anthu onse, adati, “Sindikuzidziŵa zimenezo ine.”
71
Pamene Petro ankatuluka kumapita ku chipata, mtsikana winanso wantchito adamuwona, nayamba kuuza amene anali pamenepo kuti, “Akulu ameneŵa anali ndi Yesu wa ku Nazareteyu.”
72
Petro adakananso molumbira kuti, “Ndithudi sindikumdziŵa munthu ameneyo.”
73
Ndipo patangopita kanthaŵi, anthu amene anali pamenepo adadza nauza Petro kuti, “Ndithu nawenso ndiwe wa gulu lomweli, tadziŵira kalankhulidwe kakoka.”
74
Apo Petro adayamba kulumbira nkumanena kuti, “Mulungu andilange, munthu mukunenayu ine sindimdziŵa konse.” Nthaŵi yomweyo tambala adalira.
75
Tsono Petro adakumbukira mau aja a Yesu akuti, “Tambala asanalire, ukhala utakana katatu kuti sundidziŵa.” Pomwepo adatuluka, nakalira misozi ndi chisoni chachikulu.
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 27 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28