bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 4
Matthew 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 5 →
1
Zitatha izi, Mzimu Woyera adatsogolera Yesu kupita ku chipululu kuti Satana akamuyese.
2
Pa masiku makumi anai Yesu adasala zakudya usana ndi usiku, ndipo pambuyo pake adamva njala.
3
Tsono Woyesa uja adadza namuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, lamulani miyala ili apayi kuti isanduke chakudya.”
4
Koma Yesu adati, “Malembo akuti, “ ‘Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mau onse olankhula Mulungu.’ ”
5
Pambuyo pake Satana adatenga Yesu kupita naye ku Yerusalemu, Mzinda Wopatulika, nakamuimika pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu.
6
Adamuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, mudziponye pansi. Paja Malembo akuti, “ ‘Mulungu adzalamula angelo ake kuti akusamaleni, iwo adzakunyamulani m'manja mwao, kuti mapazi anu angapweteke pa miyala.’ ”
7
Koma Yesu adati, “Malembo akutinso, ‘Usaŵayese Ambuye, Mulungu wako.’ ”
8
Potsiriza Satana adatenga Yesu kupita naye pa phiri lalitali kwambiri, ndipo adamuwonetsa maufumu onse a pansi pano ndi ulemerero wake.
9
Tsono adamuuza kuti, “Zonsezi ndidzakupatsani mukagwada pansi ndi kundipembedza.”
10
Apo Yesu adati, “Choka, Satana! Paja Malembo akuti, ‘Uzipembedza Ambuye, Mulungu wako, ndipo uziŵatumikira Iwo okha.’ ”
11
Pamenepo Satana adamsiya, angelo nkubwera kumadzamutumikira Yesuyo.
12
Yesu atamva kuti Yohane adamponya m'ndende, adabwerera ku Galileya.
13
Adachokako ku Nazarete, nakakhala ku Kapernao, mzinda wina wa m'mbali mwa nyanja ku dera la Zebuloni ndi Nafutali.
14
Zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri Yesaya adaanena kuti,
15
“Iwe dziko la Zebuloni ndi iwe dziko la Nafutali, ku njira yakunyanja, patsidya pa Yordani, iwe Galileya, dziko la anthu akunja!
16
Anthu okhala mu mdima aona kuŵala kwakukulu. Anthu okhala m'dziko la mdima wabii wa imfa, kuŵala kwaŵaonekera.”
17
Kuyambira nthaŵi imeneyo Yesu adayamba kulalika kuti, “Tembenukani mtima, chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira.”
18
Yesu akuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, adaona anthu aŵiri pachibale pao: Simoni wotchedwa Petro, ndi mbale wake Andrea, akuponya khoka m'nyanjamo, popeza kuti anali asodzi.
19
Yesu adaŵauza kuti, “Inu, munditsate, ndikakusandutseni asodzi a anthu.”
20
Pomwepo iwo adasiya makoka ao, namamtsatadi.
21
Atapitirira pamenepo, Yesu adaona enanso aŵiri pachibale pao: Yakobe ndi Yohane, ana a Zebedeo. Iwo anali m'chombo pamodzi ndi bambo waoyo, akukonza makoka ao, Yesu nkuŵaitana.
22
Pomwepo iwowo adasiya chombo chao ndi bambo wao uja, namatsata Yesu.
23
Yesu adayendera dziko lonse la Galileya akuphunzitsa m'nyumba zamapemphero ndi kulalika Uthenga Wabwino wonena za ufumu wakumwamba. Ankachiritsanso nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi.
24
Mbiri yake idabuka m'dziko lonse la Siriya, kotero kuti anthu ankabwera kwa Iye ndi odwala onse ovutika ndi nthenda ndi zoŵaŵa zosiyanasiyana, ogwidwa ndi mizimu yoipa, akhunyu ndi opunduka, Iye nkumaŵachiritsa.
25
Anthu ambirimbiri ankamutsata kuchokera ku Galileya, ku dera lotchedwa Mizinda Khumi, ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi kutsidya kwa mtsinje wa Yordani.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28